Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 2:6 - Buku Lopatulika

6 Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? Ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira chofukiza ndiko?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? Ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira chofukiza ndiko?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Koma ndani angathe kummangira nyumba, poti ku mlengalenga ngakhale kumwambamwamba sikungathe kumkwanira Iye? Kodi ine ndinenso yani kuti ndingammangire nyumba, osati kamalo chabe koti nkumafukizapo lubani pamaso pa Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Koma ndani angathe kumumangira Iye Nyumba, pakuti mlengalenga, ngakhale kumwamba kwenikweni sikungamukwane? Tsono ine ndine yani kuti ndimangire Iyeyo Nyumba, kupatula malo chabe opserezerapo nsembe pamaso pake?

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 2:6
19 Mawu Ofanana  

Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhala pansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi chiyani kuti munandifikitsa pano?


Ndipo mfumu Solomoni anatuma anthu kukatenga Hiramu ku Tiro.


Iyeyo anali mwana wake wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali, atate wake anali munthu wa ku Tiro, mfundi wamkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira ntchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomoni namgwirira ntchito zake zonse.


Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.


Uli naonso antchito ochuluka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akuchita ntchito zilizonse;


Koma ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? Popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.


Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?


Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?


Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele mu Ejipito?


ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kozokota mtengo, kuchita ntchito zilizonse.


Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?


Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.


koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?


Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;


Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.


koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mafuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzichita zonse ndikuuzani.


Zopatulika zanu zokha zimene muli nazo, ndi zowinda zanu, muzitenge, ndi kupita nazo ku malo amene Yehova adzasankha;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa