Ndikayang'ana chilengedwe cha Mulungu, kukongola kwake konse, ndimadabwa kwambiri ndi ukulu wake ndi dongosolo lake labwino. Kuyambira kale, anthufe timayesetsa kumvetsa dziko ndi cholinga chake m'njira zosiyanasiyana. Koma Baibulo limatipatsa njira yoona zinthu yotithandiza kumvetsa bwino dzikoli.
M'mavesi oyamba a buku la Genesis, timapeza kuti Mulungu ndiye analenga thambo ndi dziko lapansi, ndi zonse zili mmenemo. "Pachiyambi Mulungu analenga thambo ndi dziko lapansi." (Genesis 1:1). Mawu awa, ochepa koma ofunika kwambiri, amatiuza kuti chilengedwe chonse chinachokera kwa Mulungu. Dziko linapangidwa ndi Mlengi Wamkulu.
Baibulo limatilimbikitsa kuona kupitirira zomwe maso athu akuona, ndikuganizira cholinga chenicheni cha chilengedwechi. Mu Salmo 19:1, limati: "Zakumwamba zimalengeza ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo limasonyeza ntchito ya manja ake." Apa tikuona kuti dziko sili mboni chete ya ukulu wa Mulungu, koma limalankhulanso za kukhalapo ndi mphamvu zake kwa ife.
Dziko limatilimbikitsa kuona ukulu wa Mulungu m'chilengedwe chake. Limatithandiza kumvetsa kuti dziko limene tikukhala ndilo umboni wa chikondi, mphamvu, ndi nzeru za Mlengi wathu.
Pokhala ndi chikhulupiriro timamvetsa kuti zonse zimene zilipo zidalengedwa ndi mau a Mulungu, mwakuti zinthu zoonekazi zidachokera ku zinthu zosaoneka.
“Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu, ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu, pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse. Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.”
Adadalitsa Abramuyo, adati, “Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu.
Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pamwamba pa akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira mafumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi.
“Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pamwamba pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi.
Chauta, Mpulumutsi wako, amene adakupanga m'mimba mwa mai wako, akunena kuti, “Ndine Chauta, amene ndidapanga zinthu zonse. Pamene ndinkayalika zakuthambo, ndinali ndekha. Pamene ndinkalenga dziko lapansi, kodi analipo amene adandithandiza?
Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo.
Mulungu adayala thambo lakumpoto pa phompho, adakoloŵeka dziko lapansi m'malo mwake, pamene panali popanda nkanthu komwe.
Koma Ine Chauta ndidachita chipangano ndi usana ndi usiku, ndipo ndidapanga malamulo oyendetsa zonse za pa dziko lapansi ndi zamumlengalenga.
Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa. Zonse zakumeneko zidalengedwa pamene Iye adalankhula mau ake.
Pa nthaŵi imeneyo Yesu adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira, nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira.
Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye.
“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.
Pamenepo Ezara adapemphera kuti, “Inu nokha ndiye Chauta. Inu mudalenga kumwamba, kumwambamwamba, ndiponso zonse zokhala komweko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Mudalenga nyanja ndi zonse zam'menemo. Zonse zakumwamba zimakupembedzani.
Ndine amene ndidalenga dziko lapansi ndi kulenga munthu kuti akhalemo. Ndidayalika zakuthambo ndi manja anga, ndipo tsopano ndimalamulira gulu lonse lamumlengalenga.
Tsono tamvani, Iyeyo ndiye amene amaumba mapiri ndi kupanga mphepo, ndiye amene amaululira munthu za m'maganizo mwake, ndiye amene amasandutsa usana kuti ukhale usiku, ndiye amene amayenda pa zitunda za dziko lapansi. Dzina lake ndi Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse.
Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba.
“Kodi udaali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi? Undiwuze ngati ndiwe womvetsa zinthu. pamene ili khale m'mapanga mwake, kapena pamene ikubisala m'tchire? Kodi khwangwala amampatsa chakudya chake ndani, pamene maunda ake akulirira kwa Mulungu, namadzandira chifukwa chosoŵa chakudya?” Nanga kodi ukudziŵa amene adalemba malire ake, amene adayesapo ndi chingwe padzikopo? Kodi maziko ake adaŵakumba potani? Nanga mwala wake wapangodya adauika ndani? Pa nthaŵiyo nyenyezi zakuvuma zinkaimba pamodzi, ndipo angelo onse a Mulungu ankafuula mokondwa?
Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”
Mulungu, Chauta, adalenga zakuthambo ndi kuziyalika. Adalenga dziko lapansi ndi zonse zimene limabereka. Adapatsa mpweya kwa anthu okhala m'dzikomo, ndi kuninkha moyo kwa onse oyendamo. Iyeyo akunena kuti,
Yang'anani kumlengalenga. Kodi ndani adalenga nyenyezi mukuziwonazi? Ndiye amene amazitsogolera ngati gulu lankhondo, ndipo iliyonse amaiitana ndi dzina lake. Popeza kuti nyonga ndi mphamvu zake nzazikulu. Palibe ndi imodzi yomwe imene imasoŵapo.
Pambuyo pake Mulungu adati, “Kuthambo kukhale miyuni kuti izilekanitsa usana ndi usiku, ndiponso kuti ikhale zizindikiro za nyengo, masiku ndi zaka. Miyuni imeneyi ikhale ku thambo ndi kumaunikira dziko lapansi,” ndipo zidachitikadi. Motero Mulungu adalenga miyuni iŵiri yaikulu: dzuŵa loŵala masana, ndi mwezi woŵala usiku. Adalenganso nyenyezi. Mulungu adaika miyuniyo ku thambo, kuti iziwunikira dziko lapansi, kuti iziŵala usana ndi usiku, kulekanitsa kuyera ndi mdima. Mulungu adaona kuti zinali zabwino.
Adalenga zakumwamba ndi nzeru zake, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adayala dziko lapansi pa madzi, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adalenga miyuni yaikulu yamumlengalenga, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Dzuŵa kuti lizilamulira usana, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira usiku, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Kumwamba ndi zonse zili kumeneko ndi zake za Chauta, pamodzi ndi dziko lapansi pano ndi zonse zili m'menemo.
Zakumwamba zimatamanda zodabwitsa zanu, Inu Chauta, zimatamanda kukhulupirika kwanu mu msonkhano wa oyera mtima.
Iye uja ndiye amene adalenga nyenyezi za Akamwiniatsatana ndiponso Nsangwe, ndiye amene amasandutsa mdima kuti ukhale m'maŵa nasandutsa usana kuti ukhale usiku. Ndiye amene amaitana madzi am'nyanja ndi kuŵathira pa dziko lapansi. Dzina lake ndi Chauta.
Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri. Pamene adatumphutsa madzi kuchoka kunsi kwa dziko, ndipo mitambo idagwetsa mvula, adaonetsa nzeru zodziŵa zinthu.
Manja anga adamanga maziko a dziko lapansi, dzanja langa lamanja lidafunyulula mlengalenga. Ndikaitana dziko lapansi ndi dziko lakumwamba, zonsezo zimabwera pamodzi kwa Ine.
Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino.
Zakumwamba ndi zanu, dziko lapansi nalonso ndi lanu. Mudapanga dziko lonse ndi zonse zam'menemo.
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Inu mudaika maziko a dziko lapansi kalekale, ndipo zakumwamba mudazipanga ndi manja anu. Zonsezi zidzatha ngati malaya, koma Inu mulipobe. Inu mumazisintha ngati chovala, ndipo zimatha. Koma Inu simusintha, zaka zanu sizitha.
Dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba, kuseri kwa mlengalenga. Amaona anthu pansi ngati ziwala. Adafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchingira, ngati hema lokhalamo anthu.
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira.
Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi, mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala! Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo! Zonsezo zitamande dzina la Chauta! Paja Iye adaalamula, izo nkulengedwa.
Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake. Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta Wamphamvuzonse. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero. Pakuti iye ndi amene adaika dziko lapansi pa nyanja yaikulu, adalikhazika pa mitsinje yozama.
Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Mapiri asanabadwe, ndipo musanalenge dziko lapansi ndi pokhala anthu, ndinu Mulungu kuyambira muyaya mpaka muyaya.
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
Ndidzasinkhasinkha za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu, ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.
Chauta ndiye mfumu. Wavala ulemerero, wavala mphamvu ngati lamba. Iye adakhazikitsa dziko lapansi, silidzagwedezeka konse.
Nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wakutiwakuti, koma amene adapanga zonse, ndi Mulungu.
Paja milungu ya anthu a mitundu ina ndi mafano chabe, koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba.
Chauta akunena kuti, “Ndikulenga thambo lam'mwamba latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zakale sadzazikumbukiranso, zidzaiŵalika kotheratu.
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu. Kuli nyanja yaikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zinthu zosaŵerengeka, zinthu zamoyo, zazing'ono ndi zazikulu zomwe.
Kodi ndani adayesa kuchuluka kwa madzi am'nyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyesa kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani adayesa dothi lonse la dziko lapansi ndi dengu? Ndani adayesa kulemera kwa mapiri ndi magomo pa sikelo?
“Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba? Ona nyenyezi zili m'mwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene ziliripo!
Tamandani Chauta! Tamandani Chauta inu okhala kumwamba, mtamandeni inu okhala mu mlengalenga! Inu nyama zakutchire ndi zoŵeta zonse, inu zinthu zokwaŵa ndi mbalame zouluka! Inu mafumu a pa dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akuluakulu ndi olamulira dziko lapansi! Inu anyamata pamodzi ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe! Onsewo atamande dzina la Chauta, pakuti dzina lake lokha nlolemekezeka, ulemerero wake ndi woposa, pansi pano nkumwamba komwe. Chauta wakweza anthu ake poŵapatsa mphamvu. Walemekeza anthu ake onse oyera mtima, Aisraele amene Iye amaŵakonda. Tamandani Chauta! Mtamandeni inu angelo ake onse, mtamandeni inu magulu a ankhondo ake onse! Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi, mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala! Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo! Zonsezo zitamande dzina la Chauta! Paja Iye adaalamula, izo nkulengedwa. Adazikhazikitsa kuti zikhale mpaka muyaya, adaikapo lamulo limene silingathe kusinthika.
Paja milungu yonse ya mitundu ina ya anthu ndi mafano chabe. Koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba.
Koma kwa ife, Mulungu ndi mmodzi yekha, ndiye Atate, amene adalenga zonse, ndipo moyo wathu umalinga kwa Iye. Tilinso ndi Ambuye amodzi okha, Yesu Khristu. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo ife tili ndi moyo chifukwa cha Iye.
Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba. Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba, ndiye amene amadzetsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amang'animitsa mphezi za mvula, amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga.
Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso.
Mudalenga usana ndi usiku. Mudaika mwezi ndi dzuŵa m'malo mwake. Mudalemba malire a dziko lapansi, mudakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.
Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera.
Inu mudapanga mwezi kuti uzisiyanitsa nyengo, ndipo dzuŵa limadziŵa nthaŵi yake yoloŵera.
Akutero Chauta amene adalenga zakumwamba, ndi Iyeyo Mulungu amene adaumba ndi kulenga dziko lapansi, ndipo adalikhazikitsa mwamphamvu. Sadalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma kuti likhale malo okhalamo anthu. Iyeyo akunena kuti: “Chauta ndine, palibenso wina ai.
Kodi ndinu yani kuti muziiŵala Chauta, Mlengi wanu, amene adayalika zakuthambo, ndi kuika maziko a dziko lapansi? Kodi ndinu yani kuti nthaŵi zonse muziwopa ukali wa anthu okuzunzani, amene angofuna kukuwonongani? Ukali wa anthu okuzunzaniwo tsopano uli kuti?
Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
“Inu aYobe, tamvani izi, imani, muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu. Kodi mukudziŵa m'mene Mulungu amazichitira, ndi m'mene amang'anipitsira mphezi m'mitambo yake? Kaya mukudziŵa m'mene Mulungu amayalira mitambo, ntchito yosonyeza nzeru zake zodabwitsa,
Chauta akunena kuti, “Thambo lam'mwamba ndiye mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndiye chopondapo mapazi anga. Kodi ndi nyumba yotani imene mungathe kundimangira inu? Ndi malo otani amene inu mungandikonzere kuti Ine ndizipumulirapo? “Kondwera nayeni Yerusalemu, musangalale chifukwa cha iye, inu nonse amene mumakonda mzinda umenewu. Kondwera nayeni mwachimwemwe, nonsenu amene mukumlira. Mudzalandira chitonthozo ndi kukondwera nacho kwambiri. Mudzagaŵana naye ulemerero wake ndi kusangalala nawo.” Chauta akunena kuti, “Ndidzakupatsa zabwino zochuluka ngati mtsinje wa madzi. Chuma cha mitundu ya anthu chidzafika kwa inu ngati mtsinje wosefukira. Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene mai wake wamnyamulira pambalipa, kapena akumluluza pa maondo. Ndidzakusangalatsani ku Yerusalemu monga momwe mai amasangalatsira mwana wake. Mudzasangalala poona zimenezi. Zidzakulimbitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu. Tsono mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndimathandiza amene amandimvera, ndipo ndimakwiyira adani anga.” “Pajatu Chauta adzabwera ndi moto. Ndipo magaleta ake adzafika ngati mkuntho. Iye adzaonetsa poyera ukali wake, ndipo adzalanga adani ake ndi malaŵi a moto. Adzalanga anthu onse a pa dziko lapansi ndi moto ndi lupanga. Alipo ambiri amene Chauta adzaŵapha.” Chauta akunena kuti, “Amene akuti akudzipatula ndi kudziyeretsa pamene akufuna kuchita miyambo yam'minda ija, ali ndi mtsogoleri wao yemwe, nkumadya nyama yankhumba, mbeŵa ndi zonyansa zina, onsewo adzafera limodzi,” akuterotu Chauta. “Ndikudziŵa ntchito zao ndi maganizo ao. Ndikubwera kudzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndi a zilankhulo zonse. Adzabweradi ndipo adzaona ulemerero wanga. “Ndidzaika chizindikiro pakati pao. Mwa iwowo padzakhala ena opulumukako amene ndidzaŵatuma kwa anthu a mitundu ina, monga a ku Tarisisi, a ku Puti ndi a ku Ludi, akatswiri a mauta, ndiponso ku Tubala, ku Yavani, ndi ku maiko akutali amene sadamvepo za mbiri yanga kapena kuwona ulemerero wanga. Iwowo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina. Zinthu zonsezi ndidazilenga ndine, tsono zonsezi nzanga,” akutero Chauta. “Anthu amene ndimakondwera nawo ndi aŵa: odzichepetsa ndi olapa, ondiwopa ndi omvera mau anga.
Paja Mulungu amene ndi Mlengi wa zonse ndipo zonse zimalinga kwa Iye, adafuna kufikitsa ana ake ambiri ku ulemerero. Tsono kudaamuyenera kuti mwa njira ya zoŵaŵa, amsandutse Yesu mtsogoleri wangwiro woŵatsogolera ku chipulumutso.
Zakumwamba zimalalika za kulungama kwake, ndipo anthu a mitundu yonse amaona ulemerero wake.
Mitundu ya anthu ili ngati kadontho ka madzi mu mtsuko, ilinso ngati fumbi chabe pa sikelo. M'manja mwa Chauta zilumba nzopepuka ngati fumbi.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri. Mumavala ulemu ndi ufumu. Inu mumatumphutsa akasupe m'zigwa, mitsinje imayenda pakati pa mapiri. Imapatsa nyama zonse zakuthengo madzi akumwa, mbidzi zimapherapo ludzu. Mbalame zimamanga zisa pafupi ndi mitsinjeyo, zimaimba m'nthambi za mitengo. Inu mumathirira mapiri ndi madzi ochokera ku malo anu akumwamba. Dziko lapansi ladzaza ndi madalitso anu. Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka. Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu. Mitengo ya Chauta amaithirira ndi madzi ambiri, mikungudza ya ku Lebanoni imene adaibzala. Mbalame zimamanga zisa m'menemo, dokowe amamanga chisa m'mikungudzamo. M'mapiri aatali ndimo m'mene mumakhala mbalale, m'matanthwe ndimo m'mene mumathaŵira mbira. Inu mudapanga mwezi kuti uzisiyanitsa nyengo, ndipo dzuŵa limadziŵa nthaŵi yake yoloŵera. Mumadzifunditsa ndi kuŵala ngati chovala, mwatambasula mlengalenga ngati hema.
“Atate, ndifuna kuti amene mudandipatsa, iwonso akhale pamodzi ndi Ine kumene ndili. Ndifuna kuti aone ulemerero wanga umene mudandipatsa, chifukwa mudandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
Ine ndinalipo kale, pamene ankakhazikitsa zakumwamba, pamene ankalemba mzere wa malire a nyanja yozama, pamene ankaika thambo m'malo mwake, pamene ankatsekula akasupe a m'nyanja yozama, pamene ankaika malire a nyanja kuti madzi ake asabzole malirewo, pamene ankaika maziko a dziko lapansi.
Apa akuiŵala dala kuti kalelo Mulungu atanena mau, zakuthambo zidalengedwa, ndipo dziko lapansi lidapangidwa ndi madzi kufumira m'madzi.
Ndiwo amene amamanga malo ao okhalamo kumwamba, naika thambo ngati denga la dziko lapansi, amaitana madzi akunyanja naŵakhuthulira pa dziko lapansi. Iwowo dzina lao ndi Chauta.
Inu mumathirira mapiri ndi madzi ochokera ku malo anu akumwamba. Dziko lapansi ladzaza ndi madalitso anu. Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka.
“Gwetsa mvula, iwe thambo, kuchokera kumwamba, mitambo ikhuthule chilungamo chopulumutsa. Dziko lapansi litsekuke kuti patuluke chipulumutso, kuti chilungamo chimerepo. Ndine, Chauta, amene ndidalenga zimenezi.”
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
Atatero adalumbira m'dzina la Mulungu wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene adalenga thambo lakumwamba ndi zonse zokhala kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo, ndiponso nyanja ndi zonse zokhala m'menemo. Mngeloyo kulumbira kwake adati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Chauta adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale ndi cholinga chake, ngakhale anthu oipa, kuti aone tsiku la mavuto.
Onsewo amadziŵika ndi dzina langa, ndidaŵalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndidaŵapanga ndi kuŵapatsa moyo.”
Pamwamba pa thambo lija panali chinthu china chooneka ngati mpando waufumu, wopangidwa ndi mwala wa safiro. Pamwamba pa mpandowo panali chinthu chooneka ngati munthu. M'mwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo choŵala konsekonse ngati moto. M'munsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokhawo. Kuŵala kwamphamvu kudaamzungulira munthuyo. Kuŵalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza m'mitambo tsiku limene kwagwa mvula. Umu ndi m'mene ulemerero wa Chauta unkaonekera. Ndidangoti ntauwona, ndidadzigwetsa pansi chafufumimba, ndipo ndidamva mau ondilankhula.
Adalenga miyuni yaikulu yamumlengalenga, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Dzuŵa kuti lizilamulira usana, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira usiku, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Mngeloyo adanena mokweza mau kuti, “Opani Mulungu ndi kumtamanda, pakuti yafika nthaŵi yoti aweruze anthu. Mumpembedze Iye amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe a madzi.”
“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
Ndiye amene adalenga nyenyezi za Mlalang'amba ndi Akamwiniatsatana, Nsangwe ndi Kumpotosimpita.
Ulemerero wa Chauta ukhalebe mpaka muyaya, Chauta akondwe nazo ntchito zakezo, Iye amati akayang'ana dziko lapansi, limanjenjemera, akakhudza mapiri, mapiriwo amafuka nthunzi.
Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka pa mibadwo yonse. Inu mwakhazikitsa dziko, ndipo siligwedezeka. Zolengedwa zikupezeka lero lino chifukwa cha kulamula kwanu, pakuti zinthu zonse zimakutumikirani.
Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi.
Ntchito za Chauta nzazikulu, onse okondwera nazo amazilingalira. Ntchito zake ndi zaulemu ndi zaufumu, ndipo kulungama kwake nkwamuyaya.
Wotchedwa Mauyo anali m'dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa Iye, komabe anthu apansipano sadamzindikire.
Amakweza osauka kuŵachotsa pa fumbi, amachotsa anthu osoŵa pa dzala, amaŵakhazika pamodzi ndi akalonga, amaŵapatsa mpando waulemu. Nsanamira za dziko lapansi nzake za Chauta, adakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.