Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 20:23 - Buku Lopatulika

23 Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi Ine; musadzipangire milungu yagolide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi Ine; musadzipangire milungu yagolide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide, kuti muziipembedzera kumodzi ndi Ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 20:23
21 Mawu Ofanana  

Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawachotsako.


Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.


Ndipo Mose anabwerera kunka kwa Yehova, nati, Ha! Pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolide.


Usadzipangire milungu yoyenga.


Ndipo inu, nyumba ya Israele, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ake, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvere Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.


ndi kuika chiundo chao pafupi pa chiundo changa, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazichita; chifukwa chake ndinawatha mu mkwiyo wanga.


koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.


Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolide, ndi yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala.


Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;


Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.


ndipo munapenya zonyansa zao, ndi mafano ao, mtengo ndi mwala, siliva ndi golide, zokhala pakati pao;


Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.


Nabwezera amake ndalama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wake, Kupatula ndapatulira Yehova ndalamazo zichoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo fano losema ndi fano loyenga; m'mwemo ndikubwezera izi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa