Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


55 Mau a M'Baibulo Okhudza Ulemu kwa Makolo

55 Mau a M'Baibulo Okhudza Ulemu kwa Makolo

Ndikufuna ndikuuzani nkhani ya ulemu kwa makolo athu. Nthawi zina timavutika kumvetsa tanthauzo lenileni la ulemu umenewu. Koma Mulungu, m’mawu ake opatulika, amatiuza kuti tiyenera kulemekeza ndi kuwayamikira makolo athu, mosasamala kanthu za msinkhu wawo kapena momwe amatikhalira.

Kulemekeza makolo athu ndi chizindikiro cha chikondi, ndipo chimabweretsa madalitso ambiri m'miyoyo yathu. Sikuti timachita izi chifukwa cha momwe makolo athu alili, koma chifukwa chomvera malamulo a Ambuye. Sikuti timayesa kuwerengera momwe tiyenera kuwachitira, koma timayesetsa kuwachitira ulemu tsiku ndi tsiku, kuti tikhalitse ndi moyo wautali komanso kuti tione chisomo ndi chikondi cha Mulungu m'miyoyo yathu.

Mulungu amatiuza kuti tilemekeze makolo athu. Kulemekeza kumeneku kumaphatikizapo kuwamvera, kutsatira uphungu wawo wanzeru, kuwamvetsera mwatcheru, ndi kulemekeza ulamuliro wawo. Baibulo limatipatsa malangizo omveka bwino okhudza momwe tiyenera kuchitira makolo athu. Musaiwale zimenezi!




Deuteronomo 5:16

“Uzilemekeza atate ako ndi amai ako, monga momwe Chauta, Mulungu wako, adakulamulira, kuti pakutero masiku a moyo wako achuluke ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:19

Malamulo ukuŵadziŵa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:22

Umvere atate ako amene adakubala, ndipo usamanyoza amai ako atakalamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:20

Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:1

Mwana wanzeru amamvera malangizo a atate ake, koma wonyoza samvetsera akamamdzudzula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4

Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:32

“Muzikhala mwaulemu pamaso pa munthu waimvi. Wokalamba muzimchitira ulemu, ndipo pakutero mudzaopa Mulungu wanu. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8

Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:12

“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:9

Munthu aliyense wotemberera bambo wake ndi mai wake ayenera kuphedwa. Munthu ameneyo watemberera bambo wake ndi mai wake, tsono magazi ake akhale pa iyeyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:26

Amene amachita ndeu ndi atate ake ndi kupirikitsa amai ake, ameneyo ndi mwana wochititsa manyazi ndiponso wonyozetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:3

Aliyense mwa inu aziwopa mai wake ndi bambo wake. Muzisunga masiku anga a Sabata, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:19

lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-3

Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:11-12

Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8-9

Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa. Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:20

Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:4

Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:20-22

Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako. Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako. Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira. Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda. Pamene ukudzuka, zidzakulangiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:20

Wina akatemberera bambo wake kapena mai wake, moyo wake udzatha ngati nyale yozima mu mdima wandiweyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:1

Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:17

“Munthu aliyense wotemberera bambo wake kapena mai wake, aphedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:20

Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:6

Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ulemerero wa ana ndi atate ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3-5

Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:17

Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4-6

Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’ Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni, ndazipereka kwa Mulungu,” ameneyo sasoŵanso kulemekeza atate ake.’ Pakutero, chifukwa cha mwambo wanuwo, mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:5

Chitsiru chimanyoza malangizo a bambo wake, koma wochenjera amamvera chidzudzulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:51

Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankaŵamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:10

Paja Mose adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:15

Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:5-7

Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe, adakhazikitsa malamulo ake mu Israele. Adalamula makolo athu kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo. Adalola kukwiya, osadziletsa, sadaŵapulumutse ku imfa, koma adapereka moyo wao ku miliri. Adapha ana achisamba onse a Aejipito, ana oyamba a mphamvu zao, m'zithando za zidzukulu za Hamu. Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa, naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta. Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao. Adaŵafikitsa ku dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene adaŵagonjetsera ndi dzanja lake lamphamvu. Adapirikitsa mitundu ina ya anthu, kuŵachotsa m'njira. Adagaŵagaŵa dziko la anthuwo kuti likhale la anthu ake, adakhazikitsa mafuko a Israele m'midzi ya anthuwo. Komabe Aisraele adamuputa ndi kumuukira Mulungu Wopambanazonse, sadasunge malamulo ake, koma iwo adakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo ao. Adapotoka ngati uta wosakhulupirika. Iwo adakwiyitsa Mulungu ndi akachisi ao opembedzerako mafano ku mapiri. Adamupsetsa mtima chifukwa cha mafano ao osemawo. Pamene Mulungu adamva zimenezi, adakwiya kwambiri, ndipo adakana Aisraele kotheratu. Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe, udzaŵadziŵa, ndipo nawonso udzafotokozera ana ake. Adasiya malo ake a Silo kumene ankakhala, adasiya hema limene ankakhalamo pakati pa anthu, ndipo adalola adani athu kuti alande Bokosi la Chipangano chake, limene linali chizindikiro cha mphamvu zake ndi ulemerero wake. Chifukwa adakwiyira anthu ake, adalola kuti anthu akewo aphedwe pa nkhondo. Nkhondo yoyaka ngati moto idaononga anyamata ao, ndipo atsikana ao adasoŵa oŵaimbira nyimbo zaukwati. Ansembe ao omwe adaphedwa ndi lupanga, ndipo akazi ao amasiye sadaŵalole kulira maliro. Pomaliza Ambuye adachita ngati kudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuula chifukwa choledzera. Tsono Mulungu adaŵapirikitsa adani ake, naŵachititsa manyazi anthaŵizonse. Adakana banja la Yosefe, sadasankhule fuko la Efuremu. Koma adasankhula fuko la Yuda, ndiponso phiri la Ziyoni limene amalikonda. Adamanga malo ake opatulika ngati malo ake akumwamba, okhazikika ngati dziko lapansi mpaka muyaya. Anawo aike chikhulupiriro chao pa Mulungu, ndipo asaiŵale ntchito za Mulungu, koma asunge malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:17

Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:8

Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:13

Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:9

Tinali nawo azibambo athu apansipano amene ankatilanga, ndipo tinkaŵalemekeza. Kwenikweni tsono tikadayenera kugonjera Mulungu, Atate a mizimu, kuti tikhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:1-2

Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu. Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama. Ukamayenda, mapazi ako sazidzaombana. Ukamathamanga, sudzakhumudwa ai. Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo. Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa. Njira zao uzipewe, usapitemo konse. Uzilambalale, ndi kungozipitirira. Iwo ajatu sangagone, mpaka atachita ndithu choipa. Tulo sangatiwone, mpaka atakhumudwitsapo munthu. Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao, kuchita ndeu ndiye chakumwa chao. Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu. Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani. Ine ndikukupatsani malamulo abwino, musasiye zimene ndikukuphunzitsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:2-3

Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:1-4

Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino. Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako. Zoonadi, ndimo m'mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:4-5

kuti choncho athe kuphunzitsa azimai achitsikana kukonda amuna ao ndi ana ao. Aŵaphunzitse kukhala a maganizo anzeru, opanda dama, osamala bwino zapabanja, ndi omvera amuna ao. Pamenepo anthu sanganyoze mau a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:4

Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu, koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:15

“Munthu aliyense amene amenya bambo wake kapena mai wake, aphedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:11

Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:9

Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:16

Mkazi wa mkhalidwe wabwino amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1-2

Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu. Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira. Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa. Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 21:18-21

Tiyese kuti wina ali ndi mwana wokanika ndiponso wachipongwe, mwana woti bambo ndi mai ake saŵamvera konse, ngakhale amlange chotani. Makolo ake a mwanayo amgwire ndi kupita naye kwa akuluakulu amumzinda ku chipata cha mzindawo. Akuluakulu anu ndi aweruzi anu apiteko, ndipo akayese kutalika kwake kuchokera pamalo pamene pali munthu wakufayo mpaka ku mizinda yoyandikana ndi malowo. Makolowo auze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu ndi wokanika ndipo ndi wachipongwe safuna kutimvera, ndi wadyera ndiponso chidakwa. Pamenepo anthu amumzindawo amuphe pakumponya miyala, motero mudzachotsa choipa pakati panu. Anthu onse a mu Israele muno akadzamva zimene zachitikazi, adzakhala ndi mantha.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13-14

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:27

Tsono leka zoipa, ndipo chita zabwino, motero udzakhala pa mtendere mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Akuchiritsa a mtima wachisoni, ndipo akumanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:1-2

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake. Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse. Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wakumwamba, ulemerero ndi ulemu zonse zikhale zako! Yesu wanga, ndikupempha undithandize kutsatira chitsanzo chako cha kumvera Atate, monga momwe iwe unachitira. Ndiphunzitseni kulemekeza ndi kuwachitira ulemu makolo anga, osawalankhula mwadyera kapena mwaukali. Ngati sindikuwalemekeza mwa kumvera, kukhala mwana wachikondi, kuwasamalira, ndi kuwateteza ngakhale atakalamba, andithandizeni. Mawu anu amati: “Lemekeza atate wako ndi amayi ako, monga momwe Yehova Mulungu wako anakulamulira, kuti masiku ako akhale ataliatali, ndi kuti zinthu zikuyendere bwino m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.” Ambuye Yesu, ndithandizeni kuyenda m’mawu anu ndikukhala ndi moyo molingana ndi lonjezo limeneli, chifukwa ndikudziwa kuti kumvera kudzabweretsa madalitso anga. M’dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa