Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patali? Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife; pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuimba anu ati, Pakuti ifenso tili mbadwa zake.
Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja. Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika. Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo. Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu. Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Yehova apenyerera m'mwamba; aona ana onse a anthu. M'malo akhalamo Iye, amapenya pansi pa onse akukhala m'dziko lapansi.
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Potero dziwani lero lino nimukumbukire m'mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m'thambo la kumwamba ndi padziko lapansi; palibe wina.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, ulemerero wake pamwambamwamba. Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali, nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za padziko lapansi.
Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika.
Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.
Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.
Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?
Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.
Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.
Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena, Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga. Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.
Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova. Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.
Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?
Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.
Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;
Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.
Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake. Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake.
Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.
ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.
Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.
Pakuti maso anga ali panjira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga.
tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa mufunafuna? Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika? Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungachitenji? Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji? Muyeso wake utalikira utali wake wa dziko lapansi, chitando chake chiposa cha nyanja.
Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.
Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso. Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.
Ine ndili Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'chuuno, ngakhale sunandidziwe; kuti anthu akadziwe kuchokera kumatulukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.
Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? Ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira chofukiza ndiko?
Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu.
Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa. Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.
Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.
Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.
Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.
Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.
Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera. Taonani, wakusunga Israele sadzaodzera kapena kugona.
Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lake; chuma cha m'mapiri chomwe ndi chake. Nyanja ndi yake, anailenga; ndipo manja ake anaumba dziko louma.
Taona ndakulembera iwe pa zikhato za manja anga; makoma ako alipo masiku onse pamaso panga.
Ndipo pali machitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse.
Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.
Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.
ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,
kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.
Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu; komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.
Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.
Usaope; pakuti Ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kuchokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo.
Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga. Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha. Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu. Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa? Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao. Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israele, Mfumu yanu. Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu; amene atulutsa galeta ndi kavalo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi. Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale. Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala. Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye. Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova? Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?
Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.
Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.
kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.
Mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi choonadi, kwa iwo akusunga pangano lake ndi mboni zake.
Ndipo ndidzapatsa iwo mtima wakundidziwa, kuti ndine Yehova, nadzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao; pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao.
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.
Ine ndiye Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine, monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.
pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime paphiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho. Chitaleka chivomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo. Utaleka moto panali bata la kamphepo kayaziyazi.
Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.
Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.
Yehova ndiye wakukusunga; Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja. Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku.
Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo. Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa.
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!
Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu. Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;
Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu. Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake. Ndipo Elikana ananka kwao ku Rama, mwanayo natumikira Yehova pamaso pa Eli wansembeyo. Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova. Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m'dzanja lake; nachipisa m'chimphuli, kapena mumkhate, kapena m'nkhali, kapena mumphika; yonse imene chovuuliracho chinaitulutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yake. Ankatero ku Silo ndi Aisraele onse akufika kumeneko. Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaotche; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi. Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda. Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikulu ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova. Koma Samuele anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'chuuno ndi efodi wabafuta. Ndiponso amake akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye chaka ndi chaka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wake kudzapereka nsembe ya pachaka. Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao; Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja. nulowa pakati pa ulendo wa Aejipito ndi ulendo wa Aisraele; ndipo mtambo unachita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizane ndi unzake usiku wonse.
Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka.
Ndipo anamuumiriza Iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo analowa kukhala nao. Ndipo m'mene analowa sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. Ndipo kunali m'mene Iye anaseama nao pachakudya, anatenga mkate, naudalitsa, naunyema, napatsa iwo. Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira Iye; ndipo anawakanganukira Iye, nawachokera.
Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife mu ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo. Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.
Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;
Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala. Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri! Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wake? Kotero ngati simungathe ngakhale chaching'onong'ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija?
Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, palibe Mulungu winanso koma Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.
Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,
Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.
Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.
Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?
Pakuti Ine ndidziwa ntchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.
Kodi unalowa magwero a nyanja? Kodi unayendayenda pozama penipeni? Kodi zipata za imfa zinavumbulukira iwe? Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa? Kodi unazindikira chitando cha dziko lapansi? Fotokozera, ngati uchidziwa chonse.
Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;
Koma akadaima mu upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo kunjira yao yoipa, ndi kuchoipa cha ntchito zao.
Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo ndiye Ambuye, mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja; satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;
koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.