Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


56 Mau a M'Baibulo Odalitsira Nyumba

56 Mau a M'Baibulo Odalitsira Nyumba

Ndikuganiza kuti tonse timafuna kuti Mulungu akhale m'banja mwathu pamene tapeza nyumba yathu. Tikamabisala m'madalitso Ake, tiyeneranso kupereka chuma chathu kwa Iye, chifukwa ndi Iye amene watipatsa zonse. Tiyeni tipitirire kwa Atate wathu mokondwera komanso mogwirizana kuti timuthokoze chifukwa cha ubwino Wake.

Ndikofunikanso kulengeza malonjezo Ake tsiku lililonse m'nyumba mwathu, kuti kuwala kwa Yesu kupitirire kuwala m'nyumba mwathu ndi m'mabanja mwathu. Monga momwe lemba la 2 Samueli 7:29 limati, "Tsopano dalitsa nyumba ya mtumiki wanu, kuti ikhalepo pamaso panu nthawi zonse; pakuti inu, Ambuye Mulungu, mwanena, ndipo ndi madalitso anu nyumba ya mtumiki wanu idzadalitsidwa kosatha."




Masalimo 127:1

Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:6-9

Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito. Amangeni pamikono panu, ndiponso muŵaike pa mphumi pakati pa maso anu. Alembeni pa mphuthu za zitseko za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 6:12

Tsono Davide adamva kuti Chauta wadalitsa banja la Obededomu ndi zinthu zonse zimene anali nazo, chifukwa cha Bokosi lachipangano. Choncho iye adapita kukatenga Bokosi lachipanganolo, kulichotsa m'nyumba ya Obededomu, napita nalo ku mzinda wake, akukondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:9

“Pambuyo pake utenge mafuta odzozera aja, udzoze Nyumba ya Mulungu ndi zonse za m'menemo. Uipereke kwa Mulungu Nyumbayo, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, kuti idzakhale yoyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:3

Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:5

Chauta adzadalitsa mbeu zanu ndi chakudya chimene muchikonza kuchokera ku mbeuzo, kuti zichuluke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:8

Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hagai 2:9

Choncho ulemerero wa Nyumba yachiŵiriyi udzaposa ulemerero wa Nyumba yoyamba ija. Ndipo ndidzakhazikitsa ufulu ndi mtendere pa malo ano. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 17:14

Koma ndidzamkhalitsa mu Nyumba yanga ndi mu ufumu wanga, ndipo ufumu wake udzakhala mpaka muyaya.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:13

Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 17:12

Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kuti ukhale wamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:24

“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:5-9

Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse. Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito. Amangeni pamikono panu, ndiponso muŵaike pa mphumi pakati pa maso anu. Alembeni pa mphuthu za zitseko za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 24:15

Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:17

Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:4

Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:1-2

Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:33

Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hagai 2:7

Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu ndipo chuma cha anthu onse chidzabwera, motero Nyumba imeneyi ndidzaidzaza ndi ulemerero waukulu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:1-4

Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino. Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako. Zoonadi, ndimo m'mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:18

Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundiloŵetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:3

Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:7

Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:19-22

Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:14

Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 7:29

Tsono ndikukupemphani kuti mudalitse mokondwa banja la ine mtumiki wanu, likhalebe pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti mwatero ndinu Ambuye Chauta, choncho banja la mtumiki wanune lidzadalitsidwadi mpaka muyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:11

Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:7

Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:3

Chauta adzadalitsa mizinda yanu ndi minda yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:15

Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:6

Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga. Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 4:8

Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:8

Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino. Ngwodala munthu wothaŵira kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:16

Chifukwa tsopano ndaisankha ndipo ndapatula Nyumba ino kuti dzina langa lizikhala m'menemo mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga, zidzakhala m'menemo nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:9

Poyenderana, muzisamalirana bwino mosadandaula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:13

Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:4

Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:11

Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:6

Munthu wochita chilungamo amakhala ndi chuma chambiri, koma zimene woipa amapindula zimamgwetsa m'mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:12-13

Poloŵa m'nyumba, muzikanena kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu’. Tsono ngati anthu am'nyumbamo akulandiranidi, mtendere wanuwo ukhale nawo ndithu. Koma ngati anthu am'nyumbamo akana kukulandirani, mtendere wanuwo ubwerere kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16-17

Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:13

Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:18

Anthu a Mulungu adzakhala m'midzi yamtendere, m'nyumba zokhulupirika, ndiponso m'malo ousira abata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:7-8

Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:14

Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:3-4

Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:5-7

Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse. Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:14

ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 65:11

Pakutha pa chaka mumapereka zokolola zambiri mwa ubwino wanu, kulikonse kumene Inu mupita, kumapezeka dzinthu dzambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:20

Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:10-11

zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga, dzina lanu ndi lolemekezeka ndi loopsa, palibe chofanana ndi chiyero chanu! Atate, tikulengeza masiku a madalitso ndi chipambano pa mabanja onse a dziko lapansi. Mulungu adalitse nyumba iliyonse, ndikupempha kuti muwapatsenso nzeru zomangira ndi kuchenjera kuti ikhale yolimba, kuti ngakhale m'masiku awo ovuta ndi mayesero nyumba yawo isagwe, chifukwa yakhazikika pa thanthwe lomwe ndinu inu. Ambuye, monga momwe munadalitsira nyumba ya Obedi-Edomu ndi zonse zomwe anali nazo, momwemonso madalitso anu akhale pa iwo ndipo kukhalapo kwanu kulamulire m'nyumba mwawo nthawi zonse. Mawu anu amati: "Pakuti ndikudziwa malingaliro amene ndikulingirira za inu, ati Yehova, malingaliro a mtendere, osati a choipa, kuti ndikupatseni chiyembekezo." Ndikulengeza magazi a Khristu pa mabanja awo ndipo angelo anu atumizidwe kuwazungulira. Atate, ulemerero ndi ulemu zonse zikhale kwa inu. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa