Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 20:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo ukandimangira guwa la nsembe lamiyala, usalimanga ndi miyala yosema; ukakwezapo chosemera chako, waliipsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo ukandimangira guwa la nsembe lamiyala, usalimanga ndi miyala yosema; ukakwezapo chosemera chako, waliipsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Mukadzandimangira guwa lamiyala, miyala yake musadzaseme, chifukwa mukadzaisema ndi chitsulo chosemera, mudzaipitsa guwalo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Ngati mudzandimangira guwa lansembe lamiyala, musagwiritse ntchito miyala yosema, pakuti mudzalidetsa mukadzagwiritsa ntchito zida.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 20:25
6 Mawu Ofanana  

Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveke kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena chipangizo chachitsulo, pomangidwa iyo.


Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.


Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Ndipo panali magome anai a nsembe yopsereza a miyala yosema, m'litali mwake mkono ndi nusu, kupingasa kwake mkono ndi nusu, msinkhu wake mkono umodzi; pamenepo ankaika zipangizo zimene anaphera nazo nsembe yopsereza ndi nsembe yophera.


monga Mose mtumiki wa Mulungu adalamulira ana a Israele, monga mulembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, guwa la nsembe la miyala yosasema, yoti palibe munthu anakwezapo chitsulo; ndipo anafukizirapo Yehova nsembe zopsereza, naphera nsembe zoyamika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa