Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 57:6 - Buku Lopatulika

6 Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Iwo aja adatchera mapazi anga ukonde. Mtima wanga umavutika kwambiri. Akumba mbuna m'njira yanga, koma agweramo okha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iwo anatchera mapazi anga ukonde ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa. Anakumba dzenje mʼnjira yanga koma agweramo okha mʼmenemo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 57:6
18 Mawu Ofanana  

Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.


Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.


kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutivomereze.


Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.


Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.


Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga.


Yehova agwiriziza onse akugwa, naongoletsa onse owerama.


Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.


M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.


Wosocheretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa, adzagwa mwini m'dzenje lake; koma angwiro adzalandira cholowa chabwino.


Wosyasyalika mnzake atcherera mapazi ake ukonde.


Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.


koma ndithu, pali Ine, dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi ulemerero wa Yehova;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa