Mukakumana ndi Mulungu weniweni kudzera mwa Ambuye Yesu Khristu, mumayamba kuzindikira choonadi. Yesu anati mu Yohane 14:6, “Ine ndine njira, choonadi, ndi moyo. Palibe amene afikira kwa Atate, koma kudzera mwa Ine.” Choonadi chenicheni chili mwa Mzimu Woyera.
Nthawi zambiri, anthu amaganiza kuti ali ndi choonadi pa zonse zimene amanena, agwiritsitsa maganizo olakwika. Koma Baibulo limatiphunzitsa kuti Mzimu Woyera adzatiwongolera ku choonadi chonse. Mau ake adzatiwongolera ku tsogolo labwino, osati ku zinthu zosakhazikika kapena zakanthawi, koma ku moyo wosatha. Mulungu akufuna kuti mupambane kudzera m’choonadi chake.
Dongosolo la dziko lino lidzayesa kukunyengani ndi kukusokonezani, kukuonetsani njira zooneka ngati zabwino koma kwenikweni ndi njira za imfa. Lidzakulimbikitsani kusiya mfundo ndi malamulo a Mulungu, koma Mulungu lero akukuuzani kuti mudziwe choonadi chake kuti mukhale omasukadi.
Kudziwa maganizo ake pa inu, zimene zalembedwa pa moyo wanu m’mawu ake, kudzakumasulani ku mabodza a mdani. Ngakhale kuti mdani amapereka choonadi chosokoneza chomwe chimakupangitsani kumva kuti ndinu wopanda pake, Khristu Yesu, m’choonadi chake, akukuuzani kuti chifukwa cha nsembe yake ndinu omasuka ndi wolandira cholowa pamodzi ndi iye, kukulolani kukhala mwana wa Mulungu.
Choonadi chenicheni chomwe mukufuna kuti mukhale olimba chili m’zimene Mulungu wanena za inu kuyambira kalekale. Lolani Mzimu Woyera akutsogolereni ku choonadi chonse ndipo mudzaona ulemerero wake pa inu.
Muzichita izi: muzikambirana zoona, muziweruza moona ndi mwamtendere m'mabwalo a milandu.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Tumizani kuŵala kwanu ndi choona chanu kuti zinditsogolere. Zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kokhala Inu.
Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Mwa kufuna kwake mwiniwakeyo, adatipatsa moyo kudzera mwa mau ake oona, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, ife tikhale ngati zipatso zoyamba zimene Iye wadzipatulira.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza.
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu.
Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.
Phunzitseni njira zanu, Inu Chauta, kuti ndiziyenda m'zoona zanu. Mundipatse mtima wosagaŵikana, kuti ndiziwopa dzina lanu.
Paja Mulungu adatipatsa Malamulo ake kudzera mwa Mose, koma kudzera mwa Yesu Khristu adatizindikiritsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake.
Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu,
Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona.
Sindidalankhule mwachinsinsi pa malo ena m'dziko lamdima. Sindidauze zidzukulu za Yakobe kuti zizindifunafuna kumene kuli kopanda kanthu. Ine Chauta ndimalankhula zoona, ndimanena zolungama.”
Mpang'ono pomwe. Koma anthu adziŵe kuti zimene Mulungu amalankhula nzoonadi, ngakhale kuti anthu onse ndi onama. Ndi monga Malembo akunenera kuti, “Inu Mulungu, anthu adziŵe kuti mumanena zoona mukamalankhula, adziŵe kuti mumapambana mukamazenga mlandu.”
Takaniratu njira zonse zochititsa manyazi zimene anthu amatsata mobisika. Sitichita kanthu monyenga kapena kupotoza mau a Mulungu; koma pakulankhula zoona poyera pamaso pa Mulungu, tifuna kuti anthu onse ativomereze m'mitima mwao.
Pajatu pamene pali kuŵala, pamapezekanso ubwino wonse, chilungamo chonse ndi choona chonse.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu.
Mwayeretsa mitima yanu pakumvera choona, kotero kuti muzikondana ndi akhristu anzanu mosanyenga. Nchifukwa chake muzikondana ndi mtima wonse, mosafookera.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro, chimakhala mpaka muyaya. Chiweruzo cha Chauta nchoona, ncholungama nthaŵi zonse.
Ndakulemberani, osati chifukwa chakuti simudziŵa choona, koma chifukwa chakuti mumachidziŵa, ndipo mukudziŵanso kuti bodza silichokera ku choona.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Gwero la zonsezi ndi chiyembekezo chimene muli nacho chodzalandira zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Mudamva za zimenezi pamene mau oona, adakufikani poyamba paja. Mau oonawo ndi Uthenga Wabwino.
Pakuti chikondi chake kwa ife nchachikulu, kukhulupirika kwa Chauta nkwamuyaya. Tamandani Chauta!
Chifukwa cha kudzipereka ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake. Chifukwa choopa Chauta munthu amalewa zoipa.
Timakukondani chifukwa cha choona chimene chimakhala mwa ife, ndipo chidzakhala nafe mpaka muyaya.
Pakamwa panga musapaletse mpang'ono pomwe kulankhula mau anu oona, pakuti ndimakhulupirira malangizo anu.
Koma mbeu zogwera pa nthaka yabwino zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, naŵasunga mu mtima woona ndi wabwino, ndipo amalimbikira mpaka kubereka zipatso.”
Kuweruza kolungama kwalekeka, ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika. Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu, ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko.
Adatuma ophunzira ao ena pamodzi ndi ena a m'chipani cha Herode kwa Yesu. Iwoŵa adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumanena zoona, mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona, ndipo simuwopa munthu aliyense. Paja Inu simuyang'anira kuti uyu ndani.
Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.
Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.
Sitidaŵagonjere mpang'ono pomwe, popeza kuti tinkafuna kukusungirani kwathunthu zoona za Uthenga Wabwino.
Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako.
Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse.
Usachite naye nsanje munthu wachiwawa, usatsanzireko khalidwe lake lililonse.
Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo.
Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa.
Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza, koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima.
Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi.
Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.
Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Tamandani Chauta, inu mitundu yonse ya anthu. Mlemekezeni kwambiri, inu anthu a m'maiko onse.
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse.
Mulungu aŵapatse mtendere, ndipo aŵachitire chifundo anthu a Mulungu onse amene amatsata njira imeneyi.
Pakuti sitingathe kuchita chilichonse chotsutsana ndi choona, koma zokhazokha zothandizira choonacho.
Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo.
Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake.
Anthu anu adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthaŵi yaitali. Adzamanganso pa maziko akalekale. Apo mudzatchedwa anthu okonza makoma, omanganso nyumba zamabwinja, kuti anthu azikhalamo.”
Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu.
Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa.
Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen.
Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma.
Musamauzana mabodza, pakuti mwachita ngati mwavula moyo wanu wakale, pamodzi ndi zochitachita zake zoipa,
Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.
Paja Malembo akuti bwanji? Akuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo pakukhulupirirapo, Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.”
Mundidziŵitse mfundo za malamulo anu, ndipo ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zodabwitsa.
Angathe kutero ndi amene amachita zolungama ndi kulankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga, amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu, amene amatseka makutu kuti angamve mau opangana za kupha anzao, amene amatsinzina kuti angaone zoipa.
Munthu wotere adzakhala pa malo otetezedwa. Kothaŵirako iye kudzakhala ku malinga am'matanthwe. Chakudya azidzalandira, ndipo madzi sadzamsoŵa.
Agalatiya opusa inu, adakulodzani ndani? Pamene tidakulalikirani Yesu Khristu, tidamuwonetsa poyera pamaso panu ngati wopachikidwa pa mtanda.
Tiyeni tsono, tichite chikondwererocho, osati ndi chofufumitsira chakale chija cha uchimo ndi cha kuipa mtima, koma ndi buledi wosafufumitsa, wa kuyera mtima ndi wa choona.
Kwa ife ai, Chauta, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu lokha ndiye kukhale ulemerero. Chifukwa ndinu Mulungu wa chikondi chosasinthika ndi wokhulupirika.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.
Anthu oipa samvetsa kuti chilungamo nchiyani, koma amene amatsata kufuna kwa Chauta amachimvetsa kwathunthu.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Ndalumbira dzina langa lomwe, pakamwa panga palankhula moona mau amene sadzasinthika konse, akuti, ‘Bondo lililonse lidzandigwadira, anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.’
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Tikanena kuti timayanjana naye, pamene tikuyendabe mu mdima, tikunama, ndipo zochita zathu nzosagwirizana ndi zoona.
Tiyamike Mulungu! Inu kale munali akapolo a uchimo, koma tsopano mukumvera ndi mtima wonse zoona za chiphunzitso chimene mudalandira.
Ndipo zonse zimene Mulungu adalonjeza zidachitika ndi “Inde” ameneyu. Nchifukwa chake mwa Yesu Khristuyo timanena kuti, “Amen” kulemekeza Mulungu.
Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.
Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.