Mukayandikira Atate, mukuyandikiranso Mwana, chifukwa onse ndi mmodzi. Kale, chifukwa cha zolakwa zathu, tinali kutali ndi Atate; mkhalowu unatilenga kutali ndi iye.
Koma chikondi chake ndi chachikulu, ndipo chifundo chake n’chosatha, moti sanafune kukhala kutali nanu, cholengedwa chake chamtengo wapatali. Chifukwa cha chikondi chake chopanda malire, anatuma Mwana wake yekha kuti adzafere inu; mwana wopanda chilema, wopanda tchimo, wangwiro.
Iye anachita izi kuti pasakhale cholepheretsa inu kukapembedza dzina lake. Kuti mukafike kwa Atate, muyenera kudzera mwa Yesu, kumuzindikira ngati Mpulumutsi wokha komanso wokwanira. Ndipo magazi ake adzakutsukani ku zoipa zanu, ndipo mudzakhala mwana wa Mulungu.
Palibe chifukwa choti musayandikire kwa iye; chophimba chachotsedwa, ndipo tsopano muli ndi ufulu wokhala osangalala ndikukonda Mlengi wanu. Musaiwale Yesu pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku, yamikirani nsembe yake ndipo muzimufunafuna ndi mtima wanu wonse.
Musakhale popanda chisomo chake, musachoke pafupi naye, musatembenukire chisomo chabwino chomuchitira ichi chomwe chabwera pa moyo wanu kuti mukakhale ndi moyo. Koposa zonse, kondani Mulungu ndi mtima wanu wonse, ndipo yendani naye nthawi zonse. Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi mkhalapakati mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu (1 Timoteo 2:5).
monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.
koma anthu onse ayenera kudziŵa kuti ndimakonda Atate, nchifukwa chake ndikuchita monga Atate adandilamulira. Tiyeni, tizipita.”
Pajatu ndidatsika kuchokera Kumwamba kudzachita zofuna za Iye amene adandituma, osati kuti ndidzachite zofuna Ine ai.
Ndidachokeradi kwa Atate kudza pansi pano. Tsopano ndikuchokanso pansi pano kupita kwa Atate.”
Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse.
Ine ndidadza m'dzina la Atate anga, ndipo inu simukundilandira. Koma wina atabwera m'dzina la iye yekha, iyeyo ndiye mungamlandire.
Tsono Yesu adati, “Kunena zoona Ine Mwanane sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimangochita zimene ndikuwona Atate anga akuchita. Zimene Atate amachita, Mwana amachitanso zomwezo.
ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi ngati la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Atate amafuna kuti anthu onse azilemekeza Mwana, monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana, salemekezanso Atate amene adamtuma.
Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu.
“Namwali wina wosadziŵa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.”
Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu.
Simoni Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu wamoyo.”
Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera naye kwambiri.”
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu.
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
Ngati mutsata malamulo anga, mudzakhala m'chikondi changa, monga momwe Ine ndatsatira malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala m'chikondi chao.
“Ine ndine Woyamba ndiponso Wotsiriza,” akutero Ambuye Mulungu, Mphambe, amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza.
Pakuti Atate amakonda Mwana, namuwonetsa zonse zimene Iwo akuchita. Atate adzamuwonetsanso ntchito zoposa zimenezi, kuti inu muzizwe.
Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Simoni Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu wamoyo.”
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Atate anga akugwira ntchito mpaka tsopano, nanenso ndikugwira ntchito.”
Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake.
Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera Kumwamba.”
Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere.
Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
Koma Yesu adati, “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kani simumadziŵa kuti ndiyenera kupezeka m'nyumba ya Atate anga?”
Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake. Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene adandituma samkoka. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.
Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye Mwana wake woyamba, wolamulira zolengedwa zonse. Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.
Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye Mwana wake woyamba, wolamulira zolengedwa zonse.
Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine.
koma poyang'anira kuyera kwake kwaumulungu, kuuka kwake kwa akufa kukutsimikiza kuti Yesuyo ndi Mwana wa Mulungu.
Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao. Ndi opusa, osakhulupirika, okhakhala moyo, ndi opanda chifundo. Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita. koma poyang'anira kuyera kwake kwaumulungu, kuuka kwake kwa akufa kukutsimikiza kuti Yesuyo ndi Mwana wa Mulungu.
Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha.
Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake. Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Mngeloyo adayankha kuti, “Mzimu Woyera adzakutsikirani, ndipo mphamvu za Mulungu Wopambanazonse zidzakuphimbani. Nchifukwa chake Mwana wodzabadwayo adzakhala Woyera, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu.
Pamenepo ndiye Ayuda adankirankira kufuna kumupha. Ankati Yesu akuphwanya lamulo lokhudza Sabata, ndiponso ponena kuti Mulungu ndi Atate ake, ankadzilinganiza ndi Mulungu.
Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphaŵi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse.
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?”
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”
Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima
Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”
Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimalizo ndine.”