Chifundo cha Mulungu n’chachulukitsitsa, mpaka chingati chiposa moyo weniweniwo. Tangoganizani, moyo wanga ukanakhala wopanda phindu ndikanapanda kuona chikondi cha Mulungu m’mawa uliwonse. Amandikonda kwambiri moti sanandisiye ngakhale ndili ndi zolakwa zambiri.
Ndani angapeze mtendere ngati chifundo cha Mulungu sichingawonekere pa moyo wake? Ine sindingathe kuganiza wina aliyense. Munthu wopanda Mulungu ali ngati chotengera chopanda kanthu, wodzala ndi uchimo ndipo ali mu dziko lachitayiko.
Koma Mulungu atandiwonetsa kukoma mtima kwake, ndimazindikira zonse zomwe amandithandiza kuyambira ndikadzuka mpaka ndikagona. Ndikamaganizira zoyipa zomwe ndimachita ndi kuipa kwanga, mtima wanga umakhudzidwa kwambiri moti ndimayamba kuthokoza Mulungu nthawi zonse.
Kungoti ndikupumirabe ndi chizindikiro cha chifundo cha Mulungu pa ine. Wandikhululukira, wanditsuka uchimo wanga, ndipo wanatenga chilango chomwe ndinayenera kulandira. Chifukwa cha ichi, ndiyenera kuthokoza. Tsegulani pakamwa panu, muthokoze Mulungu. Wakhalandi wabwino, wakuganizirani, wakuonani ndi maso achikondi, ndipo sanakanepo chifundo chake chachikulu, chifundo chomwe sichingathe kutha.
Yamikirani lero ndi nthawi zonse chikondi chachikulu cha Yesu kwa inu, yamikirani magazi ake amtengo wapatali, ndipo mulowe mu chikondi Chake.
Pajatu Iye adaauza Mose kuti, “Ndidzachitira chifundo amene ndifuna kumchitira chifundo, ndidzamvera chisoni amene ndifuna kumumvera chisoni.”
Motero chachikulu si zimene munthu azifuna, kapena zimene munthu amayesetsa kuchita, koma chachikulu ndi chifundo cha Mulungu.
Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika.
Chauta ndi wabwino kwa onse, amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.
Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya.
Adani a mitundu yonse adandizinga, koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta.
Adandizinga, inde adandizinga pa mbali zonse, koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta.
Adandizinga ngati njuchi, koma adatha msanga ngati moto wapaminga. Ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta.
Adandikankha kwambiri, kotero kuti ndinali pafupi kugwa, koma Chauta adandithandiza.
Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga. Ndiye mpulumutsi wanga.
Mverani nyimbo m'mahema mwa anthu a Mulungu, nyimbo zokondwerera kupambana, zakuti, “Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,
dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”
Sindidzafa, ndidzakhala moyo, ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.
Chauta wandilanga koopsa, koma sadandisiye kuti ndife.
Tsekulireni zipata za Nyumba ya Mulungu, kuti ndifike ku malo ake achilungamo, ndikathokoze Chauta.
Aisraele anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.”
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu ndi chikondi chanu chosasinthika, chifukwa mudaziwonetsa kuyambira kalekale.
Musakumbukire machimo a unyamata wanga ndi mphulupulu zanga. Koma mundikomere mtima, Inu Chauta, chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.
Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu.
Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Kamvetsetseni tanthauzo la mau a Mulungu aja akuti, ‘Ndimafuna chifundo, osati nsembe ai.’ Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa.”
Mulungu adasandutsa anthu onse akaidi a kusamvera, kuti Iye athe kuchitira onse chifundo.
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.
Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.
“Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona.
Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’
Iwe Israele, khulupirira Chauta. Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.
Adzaombola Israele ku machimo ake onse.
Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Mundiyankhe, Inu Chauta, pakuti chikondi chanu chosasinthika nchabwino. Munditchere khutu chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.
Kodi sunayenera kuti iwenso umchitire chifundo wantchito mnzako, monga ndinakuchitira iwe chifundo?’
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.
Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera.
Pamenepo ochimwa ndidzaŵaphunzitsa njira zanu, ndipo iwo adzabwerera kwa Inu.
Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu.
Ambuye, tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu.
Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani. Ndikadapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo.
Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza.
Muŵachitire zabwino anthu a ku Ziyoni, chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Mumangenso kachiŵiri makoma a Yerusalemu.
Pamenepo mudzakondwera ndi nsembe zoyenera, nsembe zootcha ndi zopsereza kwathunthu. Choncho adzapereka ng'ombe zamphongo pa guwa lanu lansembe.
Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga, mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Koma pamenepo Mulungu Mpulumutsi wathu adaonetsa kukoma kwake ndiponso chifundo chokonda anthu.
Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake afafanizidwa.
Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika.
Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.
Ngwodala amene Chauta samuŵerengera mlandu wake, amene mumtima mwake mulibe zonyenga.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Chifundo chanu nchachikulu, Inu Chauta, mundipatse moyo molingana ndi chilungamo chanu.
Tamandani Chauta. Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Apo Davide adauza Gadi kuti, “Iyai, ine pamenepa ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka tigwe m'manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu. Koma chonde, tisagwe m'manja mwa anthu ai.”
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Komabe pakuti Mulungu ngwachifundo, adaŵakhululukira machimo ao, ndipo sadaŵaononge. Kaŵirikaŵiri ankadziletsa kukwiya, sadalole kuti mkwiyo wake wonse uyake.
Ndichitireni chifundo, Inu Chauta, chifukwa chakuti ndine wofooka. Limbitseni, Inu Chauta, chifukwa m'nkhongono mwanga mwaweyeseka.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu.
Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje.
Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye?
Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Kale simunali anthu a Mulungu, koma tsopano ndinu anthu ake. Kale simudaalandira chifundo, koma tsopano mwachilandira.
Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.
hokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Adapha ana achisamba a ku Ejipito, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Ndipo adatulutsa Aisraele pakati pao, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambalitsa, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Adagaŵa pakati Nyanja Yofiira, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Adaolotsa Aisraele pakati pake, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Koma adamiza Farao ndi ankhondo ake m'Nyanja Yofiira, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Adatsogolera anthu ake m'chipululu, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Adapha mafumu amphamvu, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Adaphanso mafumu otchuka, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Adapha Sihoni, mfumu ya Aamori, pakuti chikondi chake nchamuyaya,
Thokozani Mulungu wa milungu, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Adapha Ogi, mfumu ya ku Basani, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Napereka dziko la mafumuwo kuti likhale choloŵa, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Choloŵa cha Israele mtumiki wake, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Adatikumbukira pamene adani adatigonjetsa, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Ndipo adatipulumutsa kwa adani athu, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Amapatsa zamoyo zonse chakudya, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Thokozani Mulungu wakumwamba, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Thokozani Chauta woposa ambuye onse, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?”
Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.
Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”
Mudzadzuka nkuchitira chifundo mzinda wa Ziyoni, zoonadi, nthaŵi yake youkomera mtima yafika.
Koma Mulungu adandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwa koposane, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse. Adafuna kuti ndikhale chitsanzo cha kuŵalezera mtima onse amene adzamkhulupirire kuti alandire moyo wosatha.
Maziko a ufumu wanu ndiwo kulungama ndi kuweruza mosakondera. Mumaonetsa chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika pa zonse zimene mumachita.
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
ndiponso pakupatsa anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Nchifukwa chake ndidzakuyamikani pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
Tithandizeni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, kuti dzina lanu likhale ndi ulemerero. Tipulumutseni, ndipo mutikhululukire zochimwa zathu, kuti dzina lanu lilemekezeke.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse ine mtumiki wanu, monga momwe mudalonjezera.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang'ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’ ”
Sadzamva njala kapena ludzu. Mphepo yotentha kapena dzuŵa sizidzaŵapsereza, chifukwa amene amaŵachitira chifundo adzaŵatsogolera ndi kuŵaperekeza ku akasupe a madzi.
Lolani kuti m'maŵa ndimve za chikondi chanu chosasinthika, chifukwa ndimakhulupirira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo, pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu.
Motero chachikulu si zimene munthu azifuna, kapena zimene munthu amayesetsa kuchita, koma chachikulu ndi chifundo cha Mulungu.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta.
Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
pakuti chikondi chanu chosasinthika nchachikulu, chofika mpaka mlengalenga, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake.
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Nchifukwa chake adaayenera kusanduka wofanafana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe onse wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, ndipo kuti pakutero achotse machimo a anthu.
Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.
Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana.
Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.
Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wachifundo. Sadzakulekererani kapena kukuwonongani. Chipangano chimene Iye adachita molumbira ndi makolo anu, sadzachiiŵala.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka.
Koma Chauta anali naye Yosefe, namkomera mtima kwambiri, kotero kuti wosunga ndende adakondwera naye Yosefe.
Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.
Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha.
M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.
Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse.
Motero bwererani nonsenu ndi chithandizo cha Mulungu wanu. Mukhale achikondi ndi olungama, ndipo muzidalira Mulungu wanu nthaŵi zonse.
Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga. Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse.
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu ndi chikondi chanu chosasinthika, chifukwa mudaziwonetsa kuyambira kalekale.
“Kwa anthu okhulupirika, Inu Mulungu mumadziwonetsa okhulupirika, kwa anthu aungwiro mumadziwonetsa abwino kotheratu.
Chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika zidzakumana. Chilungamo ndi mtendere zidzagwirizana.