Tikumbukire kuti kuchepetsa mtima ndi kuyamikira ziyenera kukhala zinthu zomwe zimatipangitsa kukhala osiyana, ife amene timazindikira ubwino wa Mulungu pa moyo wathu.
Tikamayesetsa kuchita ntchito zathu mwangwiro ndi molungama, timalemekeza Ambuye ndi kutsegula zitseko kuti madalitso ake aziyenda bwino pa moyo wathu.
Choncho, pa ntchito iliyonse yomwe ndiyamba, ndikumbukire kuti ndi ya Ambuye, ndipo ndi chikhulupiriro ndi kumvera ndidzaona mapulani ake akukula pa moyo wanga. Zikomo Mulungu.
Paja nthaŵi imene tinali nanu pamodzi, tidaakulamulani kuti munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye.
Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.
Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Musamagwira ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimaonongeka, koma muzigwira ntchito kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chili cha moyo wosatha. Mwana wa Munthu ndiye adzakupatsani chakudya chimenechi, pakuti Mulungu Atate adamuvomereza motsimikiza.”
Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.
Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima, ndi kudalitsa zonse zimene timachita, ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu.
Koma chifukwa chakuti Mulungu adandikomera mtima, ndili monga ndilirimu. Ndipo kukoma mtima kwakeko sikunali kopanda phindu, popeza kuti ndidagwira ntchito koposa atumwi ena onse. Komabe si ndine ndidaigwira, koma mphamvu za Mulungu zimene zikundilimbikitsa.
Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.
Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
“Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza?
Ukonzeretu ntchito zako zonse makamaka zakumunda, pambuyo pake mpamene ungayambe kumanga nyumba.
Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri, koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru.
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru.
Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira.
Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika.
Inu akapolo, ambuye anu a pansi pano muziŵamvera mwamantha ndi monjenjemerera. Muzichita zimenezi ndi mtima woona, ngati kuti mukuchitira Khristu yemwe.
Musazichite mwachiphamaso chabe, ngati kuti mukungofuna kukondweretsa anthu. Koma ngati akapolo a Khristu, muzichita ndi mtima wonse zimene Mulungu afuna.
Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe.
Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.
Ntchito iliyonse imene ukuti uigwire, uigwire ndi mphamvu zako zonse. Pajatu kumanda kumene ukupitako kulibe ntchito, kulibe malingaliro, kulibe nzeru, ndiponso kulibe luntha.
Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja,
kuti akunja azikulemekezani, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.
Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, m'menemo munthu wakhama amalemera.
Aliyense aziyesa yekha ntchito zake m'mene ziliri. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, osati chifukwa zapambana ntchito za mnzake.
Pakuti aliyense adzayenera kudzisenzera katundu wakewake.
Choncho ndidaona kuti palibe chinthu chabwino kuposa kuti munthu azikondwerera ntchito yake, pakuti chake chenicheni nchimenechi. Ndani angathe kudziŵa chimene chidzamchitikire iye atafa?”
Tsono Chauta adamtenga munthuyo, namukhazika m'munda wa Edeni uja kuti azilima ndi kumausamala.
Mlimi wogwira ntchitoyo molimbika, ndiye ayenera kukhala woyamba kulandira nao zipatso.
Manja aulesi amagwetsa munthu mu umphaŵi, koma manja achangu amalemeretsa munthu.
Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru, koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi.
Khalani m'nyumba yomweyo. Mudye ndi kumwa zimene akupatsani, pakuti wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake. Musamachoka kumene mwafikirako nkukaloŵa ku nyumba zina ai.
Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso? Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba.
Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye.
Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira.
Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.
“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake.
Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo.
Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu.
Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri.
Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija.
“Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija.
Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera.
Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’
Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’
Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’
Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’
“Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu.
Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’
Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu?
Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake.
Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo.
Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.
Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera.
Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’
Kwa munthu palibe chabwino china choposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Ngakhale zimenezi ndazindikira kuti nzochokera kwa Mulungu.
Nanga popanda Iye ndani angathe kudya, ndani angathe kusangalala?
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake.
Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Wantchito amagona tulo tabwino, ngakhale adye pang'ono kapena kudya kwambiri. Koma wolemera, chuma sichimgonetsa tulo.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Kulakalaka kwa munthu waulesi kumamupha, poti amangokhala manja ali khoba, osagwira ntchito.
Tsiku lathunthu anthu oipa amasirira zinthu, koma omvera Mulungu amapatsa ndipo alibe kaliwumira.
Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo.
Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa, koma adzalimbikitsa anthu onse abwino.
Paja Malembo akuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe imene ikupuntha tirigu.” Penanso akuti, “Wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake.”
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.
Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.
Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.
Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.
Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino.
Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere.
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Iyeyu ndampatsa mzimu wanga, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndipo akudziŵa bwino ntchito zonse zaluso monga izi:
kulemba mapulani a ntchito zaluso ndi kugwira ntchito ndi golide, siliva ndi mkuŵa.
Akudziŵanso kuzokota miyala yogwira nayo ntchito, kujoba mitengo, ndi kuchita zaluso zonse.
Sadzagwira ntchito pachabe, kapena kubereka ana kuti aone tsoka, chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Chauta, iwowo ndi zidzukulu zao zomwe.