Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 57:4 - Buku Lopatulika

4 Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndimagona pakati pa anthu olusa amene ali ngati mikango. Mano ao ali ngati mikondo ndi mivi, lilime lao lili ngati lupanga lakuthwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ine ndili pakati pa mikango, ndagona pakati pa zirombo zolusa; anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi, malilime awo ndi malupanga akuthwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 57:4
20 Mawu Ofanana  

Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pake? Mano ake aopsa pozungulira pao.


Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.


Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango.


Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere; zindifikitse kuphiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.


Lilime lako likupanga zoipa; likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Thyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu, zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.


Onani abwetuka pakamwa pao; m'milomo mwao muli lupanga, pakuti amati, Amva ndani?


Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;


Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.


Wochitira mnzake umboni wonama ndiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa.


Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda, momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.


Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni; kuti adye osauka kuwachotsa kudziko, ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu.


Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.


Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.


koma ngati simunatero, utuluke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ake a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nutuluke moto kwa eni ake a ku Sekemu, ndi kunyumba yake ya Milo, nunyeketse Abimeleki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa