Pamene tikuganizira za Abrahamu pa phiri la Moriya ndi mwana wake Isake, tikuona chinthu champhamvu kwambiri. Isake anafunsa kuti nkhosa yoti iperekedwe nsembe ili kuti, ndipo Abrahamu anati, “Mulungu adzapeza nkhosa yoti iperekedwe nsembe mwana wanga.” (Genesis 22:8). Kodi simukuganiza kuti izi n’zolimbikitsa? Mulungu amadzipereka yekha.
Kenako, pamene Abrahamu anali pafupi kupereka nsembe mwana wake, Yehova analankhula naye ndipo anapereka nkhosa yamphongo m’malo mwa Isake. Abrahamu anatsegula maso ake, ndipo anaona nkhosa yamphongo itagwidwa mu chitsamba ndi nyanga zake. Anaitenga ndipo anaipereka nsembe m’malo mwa mwana wake. (Genesis 22:13) Ngakhale Abrahamu ananena za nkhosa, Mulungu anapereka nkhosa yamphongo. Koma nkhosa imene Abrahamu anayembekezera inabwera patatha zaka 2,000, yobweretsedwa ndi Yohane M’batizi ku mtsinje wa Yorodani.
Khristu ndiye Mwanawankhosa wathu wa Pasika, Mwanawankhosa wathu wamuyaya. Yohane, mtumwi, anaona masomphenya odabwitsa m’buku la Chivumbulutso 5:12. Anaona angelo, zamoyo, akulu ndi mamiliyoni ambirimbiri “akunena mokweza kuti: ‘Mwanawankhosa amene anaphedwa ndiye woyenera kutenga mphamvu, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu, ulemerero ndi kutamandidwa.’” Ngakhale kumwamba, Khristu wathu akuimiridwa ndi Mwanawankhosa. Magazi ake ndi amphamvu! Khulupirirani iye.
Tili otetezeka m’magazi ake. Ngakhale zinthu zoopsa zikuchitika padziko lapansi, sizingatikwanire chifukwa cha magazi abwino kuposa a ana a nkhosa a Israyeli ku Igupto. Yesu ndiye Pasika wathu. Kodi simukuganiza kuti izi n’zodabwitsa?
Tsono adaŵauza kuti, “Ndafunitsitsa kudya phwando ili la Paska pamodzi ndi inu ndisanayambe kumva zoŵaŵa.
Pamene Yesu anali m'Yerusalemu pa chikondwerero cha Paska, anthu ambiri adayamba kuika chikhulupiriro chao pa Iye, poona zozizwitsa zimene ankachita.
Itayandikira nthaŵi ya Paska, chikondwerero cha Ayuda, Yesu adanyamuka kupita ku Yerusalemu.
Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Paska.
Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziŵiri, iwo adapita kumeneko monga adaazoloŵera.
Kudangotsala masiku aŵiri kuti chifike chikondwerero cha Paska ndi chikondwerero cha masiku odya buledi wosafufumitsa. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti amgwirire Yesu mochenjera, nkumupha.
Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe kuti akapereke Yesu kwa iwo.
Pamene iwo adamva zimenezi adakondwa, ndipo adamlonjeza kuti adzampatsa ndalama. Iyeyo tsono adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo.
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”
Yesu adatuma aŵiri mwa ophunzira ake, naŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu. Mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire.
Kunyumba kumene ati akaloŵe, mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda cha alendo choti Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’
Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.”
Ophunzira aja adanyamuka naloŵa mumzindamo. Adachipezadi monga momwe Yesu adaaŵauzira, ndipo adakonza za phwando la Paska.
Kutada, Yesu adabwera ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja.
Onse atakhala pansi nkumadya, Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu, mnzanga wodya nane, andipereka kwa adani anga.”
Ophunzirawo adamva chisoni, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti, “Monga nkukhala ine?”
Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.”
Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito.
“Pa tsiku la khumi ndi chinai la mwezi woyamba, muzichita chikondwerero cha Paska, chikondwerero chake cha masiku asanu ndi aŵiri. Masiku amenewo muzidya buledi wosatupitsa.
Pamene Aisraele anali m'zithando ku Giligala m'chigwa cha ku Yeriko, adachita Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo.
Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa, tsono onsewo anali oyeradi. Choncho adapha mwanawankhosa wa Paska, kuphera onse amene adatuluka ku ukapolo, ansembe anzao ndi eniakewo.
Chauta adalankhula kwa Mose ndi Aroni m'dziko lija la Ejipito kuti,
Musasiyeko nyama ina mpaka m'maŵa, motero ina ikatsalako, muitenthe.
Kudya kwake, muzikadya motere: Mudzavale zaulendo, nsapato zanu zili kuphazi, ndodo zili kumanja. Mudzadye mofulumira. Limeneli ndilo tsiku la Paska ya Chauta.
Usiku umenewo, Ine ndidzapita m'dziko la Ejipito ndipo m'dziko lonselo ndidzapha ana onse oyamba kubadwa, a anthu ndi a nyama omwe. Ndidzalanga milungu yonse ya Ejipito. Ine ndine Chauta.
Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito.
“Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.”
Tsono Chauta adati, “Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba muzidzachotsa zotupitsira buledi m'nyumba zanu zonse, chifukwa pa masiku asanu ndi aŵiri aliyense wodya buledi wofufumitsa adzachotsedwa pakati pa Aisraele.
Pa tsiku loyamba, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, muzidzachita msonkhano wachipembedzo. Musadzagwire ntchito pa masiku amenewo, koma chakudya chokha choti aliyense adye, mudzatha kukonza.
Chikondwerero chimenechi cha buledi wosafufumitsa, mudzachisunge ndithu, chifukwa pa tsiku limeneli mpamene ndidzatulutse magulu anu onse kuchoka m'dziko la Ejipito. Tsono muzidzasunga tsiku limeneli pa mibadwo yanu yonse, ngati lamulo lamuyaya.
Muzidzadya buledi wosafufumitsa kuyambira madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba, mpaka madzulo a tsiku la 21 mwezi womwewo.
Pa masiku asanu ndi aŵiri onsewo, m'nyumba mwanu musadzapezeke chofufumitsira buledi, chifukwa wina aliyense akadzadya chakudya chofufumitsa, adzachotsedwa pa mtundu wa Aisraele, mlendo ngakhale mbadwa yomwe.
“Mwezi uno udzakhala mwezi wanu woyambira chaka.
“Musapereke buledi wofufumitsa pamene mukupereka kwa Ine magazi a nsembe yanga. Nyama iliyonse yophera nsembe ya Paska, musaisunge mpaka m'maŵa.
Paska yotereyi inali isanachitikepo kuyambira nthaŵi ya aweruzi amene ankatsogolera Aisraele, kapena nthaŵi ya mafumu a ku Israele, kapenanso nthaŵi ya mafumu a ku Yuda.
Mlendo akakhala pakati panu, nafuna kuchita nao Paska ya Chauta, nayenso achite Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake. Kaya ndinu alendo kapena ndinu mbadwa, nonse mukhale ndi lamulo limodzi lokha.”
Mwanawankhosa wake adzakhale wopanda chilema, wamphongo, wa chaka chimodzi. Mungathe kusankhulanso mwanawambuzi.
Chikondwerero cha Paska chija chinkayandikira. Choncho anthu ambiri ochokera ku midzi adapita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa kudziyeretsa, Paska isanayambe.
Tsono adzatengeko magazi a nyamayo ndi kuwaza pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, ndi pamwamba pa chitseko cha nyumba m'mene akadyeremo nyamayo.
Yesu atatsiriza kulankhula nkhani zonsezi, adauza ophunzira ake kuti,
Yesu podziŵa zimene iwo aja ankalankhula, adaŵafunsa kuti, “Mukumuvutiranji maiyu? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri.
Anthu osauka muli nawo nthaŵi zonse, koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse.
Iyeyu wathira mafuta ameneŵa pa thupi langa kuti alidzozeretu lisanaikidwe m'manda.
Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwinowu pa dziko lonse lapansi, azikafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.”
Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe.
Adakaŵafunsa kuti, “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikadzampereka Yesuyu kwa inu?” Iwo adamupatsa ndalama zasiliva makumi atatu.
Tsono kuyambira pomwepo iye adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo.
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, ophunzira aja adadza nafunsa Yesu kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”
Iye adaŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu kwa munthu wina wake. Mukanene kuti, ‘Aphunzitsi akuti nthaŵi yao ili pafupi, akudzadyera kwanu kuno phwando la Paska pamodzi ndi ophunzira ao.’ ”
Ophunzira aja adapita nakachita zomwe Yesu adaaŵauza, nakakonzadi za phwando la Paska.
“Pajatu chikondwerero cha Paska chiyambika patangopita masiku aŵiri, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti akapachikidwe pa mtanda.”
Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja.
Tsono Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Malamulo ake a Paska ndi aŵa: Mlendo aliyense asadyeko.
Kapolo aliyense wochita kugulidwa angadyeko, koma atayamba waumbalidwa.
Mlendo kapena wantchito wanu aliyense asadyeko.
Muzidyera m'nyumba imodzi, musatuluke nayo panja nyamayo, ndipo musaphwanye mafupa ake.
Nyamayo adzaiwotche usiku womwewo, ndipo adzaidye ndi buledi wosafufumitsa ndiponso ndi ndiwo zoŵaŵa zamasamba.
Usiku umenewo, Ine ndidzapita m'dziko la Ejipito ndipo m'dziko lonselo ndidzapha ana onse oyamba kubadwa, a anthu ndi a nyama omwe. Ndidzalanga milungu yonse ya Ejipito. Ine ndine Chauta.
Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito.
“Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.”
Tsono Chauta adati, “Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba muzidzachotsa zotupitsira buledi m'nyumba zanu zonse, chifukwa pa masiku asanu ndi aŵiri aliyense wodya buledi wofufumitsa adzachotsedwa pakati pa Aisraele.
Chikondwerero chimenechi cha buledi wosafufumitsa, mudzachisunge ndithu, chifukwa pa tsiku limeneli mpamene ndidzatulutse magulu anu onse kuchoka m'dziko la Ejipito. Tsono muzidzasunga tsiku limeneli pa mibadwo yanu yonse, ngati lamulo lamuyaya.
Ndipo Mose adaitana atsogoleri onse a Aisraele, naŵauza kuti, “Pitani kasankhuleni mwanawankhosa woyenera pa banja lililonse, ndipo muphe nyama ya Paskayo.
Mutenge nthambi ya kachitsamba ka hisope, muiviike m'magazi amene mwaŵathira m'mbale. Tsono muwaze magaziwo pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo ndi pamwamba pa chitseko. Wina aliyense asatuluke m'nyumba mwake mpaka m'maŵa.
Chauta adzapita m'dziko lonse la Ejipito, ndi kumapha Aejipito. Azidzati akaona magaziwo pamwamba pa chitseko ndi pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, azidzapitirira khomolo ndipo sadzamulola mngelo wake woononga kuti aloŵe m'nyumba mwanu kuti akupheni.
Ana anu azidzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’
Pamenepo inu muzidzayankha kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Chauta, chifukwa chakuti adapitirira nyumba za Aisraele ku Ejipito; pamene ankapha Aejipito, nyumba zathu adazisiya.’ ” Atamva zimenezi, anthu adaŵerama pansi, napembedza.
Tsono Mose adauza anthu kuti, “Muzikumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito, ku dziko laukapolo, chifukwa Chauta adakutulutsani kumeneko ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye chilichonse chofufumitsa.
“Aisraele azichita Paska pa nthaŵi yake.
Nthaŵi zina mtambowo unkaphimba masiku oŵerengeka, ndipo Aisraele ankakhalabe m'mahema potsata malamulo a Chauta. Tsono ankanyamuka ulendo Chauta akaŵalamula.
Nthaŵi zina mtambowo unkangophimba chihemacho kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. M'maŵa mwake mtambowo ukachoka, iwo ankanyamuka ulendo wao. Mwina mtambowo unkaphimba chihema chija tsiku lonse ndi usiku womwe, koma ukangochokapo, iwowo ankanyamuka ulendo wao.
Ngakhale mtambowo uphimbe pamwamba pa chihema cha Mulungu nkumakhala pomwepo masiku aŵiri kapena mwezi, kapena chaka, kapena nthaŵi yopitirirapo, Aisraele ankakhalabe m'mahema, ndipo sankanyamuka. Koma mtambowo ukangochokapo, iwo ankanyamuka ulendo.
Aisraele ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula, ndipo ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula. Ankasunga lamulo la Chauta, loŵafikira kudzera mwa Mose.
Muzichita Paska tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo ake. Muzichita Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake onse.”
Muzilemekeza Chauta, Mulungu wanu, pakuchita chikondwerero cha Paska pa mwezi wa Abibu. Chifukwa usiku wina mwezi umenewu, mpamene Chauta adakutulutsani ku Ejipito.
Tsono muchite chikondwerero cha kholola, cholemekeza Chauta, Mulungu wanu, pakumpatsa chopereka chaufulu, molingana ndi madalitso amene Iye wakupatsani.
Mukhale okondwa pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, inuyo pamodzi ndi mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mtumiki wamu wamwamuna, mdzakazi wanu, Alevi amene ali m'mizinda mwanu, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, amene amakhala nanu pamodzi m'mizinda mwanu. Zimenezi muzichitira pa malo opembedzerapo aja.
Kumbukirani kuti mudaali akapolo ku Ejipito. Motero malamulo ameneŵa muziŵasungadi mosamala.
Mutatuta tirigu wanu yense, ndiponso mutafinya mphesa zanu, muzidzachita chikondwerero cha misasa masiku asanu ndi aŵiri.
Musangalale pa chikondwererocho, inuyo pamodzi ndi mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mtumiki wanu wamwamuna, mdzakazi wanu, Alevi amene ali m'mizinda mwanu, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, amene amakhala nanu m'mizinda mwanu.
Muzidzatamanda Chauta, Mulungu wanu, pochita chikondwerero chimenechi masiku asanu ndi aŵiri, pa malo amene Iye adzasankhule, chifukwa chakuti Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atadalitsa kholola lanu ndi ntchito zanu zonse, kuti chimwemwe chanu chikhale chodzaza ndithu.
Anthu aamuna onse a mtundu wanu azidzabwera kudzapembedza Chauta, Mulungu wanu, ku malo achipembedzo, katatu pa chaka. Azidzafika pa nthaŵi ya Paska, pa nthaŵi ya chikondwerero cha kholola ndiponso pa nthaŵi ya chikondwerero cha misasa.
Ndipo pobwera pamaso pa Chauta, asamadzakhale chimanjamanja, koma munthu aliyense azidzabwera ndi mphatso monga momwe angathere, molingana ndi madalitso amene Chauta, Mulungu wanu, adampatsa.
M'fuko lililonse mudzasankhe anthu oweruza ndiponso akuluakulu ena mu mzinda uliwonse umene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatseni. Anthu ameneŵa azidzaweruza anzao mosakondera.
Asadzachite zinthu mopanda chilungamo kapena kuweruza milandu mokondera. Asadzalandire chiphuphu, chifukwa ziphuphu zimadetsa m'maso ngakhale anthu anzeru ndipo zimalakwitsa anthu olungama poweruza.
Muzipereka nsembe za chikondwerero cha Paska kwa Chauta, Mulungu wanu. Muphe nkhosa kapena ng'ombe pa malo amene Chauta adzasankhule kuti anthu azidzapembedzerapo.
Nyama ya nsembeyo musadye ndi buledi wotupitsa. Pa masiku asanu ndi aŵiri, muzidya nyamayo ndi buledi wosatupitsa ndiye kuti buledi wamazunzo, pakuti mudatuluka ku Ejipito mothaŵa. Motero masiku onse a moyo wanu, mudzakumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito.
Pa masiku asanu ndi aŵiri munthu wina aliyense asadzasunge chofufumitsira buledi m'nyumba mwake m'dziko mwanumo. Nyama imene idaphedwa madzulo pa tsiku loyamba, muzidzaidya kusanache.
Musapereke nsembe ya Paska kulikonse ku dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.
Muziphera pa malo amodzi opembedzerapo aja. Muzichita zimenezi poloŵa dzuŵa, ndiye kuti nthaŵi yomwe ija imene mudachoka ku Ejipito.
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, ophunzira aja adadza nafunsa Yesu kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”
Iye adaŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu kwa munthu wina wake. Mukanene kuti, ‘Aphunzitsi akuti nthaŵi yao ili pafupi, akudzadyera kwanu kuno phwando la Paska pamodzi ndi ophunzira ao.’ ”
Ophunzira aja adapita nakachita zomwe Yesu adaaŵauza, nakakonzadi za phwando la Paska.
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”
Yesu adatuma aŵiri mwa ophunzira ake, naŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu. Mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire.
Kunyumba kumene ati akaloŵe, mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda cha alendo choti Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’
Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.”
Ophunzira aja adanyamuka naloŵa mumzindamo. Adachipezadi monga momwe Yesu adaaŵauzira, ndipo adakonza za phwando la Paska.
Itayandikira nthaŵi ya Paska, chikondwerero cha Ayuda, Yesu adanyamuka kupita ku Yerusalemu.
Kumeneko adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu napezamo anthu akugulitsa ng'ombe, nkhosa ndi nkhunda. Munalinso anthu osinthitsa ndalama.
Atatsala masiku asanu ndi limodzi kuti chifike chikondwerero cha Paska, Yesu adadza ku Betaniya, kumene kunali Lazaro uja amene Iye adamuukitsa kwa akufa.
Ndipo ataona kuti zimenezi zidakondweretsa Ayuda, adapitiriza ndithu nkugwiranso Petro. Zimenezi zidachitika pa masiku a Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa.
Muchotse chofufumitsira chakalechi cha uchimo, kuti mukhale oyera mtima ndithu, ngati buledi watsopano wosafufumitsa, monga momwe muliri ndithu, pakuti Khristu, Mwanawankhosa wathu wa Paska, adaphedwa kale ngati nsembe.
Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose.
Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu.
Pokhala ndi chikhulupiriro, adachita nawo chikondwerero cha Paska, nalamula kuti anthu awaze magazi pa zitseko kuti mngelo woononga ana achisamba uja asakhudze ana achisamba a Aisraele.
Tamandani Chauta! Mtamandeni, inu atumiki ake, tamandani dzina la Chauta.
Yamikani Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Pamene Israele adatuluka ku Ejipito, pamene banja la Yakobe lidatuluka kuchokera ku mtundu wa anthu a chilankhulo chachilendo,
Yuda adasanduka malo opatulika a Chauta, Aisraele adasanduka anthu a mu ufumu wake.
“Anthu adamsautsa ndi kumzunza, koma iye sadalankhule kanthu. Monga momwe amachitira mwanawankhosa wopita naye kuti akamuphe, ndiponso monga momwe nkhosa imakhalira duu poimeta, nayenso adangokhala chete.
Monga mbalame zouluka pamwamba pa zisa zake, Chauta Wamphamvuzonse adzatchinjiriza mzinda wa Yerusalemu. Adzauteteza ndi kuupulumutsa, adzausiya pambali ndi kuuwombola.”
Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, idyani, ili ndi thupi langa.”
Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu.
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, ili ndi thupi langa.”
Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu, nkuchipereka kwa ophunzirawo, naamwa onse.
Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka.
Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.”
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti aphere Yesu. Paja iwo ankaopa anthu.
Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira.
M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi.
Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai,
adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.
Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha.
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu.
Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe.
Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake.
Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika.
Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Paska, ndipo nkuti nthaŵi ili ngati 12 koloko masana. Pilato adauza Ayuda kuti, “Nayitu Mfumu yanu.”
Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m'nyumba imodzi.
Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.”
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Motero anthuwo adanyamula pa mapewa ao ufa wa buledi wokandiratu asanathire chofufumitsira, pamodzi ndi mbale zokandiramo buledi zili zokulunga m'nsalu.
Ndidzapambana adani anga ondizungulira, ndipo ndidzapereka nsembe m'Nyumba mwake ndili kufuula ndi chimwemwe. Ndidzaimba nyimbo yotamanda Chauta.
Kwezani mau kuimbira Mulungu amene ali mphamvu zathu. Fuulani ndi chimwemwe kwa Mulungu wa Yakobe.
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani m'dziko la Ejipito. Yasamani kukamwa, Ine ndidzakudyetsani.
“Koma anthu anga sadamvere mau anga. Israele adandinyoza.
Choncho ndidaŵasiya ndi mitima yao yosamverayo, kuti atsate zimene ankafuna.
“Anthu anga akadandimvera, Aisraele akadayenda m'njira zanga,
bwenzi posachedwa nditagonjetsa adani ao, ndipo dzanja langa likadakantha amaliwongo ao.
“Anthu amene amadana ndi Chauta, akadakhwinyata pamaso pake, ndipo tsoka lao likadakhala mpaka muyaya.
Ndikadakudyetsani ndi ufa wosalala watirigu, ndipo ndikadakukhutitsani ndi uchi wam'thanthwe.”
Yambani nyimbo, imbani ng'oma, pamodzi ndi pangwe wolira bwino ndi zeze.
Imbani lipenga mwezi ukaoneka chatsopano, ukaoneka kwathunthu, pa tsiku lathu lachikondwerero.
Pakuti ndilo lamulo lokhalira Israele, lochokera kwa Mulungu wa Yakobe,
Mverani nyimbo m'mahema mwa anthu a Mulungu, nyimbo zokondwerera kupambana, zakuti, “Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,
dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”
“Muzichita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa monga ndidakulamulirani. Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, chifukwa ndi mwezi umenewu pamene inu mudachokako ku Ejipito kuja.
“Tsiku la 14 la mwezi woyamba, ndi la Paska ya Chauta.
Ndipo pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, ndi tsiku lachikondwerero. Azidya buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri.
Pa tsiku loyamba pazikhala msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito yotopetsa,
Tsono pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, muzidzanena kuti, “Kholo langa linali Lachiaramu, munthu wongoyendayenda, amene adapita ku Ejipito ndi banja lake nakakhala kumeneko. Popita kumeneko, anthuwo adaali ochepa, koma pambuyo pake adachuluka nasanduka mtundu waukulu ndi wamphamvu.
Aejipito adatichita zankhanza ndi kutizunza potigwiritsa ntchito mwaukapolo.
Pamenepo ife tidalirira Chauta, Mulungu wa makolo athu, kuti atithandize. Iyeyo adatimva, ndipo adaona kusauka kwathu, ntchito yolemetsa imene iwo aja ankatigwiritsa, ndiponso moyo wathu wopsinjidwawo.
Mwa mphamvu zake zazikulu ndiponso ndi dzanja lake lotambalitsa, Chauta adatitulutsa ku Ejipito. Padaoneka zozizwitsa ndi zizindikiro, ndipo padachitika zinthu zoopsa zambiri.
Potsiriza adatifikitsa kuno, natipatsa dziko lino, dziko lamwanaalirenji.
Kenaka Chauta adaŵatulutsa Aisraele atatenga siliva ndi golide, pakati pa mafuko awo panalibe amene adafooka.
ntchito zodabwitsa m'dziko la Hamulo, ndiponso zinthu zoopsa ku Nyanja Yofiira kuja.
Nchifukwa chake adaŵauza kuti akadaŵaononga, pakadapanda Mose wosankhidwa wake kuima pamaso pake, ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usaŵaononge.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse.
Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Inetu zimene ndidalandira kwa Ambuye ndi zimene nanenso ndidazipereka kwa inu, zakuti usiku umene adaperekedwa uja, Ambuye Yesu adaatenga mkate.
Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.”
Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.”
Pakuti nthaŵi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye, mpaka adzabwerenso.
Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Atatero Yesu adatenga chikho, ndipo atathokoza Mulungu, adati, “Kwayani, imwani nonsenu.
Ndithu ndikunenetsa kuti kuyambira tsopano sindidzamwanso konse chakumwa cha mtengo wamphesa, mpaka Mulungu atadzakhazikitsa ufumu wake.”
“Mukamapereka magazi a nyama ngati nsembe kwa Ine, musapereke pamodzi ndi buledi wofufumitsa, ndipo mafuta a nyama yopereka pa tsiku langa lachikondwerero asakhale mpaka m'maŵa.
Ndidzambwezera chiyani Chauta pa zabwino zonse zimene adandichitira?
Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.
“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni.
Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.
Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Yesuyo adaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha zochimwa zathu, ndipo adauka kwa akufa kuti tipezeke olungama pamaso pa Mulungu.
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Ngwodala amene alikudza m'dzina la Chauta. Tikufunirani madalitso ochokera m'nyumba ya Chauta.
Chauta, Mpulumutsi ndi Woyera uja wa Israele, akulankhula ndi wonyozedwa kwambiri uja, wodedwa ndi mitundu ina ya anthu, kapolo wa mafumu ankhanza. Akunena kuti, “Mafumu adzaimirira mwaulemu poona iwe, akalonga nawonso adzadziponya pansi chafufumimba. Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Chauta, amene ali wokhulupirika, Woyera uja wa Israele, amene adakusankhula.”
Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m'mene Iye amadziŵiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya?
Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, chifukwa tonse timagaŵana mkate umodzi womwewo.
Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona.
Adati, “Ndi yodala Mfumu imene ilikudza m'dzina la Ambuye. Mtendere Kumwamba, ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.”
Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika.
Manda adatsekuka ndipo anthu a Mulungu ambiri amene anali atamwalira kale, adauka kwa akufa.
Adatuluka m'manda, ndipo Yesu atauka kwa akufa, iwo adaloŵa mu Yerusalemu, Mzinda Wopatulika, anthu ambiri nkumaŵaona.
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Chauta adzapita m'dziko lonse la Ejipito, ndi kumapha Aejipito. Azidzati akaona magaziwo pamwamba pa chitseko ndi pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, azidzapitirira khomolo ndipo sadzamulola mngelo wake woononga kuti aloŵe m'nyumba mwanu kuti akupheni.
“Koma perekani nsembe zanu zothokozera kwa Mulungu, ndipo muchite zimene mudalumbira kwa Wopambanazonse.
“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.
Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.
Abrahamu adamuyankha kuti, “Mwana wanga, Mulungu akatipatsa mwanawankhosayo.” Choncho onse aŵiri adapitiriza ulendo wao limodzi.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina.
Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha.
Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta.
Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”
Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.”
Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu.
Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale.
Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale.
Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja adabwera mbandakucha pa tsiku lotsatira Sabatalo, kudzaona manda aja.
Apo Yesu adaŵauza kuti, “Musaope. Pitani, kauzeni abale anga kuti apite ku Galileya. Akandiwonera kumeneko.”