Kale lomwe dziko lisanakhaleko, Mulungu anali atakukumbukira iwe. Anakukonzeratu moyo wako ndipo anaika mzimu wake mwa iwe kuti ukhale mwana wake.
Mulungu ndi Atate wabwino kwambiri, chikondi chake ndi choyera komanso chopanda malire, ndiye wabwino kuposa onse, amakukonda popanda chifukwa chilichonse.
Mwina unamvapo za Mulungu ndi mphamvu zake zazikulu, mwina mwa nkhani za anthu ena kapena mwa zimene waona mwa anthu, koma lero Mulungu akufuna kudziwitsa kwa iwe ngati Atate wako.
Mwina mpaka pano wamuwona ngati wochiritsa, woteteza kapena wopereka, koma tsopano akufuna kudzionetsa m'mtima mwako kuti umvetse kuti mwa iye uli ndi Atate wachikondi amene sadzakusiya, koma adzakhala nawe nthawi zonse.
Mulungu ndi Atate wathu Wakumwamba, wodzala ndi ubwino, chifundo ndi chikondi. Mulungu ndi wabwino! Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulumeka iye asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Mulungu anapereka mwana wake chifukwa cha chikondi, kusonyeza kufunika kwako kwa iye. Yandikirani kwa Mulungu tsiku lililonse, mudziwe ndipo sangalalani ndi chikondi chake ndi chipulumutso chimene wakupatsani.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Koma inu, zimene mudamva kuyambira pa chiyambi, zikhalebe m'mitima mwanu. Zimene mudamva kuyambira pa chiyambi zikakhalabe m'mitima mwanu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndi mwa Atate.
Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.
Pali Mulungu mmodzi amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Chonchonso Atate anu amene ali Kumwamba safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike.
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?
Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu.
M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo.
Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana.
Koma kwa ife, Mulungu ndi mmodzi yekha, ndiye Atate, amene adalenga zonse, ndipo moyo wathu umalinga kwa Iye. Tilinso ndi Ambuye amodzi okha, Yesu Khristu. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo ife tili ndi moyo chifukwa cha Iye.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Inu ndinu Atate athu ndithu, ngakhale Abrahamu satidziŵa, ngakhale Israele sakutivomera. Koma Inu, Chauta, ndinu Atate athu, ndinu Momboli wathu kuyambira kalekale.
“Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye.
Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse.
Amene adzapambane, ndidzamlola kukhala nane pamodzi pa mpando wanga wachifumu, monga momwe ndidachitira Ineyo: ndidapambana, ndipo ndikukhala pamodzi ndi Atate anga pa mpando wao wachifumu.
Atate anga amalemekezedwa pamene mubereka zipatso zambiri, ndipo pakutero mumaonetsa kuti ndinu ophunzira anga enieni.
Komabe Inu Chauta, ndinu Atate athu. Ife tili ngati mtapo, Inu muli ngati woumba. Mudatipanga tonse ndi manja anu.
“Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”
Adanenanso kuti, “Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m'chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu.
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.
Monga Atate amoyo adandituma, ndipo Ine ndili ndi moyo pokhala mwa Iwo, momwemonso aliyense wodya Ine, adzakhala ndi moyo pokhala mwa Ine.
“Atate, ndifuna kuti amene mudandipatsa, iwonso akhale pamodzi ndi Ine kumene ndili. Ndifuna kuti aone ulemerero wanga umene mudandipatsa, chifukwa mudandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Ndidachokeradi kwa Atate kudza pansi pano. Tsopano ndikuchokanso pansi pano kupita kwa Atate.”
Mphunzitsi wa Malamulo uja adati, “Ai, mwayankha bwino, Aphunzitsi. Monga mwaneneramo, nzoonadi kuti Mulungu ndi mmodzi yekhayo, ndipo palibe winanso koma Iye yekha.
Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.
Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.
Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira.
“Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.
Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Muzipirira masautso kuti muphunzirepo makhalidwe oyenera. Mulungu amakutengani ngati ana ake m'zochita zake zonse. Kodi nkale lonse analipo mwana amene bambo wake sadamlange? Ngati Mulungu sakulangani inuyo, monga amachitira ndi ana ake onse, ndiye kuti sindinu ana enieni, koma am'chigololo. Tinali nawo azibambo athu apansipano amene ankatilanga, ndipo tinkaŵalemekeza. Kwenikweni tsono tikadayenera kugonjera Mulungu, Atate a mizimu, kuti tikhale ndi moyo.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m'kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu.
Ndidzakhala Atate anu, inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi, akutero Ambuye Mphambe.”
“Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona.
Ndani mwa atatenu, mwana wake atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Kapena atampempha dzira, iye nkumupatsa chinkhanira? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene aŵapempha.”
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Chifukwa chotikonda, adakonzeratu kuti mwa Yesu Khristu atilandire ngati ana ake. Adachita zimenezi chifukwa adaafuna kutero mwa kukoma mtima kwake.
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse. Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu.
Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu. Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.
Yesu adamuyankha kuti, “Iwe Filipo, ndakhala nanu nthaŵi yonseyi, ndipo sunandidziŵebe? Amene waona Ine, waonanso Atate. Nanga bwanji ukuti, ‘Tiwonetseni Atate?’
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.