Eksodo 20:24 - Buku Lopatulika24 Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Mundimangire guwa ladothi, ndipo pamenepo muziperekapo nsembe zanu zopsereza, ndi zopereka zanu zamtendere, nkhosa ndi ng'ombe zanu. Pa malo onse amene ndikuuzani kuti muzindipembedzerapo, Ine ndidzabwera kudzakudalitsani. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Mundimangire guwa ladothi ndipo muziperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zanu. Pamalo paliponse pamene Ine ndidzakonza kuti muzinditamandirapo, ndidzabwera ndi kukudalitsani. Onani mutuwo |
Nadzilimbitsa Rehobowamu mfumu mu Yerusalemu, nachita ufumu; pakuti Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri mu Yerusalemu, ndiwo mzinda Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele, kuikapo dzina lake; ndipo dzina la make ndiye Naama Mwamoni.
Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.