Masalimo 57 - Buku LopatulikaDavide apempha Mulungu amtchinjirize, namlemekezapo Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Altasheti. Mikitamu wa Davide; muja anathawa Saulo, ali m'phanga. 1 Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita. 2 Ndidzafuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba; ndiye Mulungu wonditsirizira zonse. 3 Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake. 4 Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa. 5 Mukwezeke m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba padziko lonse lapansi. 6 Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha. 7 Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza. 8 Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze! Ndidzauka ndekha mamawa. 9 Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye, ndidzakuimbirani mwa mitundu. 10 Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo. 11 Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi