Loŵerani tsiku la Sabata, lomwe ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri, lomwe limatchedwanso Shabat mu Chiheberi, kutanthauza kupuma. Ndi tsiku lokhalo lotchulidwa ndi dzina lake m'Baibulo, ndipo ndi tsiku lopatulika la mlungu. Ndi lamulo limodzi mwa malamulo amene Mulungu anapatsa Mose kwa anthu Ake. Yesu anati Iye ndiye Ambuye wa Sabata, pakuti Mwana wa Munthu ndiye Ambuye wa tsiku la Sabata (Mateyu 12:8).
Yesu anachiritsa munthu wopunduka pa dziwe la Betesida pa Sabata, ndipo Ayuda anayamba kumutsatira ndi kufunafuna njira yomupha, ponena kuti anali kugwira ntchito pa tsiku la Sabata. Yesu anawayankha kuti, "Atate wanga akugwira ntchito, ndipo Inenso ndikugwira ntchito" (Yohane 5:16-17). Kwa atsogoleri achipembedzo amenewa, miyambo inali yofunika kwambiri kuposa anthu, koma Yesu anatsindika kuti Iye ndi Atate ake akupitiriza kugwira ntchito.
Kalekale, tanthauzo lenileni la Sabata linasokonezeka, monga momwe zilili masiku ano m'mipingo ina yomwe imasunga Sabata, yotaya njira yolondola pankhaniyi. Tanthauzo lenileni la Sabata ndi kusinkhasinkha za njira zathu, kuŵerenga Mawu a Mulungu ndi banja, ndikuyamikira madalitso ake onse.
Mulungu safuna kuti anthu azitsatira malamulo ake pakamwa pokha, mitima yawo ili kutali ndi Iye. Sikuti kungosunga tsiku lokha, koma kukhala moyo wotsatira malamulo ake tsiku lililonse kuti tidzipulumutse ku chilango chamuyaya chomwe chili mu gehena kwa iwo amene satsatira chifuniro cha Mulungu.
Khristu nthawi zonse adzakhala mpumulo wathu; mwa Iye timapeza mtendere weniweni (Aheberi 4:3). Ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu ananenera, "Chifukwa chake, ndinalumbira m'kukwiya kwanga, 'Sadzalowa mu mpumulo wanga'," ngakhale ntchito zake zinamalizidwa kuyambira pachiyambi pa dziko lapansi.
“Uza Aisraele kuti, ‘Muzisunga Sabata, tsiku langa lopumula, chifukwa ndilo chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi inu ndi zidzukulu zanu, choonetsa kuti Ine ndine Chauta, amene ndimakuyeretsani. Motero muzisunga tsiku la Sabata, chifukwa ndi loyera kwa inu. Munthu aliyense wosalisunga, aphedwe. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo adzachotsedwe pakati pa anthu anzake. Munthu agwire ntchito zake zonse pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku la Sabata lopumula, tsiku loyera la Chauta. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limeneli aphedwe. Aisraele azisunga tsiku la Sabatalo, ndipo mibadwo yonse yakutsogoloko izidzalisunga ngati pangano losatha. Chimenechi ndi chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi Aisraele, chakuti Ine Chauta ndidalenga kumwamba ndi dziko lapansi pa masiku asanu ndi limodzi, ndipo ndidapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.’ ”
Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi Mulungu adamaliza ntchito imene ankachitayo, ndipo adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Adamu adazitcha maina nyama zonse, mbalame ndi zamoyo zonse zakuthengo. Komabe panalibe mnzake woti azimthandiza. Tsono Chauta adagonetsa Adamu tulo tofanato, ndipo ali m'tulo choncho, Mulungu adamchotsako nthiti, natsekapo ndi mnofu pamalopo. Chauta Mulungu adapanga mkazi ndi nthiti imene adaichotsa kwa Adamu uja, ndipo mkaziyo Mulungu adabwera naye kwa iye. Adamu adati, “Uyutu ndiye ndi fupa lochokera ku mafupa anga, mnofu wochokera ku mnofu wanga. Adzatchedwa Mkazi, chifukwa watengedwa kwa Mwamuna.” Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi. Mwamunayo ndi mkazi wake uja, onse anali maliseche, komabe sankachita manyazi. Mulungu adadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, naliyeretsa, chifukwa choti pa tsiku limenelo adapuma atatsiriza zonse zimene ankachita.
“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu.
“Uzisunga tsiku la Sabata ndi kuliyeretsa, monga momwe Ine Chauta, Mulungu wako, ndidakulamulira. Uzigwira ntchito zako zonse ndi kuzitsiriza pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata la Chauta, Mulungu wako. Pa tsiku limenelo, usagwire ntchito iliyonse iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, wantchito wako wamwamuna, mdzakazi wako, ng'ombe yako, bulu wako, kaya choŵeta chako chilichonse, ngakhale mlendo wokhala m'mudzi mwako. Motero atumiki ako aamuna ndi aakazi azipumanso monga iwe wemwe. Uzikumbukira kuti paja udaali kapolo m'dziko la Ejipito, ndipo kuti Ine Chauta, Mulungu wako, ndidakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula. Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wako, adakulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata ndi kuliyeretsa.
Chauta akunena kuti, “Muzidziletsa kuchita zanuzanu pa Sabata, osagwira ntchito zanu pa tsiku langa loyera. Tsiku la Sabatali muzilitcha kuti chinthu chosangalatsa, tsiku loyera la Chauta muzilitcha kuti chinthu cholemekezeka. Muzililemekeza pakusayendayenda, poleka kugwira ntchito zanu ndiponso posakamba nkhani zachabe. Mukatero ndiye kuti mudzakondwa mwa Ine, Chauta, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndidapatsa Yakobe kholo lanu. Ine Chauta ndalankhula zimenezi ndi pakamwa panga.”
Nthaŵi ina Yesu adafika ku Nazarete kumene adaaleredwa. Ndipo pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapemphero, monga adaazoloŵera, naimirira kuti aŵerenge mau.
Tsono Yesu popitiriza mau, adauza Afarisiwo kuti, “Mulungu adaika tsiku la Sabata kuti likhale lothandiza anthu. Sadalenge anthu kuti akhale akapolo a tsiku la Sabata ai. Choncho Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.”
Ndidati, ‘Ine ndine Chauta Mulungu wanu. Muzitsata malamulo anga, ndi kumvera malangizo anga. Pamenepo Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, Muzilemekeza masiku anga a Sabata ngati opatulika, kuti adzakhale ngati chizindikiro pakati pa Ine ndi inu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wanu.’
Nanji munthu, amene amaposa nkhosa kutalitali! Ndiye kutitu Malamulo amalola kuchita zabwino pa tsiku la Sabata.”
Kumbukirani kuti ndine Chauta, amene ndidakupatsani tsiku la Sabata. Tsono chifukwa cha chimenechi ndimakupatsani chakudya chokwanira masiku aŵiri pa tsiku lachisanu ndi chimodzi. Aliyense azingokhala komwe aliriko pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Asachoke ndi mmodzi yemwe pakhomo pake.” “Kukadakhala bwino Chauta akadatiphera ku Ejipito konkuja, kumene tinkakhala tikudya nyama ndi buledi, ndipo tinkakhuta. Koma inu mwatifikitsa kuchipululu kuno kuti mutiphe tonse ndi njala.” Motero anthu sankagwira ntchito pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.
Wina aliyense asakuzengeni mlandu pa nkhani yokhudza zakudya kapena zakumwa, kapena pa zokhudza masiku a chikondwerero, kapena a mwezi wokhala chatsopano, kapena pa zokhudza tsiku la Sabata. Zonsezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zenizeni zimene zilikudza, koma zenizenizo ndi Khristu amene.
Ndipo ngati anthu a mitundu ina ya m'dzikomo abwera ndi zinthu zamalonda kapena tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la sabata, sitidzaŵagula pa tsiku limenelo, kapenanso pa tsiku loyera lina lililonse. Pa chaka chilichonse chachisanu ndi chiŵiri, tidzagoneka munda osaulima, ndipo tidzafafaniza ngongole zonse.
Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi, munthu amene amalimbikira kuzichita, amene amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga, ndipo amadziletsa kuchita zoipa. Mkunja amene waphatikana ndi Chauta, asanene kuti, “Mosapeneka konse Chauta adzandichotsa pakati pa anthu ake.” Nayenso wofulidwa asanene kuti, “Ine ndiye ndine wouma ngati chikuni.” Paja Chauta akuti, “Ofulidwa amene amalemekeza masiku a Sabata, amene amachita zokomera Ine, ndi kusunga chipangano changa mokhulupirika, Ineyo ndidzaŵapatsa dzina ndi mbiri yabwino pakati pa anthu anga, m'kati mwa fuko langa, koposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi. Ndidzaŵapatsa mbiri yabwino yosatha, yosaiŵalika.” Chauta akutinso, “Akunja amene amaphatikana ndi Chauta mpaka kumgwirira ntchito, kumkonda, ndi kumtumikira, amenenso amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga, nasunga bwino chipangano changa, Ine ndidzaŵafikitsa ku Ziyoni, phiri langa lopatulika. Ndidzaŵapatsa chimwemwe m'nyumba yanga yopemphereramo. Zopereka zao zootcha ndiponso nsembe zao zinanso ndidzazilandira pa guwa langa. Paja Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”
Tiyesetse tsono kuloŵa mu mpumulowo, kuwopa kuti wina aliyense angakhale wosamvera monga iwo aja, nalephera kuloŵamo.
Pempherani kuti nthaŵi pamene muzidzathaŵa, isadzakhale nyengo yachisanu, kapena pa tsiku la Sabata.
Nkwabwino kuthokoza Chauta, kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse. Koma ine mwandilimbitsa ngati njati. Mwandidzoza ndi mafuta atsopano. Maso anga aona kuwonongeka kwa adani anga, makutu anga amva za kugwa kwa adani ondiwukira. Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni. Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu. Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira, imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota. Nkwabwino m'maŵa kulalika za chikondi chanu chosasinthika, ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu,
Tsiku lina la Sabata Yesu ankaphunzitsa m'nyumba ina yamapemphero. M'menemo munali mai wina amene anali ndi mzimu woipa umene udamudwalitsa zaka 18. Anali ndi msana wokhota, mwakuti sankatha konse kuŵeramuka. Pamene Yesu adamuwona, adamuitana namuuza kuti, “Mai inu, mwamasuka ku matenda anu.” Adamsanjika manja, ndipo pompo maiyo adaongoka, nayamba kutamanda Mulungu. Koma mkulu wa nyumba yamapemphero ija adakwiya, poona kuti Yesu wachiritsa munthu pa tsiku la Sabata. Tsono mkuluyo adauza anthu onse kuti, “Pali masiku asanu ndi limodzi antchito. Muzibwera masiku ameneŵa kudzachiritsidwa, osati pa tsiku la Sabata ai” Koma Ambuye adati, “Anthu achiphamaso inu, kodi suja nonsenu mumamasula ng'ombe zanu kapena abulu anu pa tsiku la Sabata kukaŵamwetsa madzi? Nanga maiyu, amene ali mwana wa Abrahamu, ndipo Satana adaamumanga zaka 18, kodi sikunayenera kuti amasulidwe ku nsinga imeneyi pa tsiku la Sabata?” Yesu atanena zimenezi, adani ake onse adachita manyazi. Koma anthu ena onse adakondwera chifukwa cha ntchito zodabwitsa zimene Iye ankachita.
Yesu adakaloŵanso m'nyumba yamapemphero. M'menemo mudaali munthu wina wopuwala dzanja. Pakuti anali atachiritsa anthu ambiri, ndipo onse amene adaali ndi matenda ankakankhana pofuna kuti amkhudze. Mizimu yoipa inkati ikamuwona, inkadzigwetsa pansi pafupi ndi Iye nkumafuula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma Iye ankailetsa mwamphamvu kuti isamuulule. Yesu adakwera ku phiri, ndipo adaitana anthu amene Iye mwini ankaŵafuna, iwo nkupitadi kumene kunali Iyeko. Tsono adasankhapo khumi ndi aŵiri, naŵatcha dzina loti, “Atumwi.” Adaŵauza kuti, “Ndasankha inu kuti muzikhala nane, ndidzakutumani kukalalika, ndipo mudzakhala ndi mphamvu zotulutsira mizimu yoipa.” Anthu khumi ndi aŵiri amene adaaŵasankhawo ndi aŵa: Simoni (amene Yesu adamutcha dzina loti Petro), Yakobe ndi mbale wake Yohane, ana aja a Zebedeo (ameneŵa adaŵapatsa dzina lina lakuti Aboaneje, ndiye kuti “Oopsa ngati bingu”), Andrea ndi Filipo, kudza Bartolomeo, Mateyo, Tomasi, Yakobe (mwana wa Alifeyo), Tadeyo, Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote,) ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.) Anthu ena ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankangomuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthuyo pa tsiku la Sabata. Pambuyo pake Yesu adapita kwao, ndipo anthu ambiri adasonkhananso, kotero kuti Iye ndi ophunzira ake analibe ndi mpata womwe wodyera chakudya. Achibale ake atamva zimenezi, adabwera kuti adzamtenge, chifukwa ankati, “Wachita misala.” Aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu, ankanena kuti, “Munthu ameneyu wagwidwa ndi Belezebulu.” Ankatinso, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa nzochokera kwa mkulu wa mizimuyo.” Tsono Yesu adaitana anthu kuti adze pafupi, nanena mwafanizo kuti, “Kodi a mu ufumu wa Satana angathe bwanji kutulutsana okhaokha? Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo sungalimbe. Ndipo anthu a m'banja limodzi akayamba kugaŵikana, banja lotere silingalimbe. Tsono ngati a mu ufumu wa Satana aukirana okhaokha nagaŵikana, Satanayo sangalimbe, ndiye kuti watha basi. “Wina sangathe kungoloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkumulanda katundu wake. Amayamba wammanga, kenaka ndiye kufunkha za m'nyumba mwakemo. “Ndithu ndikunenetsa kuti anthu angathe kukhululukidwa machimo onse, ngakhalenso zonena zao zonse zomunyoza Mulunguyo. Koma aliyense wonyoza Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa konse. Tchimo lakelo limakhala mpaka muyaya.” Yesu adalamula munthuyo kuti, “Imirira, bwera kutsogolo kuno.” Yesu adalankhula zimenezi poona kuti anthu aja ankanena kuti, “Wagwidwa ndi mzimu woipa.” Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako. Adaima panja, natuma anthu kuti akamuitane. Anthu ambirimbiri adaakhala pansi pomzungulira. Ndiye iwo aja adamuuza kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akukufunani.” Koma Iye adati, “Amai anga! Abale anga! Otinso?” Apo adayang'ana anthu amene anali pomzungulira aja nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi aŵa. Aliyense wochita zimene Mulungu akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.” Tsono adafunsa anthuwo kuti, “Kodi pa tsiku la Sabata chololedwa nchiti? Kuchitira anthu zabwino, kapena kuŵachita zoipa? Kupulumutsa moyo wa munthu, kapena kuuwononga?” Anthuwo adangoti chete. Pamenepo Yesu mtima wake udamuŵaŵa, poona kuti anali anthu okanika chotero, ndipo adaŵayang'ana ndi mkwiyo. Tsono adalamula munthuyo kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino. Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo ndi anthu a m'chipani cha Herode, kuti apangane njira yophera Yesu.
Kuchokera ku Perga iwo adapitirira nakafika ku Antiokeya m'dera la Pisidiya. Pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapempherero ya Ayuda, nakhala pansi.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Ophunzira ake anali ndi njala, ndipo adayamba kuthyolako ngala za tirigu nkumadya. M'menemo munali munthu wopuwala dzanja. Tsono anthu ena amene ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, adamufunsa kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata?” Yesu adaŵayankha kuti, “Ndani mwa inu atakhala ndi nkhosa imodzi, nkhosayo nkugwa m'dzenje pa tsiku la Sabata, angapande kuigwira nkuitulutsa? Nanji munthu, amene amaposa nkhosa kutalitali! Ndiye kutitu Malamulo amalola kuchita zabwino pa tsiku la Sabata.” Atatero, adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino ngati linzake. Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo kuti apangane njira yophera Yesu. Yesu atamva za upowo, adachokako kumeneko. Anthu ambiri adamtsatira, ndipo Iye adaŵachiritsa onse amene ankadwala. Koma adaŵalamula kuti asakamuulule. Adaachita zimenezi kuti zipherezere zimene Mulungu adaalankhulitsa mneneri Yesaya kuti, “Nayu mtumiki wanga amene ndamsankha. Ndimamkonda, ndipo mtima wanga umasangalala naye kwambiri. Ndidzaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzalalika za chilungamo kwa anthu a mitundu ina. Iye sadzachita makani, kapena kufuula. Palibe munthu wodzamva mau ake m'miseu ya m'mizinda. Pamene Afarisi adaona zimenezi, adauza Yesu kuti, “Taonani, ophunzira anu akuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata.”
Munthu agwire ntchito zake zonse pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku la Sabata lopumula, tsiku loyera la Chauta. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limeneli aphedwe.
Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata la Chauta, Mulungu wako. Pa tsiku limenelo, usagwire ntchito iliyonse iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, wantchito wako wamwamuna, mdzakazi wako, ng'ombe yako, bulu wako, kaya choŵeta chako chilichonse, ngakhale mlendo wokhala m'mudzi mwako. Motero atumiki ako aamuna ndi aakazi azipumanso monga iwe wemwe.
Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala mwezi, ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Chauta.
Nthaŵi imeneyo ndidaona anthu m'dziko la Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la sabata. Ena ankaunjika tirigu milumilu, nkumasenzetsa abulu. Enanso ankatenga vinyo, mphesa, nkhuyu, ndiponso katundu wa mtundu uliwonse, nkumabwera naye ku Yerusalemu, pa tsiku la sabata. Tsono ndidaŵachenjeza kuti asamagulitse chakudya pa tsiku la sabata. Nawonso anthu ena a ku Tiro okhala mu Yerusalemu, ankabwera ndi nsomba ndi zamalonda za mtundu uliwonse, nkumazigulitsa pa tsiku la sabata kwa anthu a m'dziko la Yuda ndiponso kwa anthu okhala mu mzinda wa Yerusalemu. Pomwepo ndidadzudzula atsogoleri a Ayuda, ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Monga simukuzindikira choipa chimene mukuchitachi pakuipitsa tsiku la sabata chonchi? Makolo anu adachitanso motero momwemu, ndipo Mulungu wathu adadzetsa chiwonongeko pa ife ndi pa mzinda uno. Koma inu mukufuna kuutsanso mkwiyo wa Chauta pa Aisraele, pamene mukuipitsa tsiku la sabata motere.” Nchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuziyamba kuda, tsiku la sabata lisanayambike, azitseka zipata zonse za Yerusalemu, ndipo asazitsekule mpaka tsiku la sabata litapita. Ndidaika antchito anga ena oyang'anira pa zipata, kuti katundu aliyense asaloŵe mumzindamo pa tsiku la sabata. Paja ameneŵa sadapite kukakomana ndi ana a Aisraele, kuti akaŵapatse buledi ndi madzi. M'malo mwake adalemba Balamu kuti aŵatemberere. Komabe Mulungu wathu matembererowo adaŵasandutsa madalitso.” Motero anthu amalonda ogulitsa zinthu zamitundumitundu ankagona kunja kwa mzinda wa Yerusalemu kamodzi kapena kaŵiri konse. Koma ndidaŵachenjeza ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Mukachitanso zimenezi ndidzakumangani.” Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka m'tsogolo mwake, anthuwo sadabwerenso pa tsiku la sabata. Kenaka ndidaŵalamula Alevi kuti adziyeretse ndipo abwere kudzalonda pa zipata, kuti tsiku la sabata lisungike ngati lopatulika. Inu Mulungu wanga, mukumbukire zimenezinso pondikomera mtima, ndipo mundisunge potsata chikondi chanu chachikulu chosasinthika.
Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri, lidzakhala la Sabata, tsiku lanu lopumula, loperekedwa kwa Chauta. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo, adzaphedwa.
Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi Mulungu adamaliza ntchito imene ankachitayo, ndipo adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.
Pa tsiku la Sabata lililonse Aroni aziika makeke a nsembeyo mosalephera pamaso pa Chauta m'malo mwa Aisraele, kuti chikhale chipangano chamuyaya.
Masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wosatupitsa. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, muzisonkhana kuti mupembedze Chauta, Mulungu wanu, ndipo musadzagwire ntchito pa tsiku limenelo.
Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Akuyenda choncho, ophunzira ake adayamba kuthyolako ngala za tirigu nkumadya. Apo Afarisi adafunsa Yesu kuti, “Bwanji ophunzira anuŵa akuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata?” Iye adati, “Bwanji mukuchita ngati simudaŵerenge konse zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala? Suja adaaloŵa m'nyumba ya Mulungu, pa nthaŵi imene Abiyatara anali mkulu wa ansembe onse, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo nkosaloledwa kuti wina aliyense nkumudya, kupatula ansembe okha. Komanso adaagaŵirako anzake aja amene adaali naye.”
Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja adabwera mbandakucha pa tsiku lotsatira Sabatalo, kudzaona manda aja.
Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.
Nanga Mulungu ankanena za yani pamene adaati, “Ndikulumbira kuti ameneŵa sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera?” Pajatu ankanena za anthu amene adaamuukira. Motero tikuwona kuti anthuwo sadathe kuloŵa, chifukwa cha kusakhulupirira.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Pa tsiku lina la Sabata Yesu adakadya kwa mkulu wina wa m'gulu la Afarisi, ndipo Afarisi anzake ankamupenyetsetsa. Koma akakuitana, kakhale pa malo otsika, kuti amene adakuitana uja adzakuuze kuti, ‘Bwenzi langa, dzakhale pa malo aulemu pano.’ Apo udzalandira ulemu pamaso pa onse amene uli nao podyera. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.” Yesu adauzanso Mfarisi uja amene adaamuitana kudzadya naye kuti, “Ukamakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamaitana abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anzako achuma, chifukwa mwina iwonso adzakuitanako, motero udzalandiriratu mphotho yako. Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu. Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.” Munthu wina amene ankadya nao, atamva zimenezi, adauza Yesu kuti, “Ngwodala munthu amene adzadye nao mu Ufumu wa Mulungu.” Koma Yesu adamuphera fanizo, adati, “Munthu wina adaakonza phwando lalikulu, naitana anthu ambiri. Nthaŵi ya phwando itakwana adatuma wantchito wake kukauza oitanidwa aja kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’ Koma onsewo mmodzimmodzi adayamba kupereka zifukwa zokanira. Woyamba adati, ‘Ndidagula munda, tsono ndikuyenera kupita kuti ndikauwone. Pepani sindibwera.’ Wina adati, ‘Ndidagula ng'ombe khumi zapagoli, ndiye ndikukaziyesa. Pepani sindibwera.’ Pomwepo pamaso pake panali munthu wina wambulu. Ndipo wina adati, ‘Ndangokwatira tsopano apa, choncho sinditha kubwera.’ Tsono wantchitoyo atabwerako adadzasimbira mbuye wake zonsezo. Apo mwini nyumbayo adapsa mtima, nauza wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msanga ku miseu yaikulu ndi yaing'ono ya mumzinda muno ukapeze anthu osauka, otsimphina, akhungu ndi opunduka, ukabwere nawo kuno.’ Atabwerako wantchito uja adati, ‘Bwana, ndachita zija munandilamulazi, koma malo akalipobe.’ Apo mbuye uja adamuuza wantchitoyo kuti, ‘Pita ku miseu ndi ku njira za kunja kwa mudzi, ukaŵakakamize anthu kubwera kuno, kuti nyumba yanga idzaze. Kunena zoona, mwa anthu amene ndidaaŵaitana aja palibe ndi mmodzi yemwe amene adzalilaŵe phwando langali.’ ” Chikhamu cha anthu chinkatsagana ndi Yesu. Tsono Iye adatembenuka naŵauza kuti, “Aliyense wofuna kukhala wophunzira wanga, azikonda Ine koposa atate ake ndi amai ake, mkazi wake ndi ana ake, abale ake ndi alongo ake, ndiponso koposa ngakhale moyo wake womwe. Aliyense amene sasenza mtanda wake nkumanditsata, sangakhale wophunzira wanga. “Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza? Akapanda kutero, mwina adzaika maziko, nkulephera kuitsiriza. Apo anthu onse, poona zimenezi, adzayamba kumseka. Yesu adafunsa akatswiri a Malamulo ndi Afarisi kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata, kapena ai?” Adzati, ‘Mkulu uyu adaayamba kumanga nyumba, koma adalephera kuitsiriza.’ “Chimodzimodzinso kodi ndi mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi aŵiri. Tsono ngati siingathe, idzatuma nthumwi kukapempha mtendere, mfumu ina ija ikali kutali. “Chonchonso aliyense mwa inu amene sasiya zonse zimene ali nazo, sangakhale wophunzira wanga.” “Mchere ndi wabwino. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Ulibenso ntchito ngakhale pa munda, kapena pa dzala. Amangoutaya basi. Amene ali ndi makutu akumva, amve!” Koma iwo adangoti chete. Tsono Yesu adatenga munthuyo, ndipo atamchiritsa, adamuuza kuti azipita. Kenaka adaŵafunsa kuti, “Ndani mwa inu, bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime pa tsiku la Sabata, sangaitulutse pa Sabata pomwepo?” Iwo adasoŵa poyankha.
Mutole chakudya pa masiku asanu ndi limodzi. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, tsiku la Sabata, chakudyacho sichidzapezeka.” Pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo anthu ena adaapita kuti akatole chakudya, koma sadachipeze. Pamenepo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi mudzakhalabe osamvera mau anga ndi malamulo anga mpaka liti? Kumbukirani kuti ndine Chauta, amene ndidakupatsani tsiku la Sabata. Tsono chifukwa cha chimenechi ndimakupatsani chakudya chokwanira masiku aŵiri pa tsiku lachisanu ndi chimodzi. Aliyense azingokhala komwe aliriko pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Asachoke ndi mmodzi yemwe pakhomo pake.” “Kukadakhala bwino Chauta akadatiphera ku Ejipito konkuja, kumene tinkakhala tikudya nyama ndi buledi, ndipo tinkakhuta. Koma inu mwatifikitsa kuchipululu kuno kuti mutiphe tonse ndi njala.” Motero anthu sankagwira ntchito pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.
Kumeneko anthu otigwira ukapolo adatipempha kuti tiimbe nyimbo. Otizunza adatipempha kuti tisangalale, adati, “Tatiimbiraniko nyimbo ya ku Ziyoni.”
Mukatero ndiye kuti mudzakondwa mwa Ine, Chauta, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndidapatsa Yakobe kholo lanu. Ine Chauta ndalankhula zimenezi ndi pakamwa panga.”
Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya. Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu. Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Paja kuyambira kalekale mu mzinda uliwonse muli anthu ophunzitsa Malamulo a Mose, ndipo amaŵerenga mau ake m'nyumba zamapemphero pa tsiku la Sabata lililonse.”
Kaya simudaŵerengenso m'Malamulowo kuti m'Nyumba ya Mulungu, pa tsiku la Sabata, ansembe amaphwanya lamulo lokhudza tsiku la Sabata, komabe saŵayesa olakwa? Pakuti aliyense wochita zimene Atate anga akumwamba akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.” Ndipotu ndikunenetsa kuti pali wina pano woposa Nyumba ya Mulunguyo.
Motero muzisunga tsiku la Sabata, chifukwa ndi loyera kwa inu. Munthu aliyense wosalisunga, aphedwe. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo adzachotsedwe pakati pa anthu anzake.
Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.
Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Pena pake ponena za tsiku lachisanu ndi chiŵiri pali mau akuti, “Mulungu adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, kuleka ntchito zake zonse.”
Mudalenga kumpoto ndi kumwera. Mapiri a Tabori ndi Heremoni akukutamandani ndi chimwemwe.
Litafika tsiku la Sabata, Iye adayamba kuphunzitsa m'nyumba yamapemphero. Anthu ambiri amene ankamvetsera adadabwa kwambiri nkumanena kuti, “Kodi Iyeyu zonsezi adazitenga kuti? Nzeru zimene adalandirazi nzotani? Akutha bwanji kuchita zinthu zamphamvu zotere?
Musabwere nazonso nsembe zanu zachabechabe. Utsi wake umandinyansa. Sindingapirire misonkhano yanu yamapemphero, kapenanso zikondwerero za pokhala mwezi ndi za Sabata, sindingapirire mapemphero oipitsidwa ndi machimo.
Mulungu adachita zodabwitsa zake, makolo ao akuwona, m'dziko la Ejipito, ku dera la Zowani. Adagaŵa nyanja pakati, kuti iwo apitepo, ndipo adaimiritsa madzi ngati makoma. Masana ankaŵatsogolera ndi mitambo, usiku ankaŵatsogolera ndi kuŵala kwamoto.
“Muzigwira ntchito pa masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, musagwire ntchito iliyonse, ngakhale pa nthaŵi yolima kapena yokolola.
Mudzaitane amuna onse, akazi, ana ndi alendo amene ali m'mizinda mwanu, kuti aliyense adzimvere yekha, ndipo aphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumamvera mau ake mosamala.
Muzilemekeza masiku anga a Sabata ngati opatulika, kuti adzakhale ngati chizindikiro pakati pa Ine ndi inu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wanu.’
Yesu adapita ku Kapernao, mudzi wina wa ku Galileya, nkumaphunzitsa pa tsiku la Sabata. Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankalankhula moonetsa ulamuliro ngati mwiniwake.
Atafika ku dera lakwao, adayamba kuphunzitsa anthu m'nyumba yao yamapemphero. Amene ankamumva ankadabwa nkumati, “Kodi Iyeyu, nzeru zimenezi ndi mphamvuzi adazitenga kuti?
Tsono Paulo adaloŵa nawo monga adaazoloŵera, ndipo adakambirana nawo za m'Malembo pa masabata atatu.
Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana.
“Muzibzala mbeu zaka zisanu ndi chimodzi m'munda mwanu, ndi kumakolola mbeuzo. Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.
Anthu anu adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthaŵi yaitali. Adzamanganso pa maziko akalekale. Apo mudzatchedwa anthu okonza makoma, omanganso nyumba zamabwinja, kuti anthu azikhalamo.”
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.
Kumbukirani kuti ndine Chauta, amene ndidakupatsani tsiku la Sabata. Tsono chifukwa cha chimenechi ndimakupatsani chakudya chokwanira masiku aŵiri pa tsiku lachisanu ndi chimodzi. Aliyense azingokhala komwe aliriko pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Asachoke ndi mmodzi yemwe pakhomo pake.”
Pemphererani mtendere wa Yerusalemu ponena kuti, “Anthu amene amakukonda iwe Yerusalemu, zinthu ziziŵayendera bwino. Mtendere ukhale m'kati mwa makoma ako, bata likhale m'nyumba zako zachifumu.” Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga ndidzanena kuti, “Mtendere ukhaledi m'kati mwako.” Chifukwa cha Nyumba ya Chauta, Mulungu wathu, ndidzakupemphera zabwino.
Wina aliyense asakuzengeni mlandu pa nkhani yokhudza zakudya kapena zakumwa, kapena pa zokhudza masiku a chikondwerero, kapena a mwezi wokhala chatsopano, kapena pa zokhudza tsiku la Sabata.
Yesu adaŵayankha kuti, “Nanga bwanji inuyo, chifukwa choumirira miyambo yanu, mumaphwanya lamulo la Mulungu?
Mukamakolola dzinthu m'minda mwanu, zina pang'ono nkuiŵalika, musabwerere kukatenga zoiŵalikazo. Zimenezo muzisiyire alendo okhala nanu, ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.
Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera.
Paja Chauta akuti, “Ofulidwa amene amalemekeza masiku a Sabata, amene amachita zokomera Ine, ndi kusunga chipangano changa mokhulupirika, Ineyo ndidzaŵapatsa dzina ndi mbiri yabwino pakati pa anthu anga, m'kati mwa fuko langa, koposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi. Ndidzaŵapatsa mbiri yabwino yosatha, yosaiŵalika.”
Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
Ena amaganiza kuti tsiku lakutilakuti ndi loposa masiku ena, koma pamene ena akuganiza kuti masiku onse nchimodzimodzi. Aliyense achite monga momwe watsimikizira kwenikweni mumtima mwake. Amene amasunga tsiku lakutilakuti, amatero kuti alemekeze Ambuye. Amene amadya chilichonse, amatero kuti alemekeze Ambuye, pakuti amayamika Mulungu chifukwa cha chakudyacho. Amene amasala zina, amatero kuti alemekeze Ambuye, ndipo amayamika Mulungu pakutero.
Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.
Linali tsiku la chikonzero, tsiku la Sabata likuti liziyamba kumene. Azimai aja amene adaabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, adatsatira Yosefe, naona manda ndi m'mene adaaikira mtembo wa Yesu. Kenaka adabwerera nakayamba kukonza zonunkhira ndiponso mafuta abwino. Tsono pa tsiku la Sabata adapumula malinga ndi Malamulo a Mose.
Pa tsiku la Sabata lililonse iye ankakambirana ndi anthu ku nyumba yamapemphero ya Ayuda, namayesetsa kukopa Ayuda ndi Agriki omwe.
Pajatu chilichonse chimene Mulungu adalenga nchabwino, palibe chilichonse choti munthu asale, akamachilandira moyamika Mulungu, pakuti chimayeretsedwa ndi mau a Mulungu ndi mapemphero aja.
“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse. Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.
Mose adaitana Aisraele onse naŵauza kuti, “Chauta akukulamulani kuti, “Anthu onse aluso pakati panupa abwere, ndipo apange zonse zimene Chauta adalamula. Apange chihema cha Chauta, hema lake pamodzi ndi chophimbira chake, ngoŵe zake zokoŵera, mafulemu ake, mitanda yake, nsanamira zake pamodzi ndi masinde ake omwe. Apangenso bokosi lachipangano ndi mphiko zake, chivundikiro chake cha bokosilo ndi nsalu zotchinga bokosilo; tebulo, pamodzi ndi mphiko zake ndi zipangizo zake, ndiponso buledi woperekedwa kosalekeza kwa Mulungu; choikaponyale ndi zipangizo zake, nyale zake ndi mafuta a nyalezo; guwa lofukizirapo lubani ndi mphiko zake, mafuta odzozera, lubani wa fungo lonunkhira bwino, ndiponso nsalu zochingira za pa chipata cha chihema cha Chauta. Apangenso guwa la zopereka zopsereza pamodzi ndi chitsolo cha sefa yamkuŵa, mphiko zake ndi zipangizo zake zomwe, beseni losambira ndi phaka lake lomwe; nsalu zochinga bwalo, nsanamira pamodzi ndi masinde ake omwe, nsalu za pa chipata choloŵera ku bwalo, zikhomo zake pamodzi ndi zingwe za chihema cha Chauta ndi za bwalo lake; nsalu zokoma kwambiri zovala anthu otumikira m'malo opatulika, ndiponso zovala zopatulika za wansembe Aroni ndi za ana ake, akamatumikira ngati ansembe.” Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri, lidzakhala la Sabata, tsiku lanu lopumula, loperekedwa kwa Chauta. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo, adzaphedwa. Tsono Aisraele onse aja adachoka ndi kumsiya Mose. Ndipo munthu aliyense, monga momwe mtima wake unkafunira, adabwera kwa Chauta ndi zopereka zopangira chihema chamsonkhano cha Chauta. Adabwera nazo zonse zogwiritsira ntchito potumikira, ndi zonse zopangira zovala zopatulika. Kudabwera amuna ndi akazi omwe. Munthu aliyense malinga ndi kufuna kwake adabwera ndi zokometsera zomangira zovala, nsapule zakukhutu, mphete, ukufu wam'khosi, ndi zokometsera zina zagolide. Munthu aliyense adabwera ndi zagolide zimene adazipatula kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta. Munthu aliyense amene anali ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, bafuta wa thonje losalala kwambiri, nsalu za ubweya wambuzi, zikopa zankhosa zonyika mu utoto wofiira, ndi zikopa zambuzi, adabwera nazo kwa Chauta. Aliyense adabwera ndi zimene anali nazo. Anthu onse amene anali ndi siliva kapena mkuŵa, zonsezo adabwera nazo kwa Chauta. Onse amene anali ndi matabwa a mtengo wa kasiya wogwiritsira ntchito pomangapo, adabwera nawo ndithu. Akazi onse aluso adaomba nsalu za thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira. Adabweranso ndi bafuta wa thonje losalala kwambiri. Akazi onse alusowo adaombanso nsalu za ubweya wambuzi. Ndipo atsogoleri adabwera ndi miyala ya onikisi ndi miyala ina yoika pa chovala cha efodi ndiponso pa chovala chapachifuwa. Adaperekanso zonunkhira, mafuta anyale, mafuta odzozera ndiponso lubani wa fungo lokoma. Motero Aisraele onse, amuna ndi akazi omwe, amene adafuna ndi mtima wao wonse kupereka zao ku ntchito zimene Chauta adalamula kudzera mwa Mose, adabwera ndi zopereka zao kwa Chauta. Pa tsiku la Sabata limenelo, musamasonkha ndi moto womwe m'nyumba mwanu.”
Koma Yesu adati, “Iyai, odala ndi anthu amene amamva mau a Mulungu naŵagwiritsa ntchito.”
Munthu wina wachinyamata adadza kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndizichita chabwino chanji kuti ndikalandire moyo wosatha?” Yesu adamuyankha kuti, “Bwanji ukundifunsa za chimene chili chabwino? Wabwino ndi Mmodzi yekha. Ngati ufuna kukaloŵa ku moyo, uzimvera Malamulo.” Iye adati, “Malamulo ake oti?” Yesu adayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Anthu ambirimbiri adamtsata, ndipo Iye ankachiritsa odwala kumeneko. Munthu uja adati, “Malamulo onseŵa ndakhala ndikuŵatsata, nanga chanditsaliranso nchiyani?” Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Koma pamene munthu uja adamva mau ameneŵa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa anali wolemera kwambiri.
Pamene ankatuluka, anthu aja adapempha Paulo ndi Barnabasi kuti adzaŵakambirenso zomwezi tsiku la Sabata linalo. Anthu osonkhana aja atamwazikana, Ayuda ambiri, ndiponso anthu a mitundu ina otembenuka nkumatsata zachiyuda, adatsatira Paulo ndi Barnabasi. Aŵiriŵa adalankhula ndi anthu aja, naŵapempha kuti alimbikire kutsata zimene Mulungu adaŵachitira mwa kukoma mtima kwake. Pa tsiku la Sabata linalo pafupi anthu onse amumzindamo adasonkhana kuti amve mau a Ambuye.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka. Aliyense wotumikira Khristu motere, amakondweretsa Mulungu, ndipo amakhala wovomerezeka kwa anthu.
“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.
Yesu adabwereranso ku Galileya ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mbiri yake idawanda kuzungulira dziko lonselo. Ankaphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, ndipo anthu onse ankamutamanda.
Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Tsono Yesu popitiriza mau, adauza Afarisiwo kuti, “Mulungu adaika tsiku la Sabata kuti likhale lothandiza anthu. Sadalenge anthu kuti akhale akapolo a tsiku la Sabata ai.
Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako.
pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku lalikulu la Sabata, lopumula, tsiku la msonkhano wopatulika. Musamagwira ntchito iliyonse. Limenelo likhale tsiku la Sabata la Chauta kulikonse kumene mukakhale.’
Mulungu adadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, naliyeretsa, chifukwa choti pa tsiku limenelo adapuma atatsiriza zonse zimene ankachita.
Ndidaŵapatsanso masiku a Sabata kuti akhale ngati chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziŵe kuti Ine Chauta ndimaŵayeretsa.
Chauta akunena kuti, “Muzidziletsa kuchita zanuzanu pa Sabata, osagwira ntchito zanu pa tsiku langa loyera. Tsiku la Sabatali muzilitcha kuti chinthu chosangalatsa, tsiku loyera la Chauta muzilitcha kuti chinthu cholemekezeka. Muzililemekeza pakusayendayenda, poleka kugwira ntchito zanu ndiponso posakamba nkhani zachabe.
Chimenechi ndi chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi Aisraele, chakuti Ine Chauta ndidalenga kumwamba ndi dziko lapansi pa masiku asanu ndi limodzi, ndipo ndidapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.’ ”
Tsono Mose adaŵauza kuti, “Chauta walamula kuti, ‘Maŵa ndi tsiku lopumula, tsiku la Sabata, loperekedwa kwa Chauta. Wotchani yense amene mufuna kuwotcha, ndipo muphike yense amene mufuna kuphika. Wotsalako mumsunge padera mpaka maŵa.’ ”
Pamene Aisraele anali m'chipululu muja, adapeza munthu akutola nkhuni pa tsiku la Sabata. Amene adapeza munthuyo akutola nkhuni, adabwera naye kwa Mose ndi Aroni ndi kwa mpingo wonse. Iwo adamponya m'ndende chifukwa choti sankadziŵa bwino zoti amchite. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Munthuyo aphedwe. Mpingo wonse umponye miyala kunja kwa mahema.” Pomwepo mpingo udamtulutsira kunja kwa mahema munthuyo ndi kumupha pomponya miyala, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.