Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 57:3 - Buku Lopatulika

3 Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mulungu adzandiyankha ali kumwamba, ndipo adzandipulumutsa. Iye adzasokoneza amene andipondereza. Adzaonetsa chikondi chake chosasinthika, adzaonetsa kukhulupirika kwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa, kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri. Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 57:3
14 Mawu Ofanana  

Ngati amuna a m'hema mwanga sanati, ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?


Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.


Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.


Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere; zindifikitse kuphiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.


Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu; mumpatse chifundo ndi choonadi zimsunge.


Yehova, mudzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira ntchito zathu zonse.


Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa.


Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.


Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa