Kwa zaka zambiri, ife okhulupirira mwa Khristu, monga Ayuda akale, takhulupirira kuti Kumwamba ndi komwe kuli Mulungu. Mawu ake amatiuza zimenezi mobwerezabwereza. Yehova anati: “Thambo ndilo mpando wanga wachifumu, ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Ndi nyumba yotani imene mungamangire Ine? Ndipo malo anga opumulirapo ndi ati?” (Yesaya 66:1).
Ngakhale m’Chipangano Chatsopano, pamene Stefano anakamulika miyala chifukwa cholalikira uthenga wabwino, maso ake anatseguka, wodzala ndi Mzimu Woyera, anayang’ana Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu ataima pa dzanja lamanja la Mulungu (Machitidwe 7:54-55).
Mzimu Woyera wakhala akutitsogolera ife okhulupirira kuti tiyang'anire Kumwamba, monga mtumwi Paulo anatilimbikitsira: “Ganizirani za kumwamba, osati za padziko lapansi” (Akolose 3:2).
Kuyamba kale, monga m’nkhani ya Nowa ndi chingalawa, taphunzira kufunika koyang’anira Kumwamba. Timakumbutsidwanso kuti monga okhulupirira mwa Khristu, tili ndi nzika ziwiri: ya padziko lapansi ndi yakumwamba. Timalimbikitsidwa kusungira chuma chathu Kumwamba, komwe njenjete ndi dzimbiri sizingawononge, ndi komwe akuba sangaboore ndi kuba, monga Yesu anatiphunzitsa mu Uthenga Wabwino wa Mateyu (6:19-20).
Ndikofunika kudzifunsa kuti, kodi ndikuganizira za Kumwamba? Kodi ndikusungira chuma changa kumeneko? Kodi ndikudziwa kuti ndine nzika yakumwamba? Tiyeni titsatire mawu a wamasalmo akuti: “Ndani amene ndili naye Kumwamba koma Inu nokha? Ndipo palibe chilichonse chimene ndichikonda padziko lapansi koposa Inu.” (Masalmo 73:25).
“Chauta akuti, ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Kapena malo opumuliramo Inewo ngotani?
Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba.
Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.”
Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu, thambo limasonyeza ntchito za manja ake.
Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide, ngakhale golide wambiri wamtengowapatali, nzotsekemera kupambana uchi, ngakhale uchi wozuna kwambiri.
Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu.
Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake? Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika.
Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Usana umasimbira zimenezo usana unzake, usiku umadziŵitsa zimenezo usiku unzake.
Monsemo Abrahamu ankadikira mzinda wa maziko okhazikika. Mzindawo, Mmisiri woganiziratu mamangidwe ake ndiponso woumanga, ndi Mulungu.
Nanga ndili ndi yani kumwamba kupatula Inu? Pansi pano palibe kanthu kena kamene ndimafuna, koma Inu nokha.
Pamenepo mudatsekuka m'Nyumba ya Mulungu Kumwamba, ndipo bokosi lachipangano lidaoneka m'Nyumbamo. Kenaka kudachita mphezi, phokoso, mabingu ndi chivomezi, ndipo kudagwa matalala akuluakulu.
M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo.
Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu.
“Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”
Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?”
Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.
Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma.
“Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu.
Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine.
Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire.
Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.
M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo.
Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.
Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake.
Palibe munthu amene adakwera kupita Kumwamba, koma Mwana wa Munthu ndiye adatsika kuchokera Kumwamba.
Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso.
Pamenepo mngelo uja adandinyamula chamumzimu nakanditula pa phiri lalikulu ndi lalitali. Adandiwonetsa Mzinda Woyera uja, Yerusalemu, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu.
Unkaŵala ndi ulemerero wa Mulungu. Kuŵala kwake kunali ngati kuŵala kwa mwala wamtengowapatali, ngati mwala wambee, wonyezimira ngati galasi.
Mzindawo unali ndi linga lalikulu ndi lalitali. Lingalo linali ndi zipata khumi ndi ziŵiri, pazipatapo panali angelo khumi ndi aŵiri, ndipo pa zitseko zake padaalembedwa maina a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.
Pa mbali zonse zinai za mzindawo panali zipata zitatuzitatu: kuvuma zitatu, kumwera zitatu, kumpoto zitatu, kuzambwe zitatu.
Linga la mzindawo lidaamangidwa pa maziko khumi ndi aŵiri, ndipo pamazikopo padaalembedwa maina a atumwi khumi ndi aŵiri a Mwanawankhosa uja.
Mngelo amene ankalankhula naneyo anali ndi ndodo yoyesera yagolide, yoti ayesere mzinda uja, zipata zake ndi linga lake.
Mzindawo unali wolingana ponseponse, m'litali mwake ndi m'mimba mwake munali chimodzimodzi. Mngelo uja adayesa chozungulira mzindawo ndi ndodo yake ija, napeza kuti kutalika kwake kunali makilomita 2,200. M'litali mwake, m'mimba mwake ndi msinkhu wake, zonse zinali zolingana.
Kenaka adayesa linga la mzindawo, napeza kuti msinkhu wake unali mamita 65. Mngeloyo ankayesa ndi muyeso womwe anthu amagwiritsa ntchito.
Linga la mzindawo linali la miyala yambee, ndipo mzinda weniweniwo unali wa golide wangwiro, woŵala ngati galasi.
Maziko aja omwe linga la mzindawo lidaamangidwapo, adaaŵakongoletsa ndi miyala yamitundumitundu yamtengowapatali. Maziko oyamba anali a mwala wambee; achiŵiri anali a mwala wabuluu ngati thambo; achitatu anali a mwala wotuŵira; achinai anali a mwala wobiriŵira;
Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake.
achisanu anali a mwala mwina mofiira mwina mwabrauni; achisanu ndi chimodzi anali a mwala wofiira; achisanu ndi chiŵiri anali a mwala wachikasu; achisanu ndi chitatu anali a mwala wobiriŵira modera; achisanu ndi chinai anali a mwala wakadzira; achikhumi anali a mwala wachisipu; achikhumi ndi chimodzi anali a mwala wabuluu ngati changululu; achikhumi ndi chiŵiri anali a mwala wofiirira.
Zitseko za pa zipata khumi ndi ziŵiri zija zinali za miyala yamtengowapatali kwambiri. Chitseko chilichonse chinali cha mwala umodzi wa mtundu womwewo. Ndipo mseu wamumzindamo unali wa golide wangwiro, woonekera mpaka pansi, ngati galasi.
Sindidaonenso Nyumba ya Mulungu mumzindamo, pakuti Nyumba yake ndi Ambuye Mulungu, Mphambe, mwini wake, ndiponso Mwanawankhosa uja.
Palibe chifukwa choti dzuŵa kapena mwezi ziziŵala pamzindapo, pakuti ulemerero wa Mulungu ndiwo umaŵalapo, ndipo nyale yake ndi Mwanawankhosa uja.
Anthu a mitundu yonse adzayenda m'kuŵala kwake kwa mzindawo, ndipo mafumu a pa dziko lonse lapansi adzabwera ndi ulemerero wao m'menemo.
Zitseko za pa zipata zake zidzakhala zosatseka tsiku lonse, chifukwa kumeneko kudzakhala kulibe usiku.
Ndipo m'menemo adzabwera ndi ulemerero wa anthu a mitundu yonse, pamodzi ndi chuma chao.
Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo.
Ndidamva mau amphamvu ochokera ku mpando wachifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao.
Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
Koma potsata lonjezo la Mulungu, tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, m'mene chilungamo chizidzakhalamo.
“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.
Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
Imvani pemphero lopemba la mtumiki wanu ndiponso la anthu anu Aisraele, pamene akupemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mukhululuke.
Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso.
Koma monga zilirimu tikuwona kuti ankafuna dziko lina, lokoma kopambana, ndiye kuti dziko la Kumwamba. Nchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wao, popeza kuti Iye adaŵakonzera mzinda.
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye.
M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye.
Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai.
Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.
Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Pambuyo pake mngelo uja adandiwonetsa mtsinje wa madzi opatsa moyo. Mtsinjewo madzi ake anali onyezimira ngati galasi, ndipo unkachokera ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja.
Adandiwuzanso kuti, “Usabise mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo, pakuti nthaŵi yake ili pafupi.
Wochita zoipa apitirire kuchita zoipazo, ndipo wodetsedwa ndi zonyansa apitirire kudzidetsa ndi zonyansazo. Wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo, ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.”
Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense molingana ndi zimene adachita.
Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimalizo ndine.”
Ngodala amene amachapa mikanjo yao, kuti aloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyo, ndiponso kuloŵa mu mzinda kudzera pa zipata zija.
Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.
“Ine, Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti akufotokozereni zimenezi ndipo zithandize mipingo. Ine ndine chiphukira chotuluka mwa mfumu Davide, ndine chidzukulu chake. Ndine Nthanda, nyenyezi yoŵala m'mamaŵa!”
Mzimu Woyera ndi Mkwati wamkazi akuti, “Bwerani!” Aliyense womva mauŵa, anenenso kuti, “Bwerani!” Aliyense womva ludzu, abwere. Aliyense woŵafuna, aŵalandire mwaulere madzi opatsa moyo.
Ine Yohane, ndikuchenjeza aliyense womva mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo. Wina akadzaonjezerapo kanthu pa mau ameneŵa, Mulungu adzamuwonjezera miliri ija yalembedwa m'buku munoyi.
Ndipo wina akadzachotsapo kanthu pa mau a m'buku lino loneneratu zam'tsogolo, Mulungu adzamchotsera gawo lake la zipatso za mtengo wopatsa moyo uja, ndi malo ake omwe mu Mzinda Woyera uja, monga zalembedwera m'buku muno.
Unkayenda pakati pa mseu wamumzinda uja. Pa mbali zonse ziŵiri za mtsinje panali mtengo wopatsa moyo. Mtengowo umabala zipatso khumi ndi kaŵiri pa chaka, kamodzi mwezi uliwonse, ndipo masamba ake ndi ochiritsa anthu a mitundu yonse.
Amene akufotokoza zimenezi akuti, “Indedi, ndikubwera posachedwa.” Inde, bwerani, Ambuye Yesu.
Ambuye Yesu akukomereni mtima nonse.
Mumzindamo simudzapezekanso kanthu kalikonse kotembereredwa ndi Mulungu. Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja udzakhala m'menemo, ndipo atumiki ake adzampembedza.
Iwo azidzaona nkhope yake, ndipo dzina lake lidzakhala lolembedwa pamphumi pao.
Sikudzakhalanso usiku, ndipo sipadzafunikanso kuŵala kwa nyale kapena kuŵala kwa dzuŵa, pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuŵala kwake, ndipo iwo adzakhala mafumu olamulira mpaka muyaya.
Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba.
Chauta akunena kuti, “Ndikulenga thambo lam'mwamba latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zakale sadzazikumbukiranso, zidzaiŵalika kotheratu.
Palibe chifukwa choti dzuŵa kapena mwezi ziziŵala pamzindapo, pakuti ulemerero wa Mulungu ndiwo umaŵalapo, ndipo nyale yake ndi Mwanawankhosa uja.
Koma Chauta ali m'Nyumba yake yoyera, Chauta mpando wake waufumu uli kumwamba. Maso ake amapenya anthu onse ndi kuŵayesa.
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba.
Ngodala anthu amene adzauke nao pa kuuka koyamba kumeneku. Ameneŵa ndiwo akeake a Mulungu. Imfa yachiŵiri ilibe mphamvu pa iwo, koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Yesu Khristu, ndipo azidzalamulira pamodzi naye zaka chikwi chimodzi.
Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m'maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta.
Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.
Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo.
“Monga momwe dziko lapansi latsopano ndi dziko lakumwamba latsopano, zimene ndidzapange, zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, chonchonso zidzukulu zanu ndi dzina lanu zidzakhala mpaka muyaya.
Tsono Iyeyo ngati Mfumu adzauza a ku dzanja lamanjawo kuti, ‘Bwerani kuno inu odalitsidwa a Atate anga. Loŵani mu ufumu umene adakukonzerani chilengedwere dziko lapansi.
Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ndiponso ku mzinda wa Mulungu wamoyo, ndiye kuti Yerusalemu wa Kumwamba, m'mene muli angelo osaŵerengeka.
Mwafika kuchikondwerero kumene kwasonkhana ana oyamba a Mulungu, amene maina ao adalembedwa Kumwamba. Mwafika kwa Mulungu, mweruzi wa anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama, amene Mulungu waŵasandutsa angwiro kwenikweni.
Zoonadi, mwaisandutsa yodala kopambana mpaka muyaya. Mwaisangalatsa ndi chimwemwe, chifukwa muli nayo.
Popeza kuti tili mwa Khristu Yesu, Mulungu adachita ngati kutiwukitsa kwa akufa pamodzi naye, kuti choncho atipatse malo aulemu pamodzi naye m'dziko la Kumwamba.
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake.
Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Amene adzapambane, ndidzamsandutsa mzati wokhazikika m'Nyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso, ndipo pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga, ndi la mzinda wa Mulungu wanga. Mzindawo ndi Yerusalemu watsopano, wotsika Kumwamba kuchokera kwa Mulungu wanga. Pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano.
“Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake.
Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga.
Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
Iwowo amakondwa masiku onse chifukwa cha Inu, ndipo amatamanda kulungama kwanu.
Tsono anthu olungama adzaŵala ngati dzuŵa mu Ufumu wa Atate ao. Amene ali ndi makutu, amve!
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni.
Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano.
Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa.
Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai.
Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu.
Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu.
Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri.
Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo.
Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo.
Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi.
Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
“Nchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndipo amampembedza m'Nyumba mwake usana ndi usiku. Wokhala pa mpando wachifumu uja adzakhala ngati hema lao loŵateteza.
Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Sadzaombedwanso ndi dzuŵa kapena kusauka ndi kutentha.
Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzaŵapukuta misozi yonse m'maso.”
Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake.
Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta Wamphamvuzonse. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.
Pakuti iye ndi amene adaika dziko lapansi pa nyanja yaikulu, adalikhazika pa mitsinje yozama.
Adatinso, “Ndithu ndikunenetsa kuti mudzaona Kumwamba kutatsekuka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”
Gwero la zonsezi ndi chiyembekezo chimene muli nacho chodzalandira zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Mudamva za zimenezi pamene mau oona, adakufikani poyamba paja. Mau oonawo ndi Uthenga Wabwino.
Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko, ndikagona m'dziko la anthu akufa, Inu muli momwemo.
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”
Iye adayang'ana pansi ali m'malo ake oyera kumwamba, ali kumwambako, Chauta adayang'ana pa dziko lapansi,
Musandibisire nkhope yanu pa tsiku la mavuto anga. Tcherani khutu kuti mundimve, mundiyankhe msanga pa tsiku limene ndikukuitanani.
kuti amve kubuula kwa anthu am'ndende, kuti aŵapulumutse amene adaayenera kuphedwa.
Munkasaukira limodzi ndi amene adaaponyedwa m'ndende, ndipo mudalola mokondwa kuti alande chuma chanu, mutadziŵa kuti muli ndi chuma choposa ndi chosatha.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma kuli mtsinje umene mifuleni yake imasangalatsa anthu amumzinda wa Mulungu, malo oyera okhalako Wopambanazonse.
Ndipo adalota akuwona makwerero ochoka pansi mpaka kukafika kumwamba. Angelo a Mulungu ankatsika ndi kumakwera pa makwererowo.
Abale, chimene ndikunena nchakuti munthu ndi thupi lake lamnofuli sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimaola, sizingathe kuloŵa kumene zinthu siziwola.
Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya.
Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe.
Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.
Kunena za oyera mtima amene ali pansi pano, ameneŵa ndi olemekezeka, ndipo ndimakondwera nawo.
Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
Mulungu adzambatuke, adani ake amwazikane. Onse amene amamuda, athaŵe pamaso pake.
Anthu anu adapezamo malo okhala. Inu Mulungu, mudapatsa anthu osauka zosoŵa zao mwa ubwino wanu.
Ambuye apereka lamulo. Nchachikulu chiŵerengero cha amene abwera ndi uthenga wakuti,
“Mafumu a magulu a ankhondo akuthaŵa, indedi akuthaŵa. Tsono azimai ku mudzi akugaŵana zofunkha, ngakhale atsalira pakati pa makola ankhosa.
“Zofunkhazo zikuwoneka ngati mapiko a nkhunda okutidwa ndi siliva, nthenga zake nzokutidwa ndi golide wonyezemira.”
Pamene Mphambe adabalalitsa mafumu kumeneko, ku Zalimoni kudagwa chisanu choopsa.
Iwe phiri la Basani, phiri laulemerero, Iwe phiri la Basani, phiri la nsonga zambiri!
Iwe phiri la nsonga zambiriwe, chifukwa chiyani ukuliyang'ana mwansanje phiri limene Mulungu adasankha kuti azikhalapo? Ndithu Chauta adzakhalapo mpaka muyaya.
Ambuye adafika ku malo ao oyera kuchokera ku Sinai, ali ndi magaleta amphamvu zikwi zambirimbiri.
Inu mudakwera kumwamba, mutatenga am'ndende ambiri, ndipo mudalandira mphatso kwa anthu, ngakhale kwa anthu oukira, kuti mudzakhale kumeneko, Inu Chauta Mulungu.
Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.
Amwazeni iwowo monga m'mene mphepo imachitira utsi. Anthu oipa aonongeke pamaso pa Mulungu, monga m'mene sera amasungunukira pa moto.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba.
Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Koma Mulungu adzaombola moyo wanga ku ulamuliro wa manda, sindidzaopa, pakuti Iye adzandilandira.
“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba.
“Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao.
Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba.
Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa.
ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza.
Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,”
ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse.
Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.
Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere.
Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa.
Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani?
Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga.
Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga.
Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.
Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse.
Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa?
Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.”
Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Ndi waukulu ubwino wanu umene mwaŵasungira anthu okumverani, umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, aliyense waona zimenezi.
Tsono mwana iwe, udzatchedwa mneneri wa Mulungu Wopambanazonse, chifukwa udzatsogola pamaso pa Ambuye, kuti ukonzeretu njira zao.
Udzadziŵitsa anthu ao kuti Mulungu adzaŵapulumutsa pakuŵakhululukira machimo ao.
Mulungu wathu ndi wa chifundo chachikulu, adzatitumizira kuŵala kwa dzuŵa lam'maŵa kuchokera Kumwamba.
Kuŵala kwake kudzaunikira onse okhala mu mdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”
Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka.
Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m'mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.
Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Linga la mzindawo linali la miyala yambee, ndipo mzinda weniweniwo unali wa golide wangwiro, woŵala ngati galasi.
Maziko aja omwe linga la mzindawo lidaamangidwapo, adaaŵakongoletsa ndi miyala yamitundumitundu yamtengowapatali. Maziko oyamba anali a mwala wambee; achiŵiri anali a mwala wabuluu ngati thambo; achitatu anali a mwala wotuŵira; achinai anali a mwala wobiriŵira;
Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake.
achisanu anali a mwala mwina mofiira mwina mwabrauni; achisanu ndi chimodzi anali a mwala wofiira; achisanu ndi chiŵiri anali a mwala wachikasu; achisanu ndi chitatu anali a mwala wobiriŵira modera; achisanu ndi chinai anali a mwala wakadzira; achikhumi anali a mwala wachisipu; achikhumi ndi chimodzi anali a mwala wabuluu ngati changululu; achikhumi ndi chiŵiri anali a mwala wofiirira.
Zitseko za pa zipata khumi ndi ziŵiri zija zinali za miyala yamtengowapatali kwambiri. Chitseko chilichonse chinali cha mwala umodzi wa mtundu womwewo. Ndipo mseu wamumzindamo unali wa golide wangwiro, woonekera mpaka pansi, ngati galasi.
Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga. Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?
Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
“Atate, ndifuna kuti amene mudandipatsa, iwonso akhale pamodzi ndi Ine kumene ndili. Ndifuna kuti aone ulemerero wanga umene mudandipatsa, chifukwa mudandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake.
Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka.
Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.
Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha.
Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi.
Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho;
limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse,
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni.
Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu.
Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira,
imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota.