Ndikufuna ndikuuzani nkhani ya ulemu kwa makolo athu. Nthawi zina timavutika kumvetsa tanthauzo lenileni la ulemu umenewu. Koma Mulungu, m’mawu ake opatulika, amatiuza kuti tiyenera kulemekeza ndi kuwayamikira makolo athu, mosasamala kanthu za msinkhu wawo kapena momwe amatikhalira.
Kulemekeza makolo athu ndi chizindikiro cha chikondi, ndipo chimabweretsa madalitso ambiri m'miyoyo yathu. Sikuti timachita izi chifukwa cha momwe makolo athu alili, koma chifukwa chomvera malamulo a Ambuye. Sikuti timayesa kuwerengera momwe tiyenera kuwachitira, koma timayesetsa kuwachitira ulemu tsiku ndi tsiku, kuti tikhalitse ndi moyo wautali komanso kuti tione chisomo ndi chikondi cha Mulungu m'miyoyo yathu.
Mulungu amatiuza kuti tilemekeze makolo athu. Kulemekeza kumeneku kumaphatikizapo kuwamvera, kutsatira uphungu wawo wanzeru, kuwamvetsera mwatcheru, ndi kulemekeza ulamuliro wawo. Baibulo limatipatsa malangizo omveka bwino okhudza momwe tiyenera kuchitira makolo athu. Musaiwale zimenezi!
“Uzilemekeza atate ako ndi amai ako, monga momwe Chauta, Mulungu wako, adakulamulira, kuti pakutero masiku a moyo wako achuluke ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa iwe.
Malamulo ukuŵadziŵa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.”
Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’
“Muzikhala mwaulemu pamaso pa munthu waimvi. Wokalamba muzimchitira ulemu, ndipo pakutero mudzaopa Mulungu wanu. Ine ndine Chauta.
Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa.
“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.
Munthu aliyense wotemberera bambo wake ndi mai wake ayenera kuphedwa. Munthu ameneyo watemberera bambo wake ndi mai wake, tsono magazi ake akhale pa iyeyo.
Amene amachita ndeu ndi atate ake ndi kupirikitsa amai ake, ameneyo ndi mwana wochititsa manyazi ndiponso wonyozetsa.
Aliyense mwa inu aziwopa mai wake ndi bambo wake. Muzisunga masiku anga a Sabata, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.
Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.
Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu.
Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.
Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima.
Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo.
Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira.
Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye.
Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima.
Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro.
Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse.
Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”
Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake.
Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.
Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa.
Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.
Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona.
Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako.
Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako.
Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira. Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda. Pamene ukudzuka, zidzakulangiza.
Wina akatemberera bambo wake kapena mai wake, moyo wake udzatha ngati nyale yozima mu mdima wandiweyani.
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.
Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake.
Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo.
Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’
Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni, ndazipereka kwa Mulungu,” ameneyo sasoŵanso kulemekeza atate ake.’
Pakutero, chifukwa cha mwambo wanuwo, mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe.
Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankaŵamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake.
Paja Mose adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’
Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.
Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe, adakhazikitsa malamulo ake mu Israele. Adalamula makolo athu kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo.
Adalola kukwiya, osadziletsa, sadaŵapulumutse ku imfa, koma adapereka moyo wao ku miliri.
Adapha ana achisamba onse a Aejipito, ana oyamba a mphamvu zao, m'zithando za zidzukulu za Hamu.
Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa, naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta.
Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao.
Adaŵafikitsa ku dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene adaŵagonjetsera ndi dzanja lake lamphamvu.
Adapirikitsa mitundu ina ya anthu, kuŵachotsa m'njira. Adagaŵagaŵa dziko la anthuwo kuti likhale la anthu ake, adakhazikitsa mafuko a Israele m'midzi ya anthuwo.
Komabe Aisraele adamuputa ndi kumuukira Mulungu Wopambanazonse, sadasunge malamulo ake,
koma iwo adakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo ao. Adapotoka ngati uta wosakhulupirika.
Iwo adakwiyitsa Mulungu ndi akachisi ao opembedzerako mafano ku mapiri. Adamupsetsa mtima chifukwa cha mafano ao osemawo.
Pamene Mulungu adamva zimenezi, adakwiya kwambiri, ndipo adakana Aisraele kotheratu.
Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe, udzaŵadziŵa, ndipo nawonso udzafotokozera ana ake.
Adasiya malo ake a Silo kumene ankakhala, adasiya hema limene ankakhalamo pakati pa anthu,
ndipo adalola adani athu kuti alande Bokosi la Chipangano chake, limene linali chizindikiro cha mphamvu zake ndi ulemerero wake.
Chifukwa adakwiyira anthu ake, adalola kuti anthu akewo aphedwe pa nkhondo.
Nkhondo yoyaka ngati moto idaononga anyamata ao, ndipo atsikana ao adasoŵa oŵaimbira nyimbo zaukwati.
Ansembe ao omwe adaphedwa ndi lupanga, ndipo akazi ao amasiye sadaŵalole kulira maliro.
Pomaliza Ambuye adachita ngati kudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuula chifukwa choledzera.
Tsono Mulungu adaŵapirikitsa adani ake, naŵachititsa manyazi anthaŵizonse.
Adakana banja la Yosefe, sadasankhule fuko la Efuremu.
Koma adasankhula fuko la Yuda, ndiponso phiri la Ziyoni limene amalikonda.
Adamanga malo ake opatulika ngati malo ake akumwamba, okhazikika ngati dziko lapansi mpaka muyaya.
Anawo aike chikhulupiriro chao pa Mulungu, ndipo asaiŵale ntchito za Mulungu, koma asunge malamulo ake.
Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu.
Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Tinali nawo azibambo athu apansipano amene ankatilanga, ndipo tinkaŵalemekeza. Kwenikweni tsono tikadayenera kugonjera Mulungu, Atate a mizimu, kuti tikhale ndi moyo.
Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu.
Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka.
Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama.
Ukamayenda, mapazi ako sazidzaombana. Ukamathamanga, sudzakhumudwa ai.
Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo.
Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa.
Njira zao uzipewe, usapitemo konse. Uzilambalale, ndi kungozipitirira.
Iwo ajatu sangagone, mpaka atachita ndithu choipa. Tulo sangatiwone, mpaka atakhumudwitsapo munthu.
Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao, kuchita ndeu ndiye chakumwa chao.
Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu.
Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani.
Ine ndikukupatsani malamulo abwino, musasiye zimene ndikukuphunzitsani.
Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo.
Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira.
Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye.
Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima.
Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro.
Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse.
Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”
Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake.
Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako.
Zoonadi, ndimo m'mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta.
kuti choncho athe kuphunzitsa azimai achitsikana kukonda amuna ao ndi ana ao.
Aŵaphunzitse kukhala a maganizo anzeru, opanda dama, osamala bwino zapabanja, ndi omvera amuna ao. Pamenepo anthu sanganyoze mau a Mulungu.
Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira.
Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera.
Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje.
Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Tiyese kuti wina ali ndi mwana wokanika ndiponso wachipongwe, mwana woti bambo ndi mai ake saŵamvera konse, ngakhale amlange chotani.
Makolo ake a mwanayo amgwire ndi kupita naye kwa akuluakulu amumzinda ku chipata cha mzindawo.
Akuluakulu anu ndi aweruzi anu apiteko, ndipo akayese kutalika kwake kuchokera pamalo pamene pali munthu wakufayo mpaka ku mizinda yoyandikana ndi malowo.
Makolowo auze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu ndi wokanika ndipo ndi wachipongwe safuna kutimvera, ndi wadyera ndiponso chidakwa.
Pamenepo anthu amumzindawo amuphe pakumponya miyala, motero mudzachotsa choipa pakati panu. Anthu onse a mu Israele muno akadzamva zimene zachitikazi, adzakhala ndi mantha.”
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake.
Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse.
Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.