Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


61 Mau a M'Baibulo Odalitsira Mnzanu

61 Mau a M'Baibulo Odalitsira Mnzanu

Mtima wanga ukukulimbikitsani kuti muchite zambiri kuposa kungonena mawu okoma kwa mnzanu, kapena kungomupatsa mphatso. Pali chinthu china chamfundo chomwe mungamuchitire, chomwe sadzachiiwala, ndipo ndicho kupempherera moyo wake kwa Mulungu. Pali malo ambiri amene sitingathe kufikako ndi mphamvu zathu, koma kudzera mu pemphero, zinthu zazikulu zimachitika.

Yesetsani kuti mawu onse otuluka pakamwa panu akhale odalitsa, kuti mulembe zinthu zabwino pa miyoyo ya anthu omwe akuzungulirani. Umu ndi momwe ubwenzi weniweni umakhalira, ndipo umatha nthawi yaitali.

M’Baibulo muli mavesi ambiri amene tingapatse anthu amene atithandiza pa moyo wathu, amene atiphunzitsa zinthu zabwino, amene Mulungu watipatsa kuti akhale nafe nthawi ya chisangalalo ndi nthawi ya mavuto. Ndi anthu amenewa amene timawayikira mtima. "Malemba onse ndi ouziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi othandiza pa kuphunzitsa, kudzudzula, kulungamitsa, ndi kulangiza m’chilungamo." (2 Timoteo 3:16)




Miyambo 17:17

Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:23

Ambuye Yesu Khristu akudalitseni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:19

Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:11

Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 6:24-26

Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4-5

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye. Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:13

Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 4:9

Kukhala aŵiri nkwabwino koposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu aŵiri ili ndi phindu lopambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:9

Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, koma kukoma kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:17

Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:24

Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Filemoni 1:7

Mbale wanga, chikondi chako chandikondweretsa kwambiri ndi kundithuzitsa mtima, pakuti watsitsimutsa mitima ya oyera onse a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:1

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
3 Yohane 1:2

Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Filemoni 1:4-5

Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukira m'mapemphero anga. Pakuti ndikumva kuti umakonda ndi kukhulupirira Ambuye Yesu, ndi oyera onse a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:8

Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:11

Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:4

Akupatse zimene mtima wako ukukhumba, akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:22

Madalitso a Chauta ndiwo amalemeretsa, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:3-4

Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-14

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:11

Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:1

Ati kukoma ndi kukondweretsa ati, anthu akakhala amodzi mwaubale!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 18:1-3

Davide atatha kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani udagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani adakonda Davideyo monga momwe ankadzikondera iye mwini. M'maŵa mwake mzimu woipa uja udamtsikira Saulo, ndipo adayamba kubwebweta moyaluka m'nyumba mwake. Davide ankamuimbira zeze, monga momwe ankachitira tsiku ndi tsiku. Saulo anali ndi mkondo m'manja mwake. Tsono adaponya mkondowo ndipo mumtima mwake adati, “Ndimubaya ndi kumkhomera ku chipupa.” Koma Davide adauleŵa. Zidachitika kaŵiri konse. Pambuyo pake Saulo adayamba kuwopa Davide, chifukwa choti tsopano Chauta anali ndi Davide, kumsiya iyeyo. Motero Saulo adamtuma Davide kwina kwake, ndipo adamuika kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Davide ankapita namabwera akuŵatsogolera. Ndipo ankapambana pa zonse zimene ankachita, chifukwa Chauta anali naye. Tsono pamene Saulo adaona kuti Davide akupambana kwambiri, adayamba kuchita naye mantha. Koma anthu onse a ku Israele ndi a ku Yuda ankamkonda Davide, chifukwa iyeyu ankaŵatsogolera namapambana pa zonse. Tsiku lina Saulo adauza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkulu. Ndidzakupatsa kuti akhale mkazi wako. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Chauta.” Potero Saulo ankaganiza kuti, “Ndisamuphe ndine ndi dzanja langa, koma amuphe ndi Afilisti.” Tsono Davide adafunsa Saulo kuti, “Kodi ine ndine yani, ndipo abale anga ndi banja la bambo wanga ndife yani m'dziko la Israele, kuti ine nkukhala mkamwini wa mfumu?” Koma pa nthaŵi yoti Merabi, mwana wa Saulo, akwatiwe ndi Davide, bambo wake adampereka kwa Adriyele Mmehola, kuti akhale mkazi wake. Mwakuti adamtenga Davideyo tsiku lomwelo, osamlola kuti abwerere ku banja kwa bambo wake. Komabe Mikala, mwana wina wamkazi wa Saulo, ankakonda Davide. Saulo atamva, adakondwa kwambiri. Adaganiza kuti, “Ndimpatse amkwatire, kuti adzakhale ngati msampha kwa Davideyo, ndipo Afilisti adzamupha.” Nchifukwa chake Saulo adauza Davide kachiŵiri kuti, “Tsopano udzakhala mkamwini wanga.” Motero adalamula nduna zake kuti, “Mulankhule naye Davide pambali nkumuuza kuti, ‘Mfumu imakukonda, ndipo ngakhale nduna zake zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ” Nduna za Saulo zidamuuza Davide mau amenewo. Koma iye adati, “Kani mukuchiyesa chinthu chapafupi kukhala mkamwini wa mfumu? Kodi simukuwona kuti ndine wosauka ndi wosatchuka?” Nduna za Saulo zidamuuza zonse zimene Davide adaanena. Tsono Saulo adati, “Kamuuzeni kuti, sindikufuna chiwongo cha mtundu uliwonse ai, ndingofuna timakungu ta nsonga za mavalo a Afilisti 100, kuti ndilipsire adani anga.” Potero Saulo ankaganiza zoti Davide aphedwe ndi Afilisti. Ndiye nduna za Saulozo zitamuuza Davide mau ameneŵa, zidamkondweretsa kuti akhale mkamwini wa mfumu. Nthaŵi yoti atenge mkazi wake isanakwane, Davide adanyamuka napita pamodzi ndi ankhondo ake, ndipo adakapha Afilisti 200. Adabwera nato timakungu tija natipereka kwa mfumu, kuti choncho akhale mkamwini wake. Apo Saulo adapatsa Davideyo mwana wake Mikala, kuti akhale mkazi wake. Koma Saulo atazindikira kuti Chauta ali naye Davide, ndiponso kuti mwana wake Mikala ankamkonda Davideyo, adamuwopabe kwambiri ndi kudana naye moyo wake wonse. Adachita naye chipangano chifukwa ankamkonda monga momwe ankadzikondera iye mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4-7

Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 42:10

Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:24

Mau okometsera ali ngati chisa cha uchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 41:1-2

Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto. Koma Inu Chauta, mundikomere mtima, mundichiritse kuti ndiŵalange anthuwo. Mukatero ndidzadziŵa kuti mumakondwera nane, chifukwa mdani wanga sadandipambane. Inu mwandichirikiza chifukwa cha kukhulupirika kwanga, mwandikhazika pamaso panu mpaka muyaya. Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Inde momwemo. Inde momwemo. Chauta adzamteteza ndi kumsunga ndi moyo. Adzatchedwa wodala pa dziko. Chauta sadzampereka kwa adani ake, kuti amchite zimene iwo akufuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:7-8

Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 3:12

Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:15

Sindikutchulaninso antchito ai, pakuti wantchito sadziŵa zimene mbuye wake akuchita. Koma ndikukutchulani abwenzi, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziŵitsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:6

Amene amakukonda, ngakhale akupweteke, chikondi chake chimakhalapobe, mdani wako ngakhale akumpsompsone, nkunyenga chabe kumeneko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:23-24

Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:25

Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 13:11

Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:20-21

Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo. Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:16-18

Nchifukwa chake sindilekeza kuthokoza Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani m'mapemphero anga, ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1-3

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5

Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:2

Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:20

Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:26

Munthu wochita zabwino amatsogolera anzake pa njira yokhoza, koma njira ya munthu woipa imaŵasokeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:15

Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:63

Ine ndine bwenzi la anthu okuwopani, anthu otsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16-19

Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi. Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:10

Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:4

Nthaŵi zonse ndimayamika Mulungu wanga chifukwa cha inu, popeza kuti adakukomerani mtima mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:14-15

Chauta akudalitseni inu, pamodzi ndi zidzukulu zanu zomwe. Akudalitseni Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Yesu wokondedwa, inu ndinu wokhulupirika nthawi zonse, chikondi chanu chandisunga ine ndipo mumandiutsa m'mawa uliwonse. Inu ndinu chitsanzo chenicheni cha kukhulupirika ndi chikondi chosatha. Ndikukupemphani kuti mundithandize kukhala mnzanga wabwino kuti ndidalitse miyoyo ya anzanga onse monga momwe inu mumachitira. Panopa, ndikukupemphani kuti muteteze ndi kulimbitsa mnzanga. Mupatseni nzeru ndi luntha kuti asankhe zinthu zabwino, kuti ayende m'njira yomwe munamuyikira. Mulimbitseni, mutsitsimutse mphamvu zake, ndipo mukulitse chikhulupiriro chake, kuti Mzimu Woyera wanu ukhale patsogolo pa moyo wake ndi wa banja lake. Mawu anu amati: "Ndipo Mulungu ndiye wakutha kukuchulukitsani chisomo chonse, kuti mukhale nacho chokwanira nthawi zonse m'zinthu zonse, kuti muchuluke ntchito iliyonse yabwino." Ambuye, pitirizani kumpatsa zonse zomwe akusowa, mupatseni nzeru ndi kulimba mtima kuti agonjetse mantha ake ndi kupambana mavuto alionse omwe akukumana nawo. Ndikulengeza kuti mukuyenda patsogolo pake ngati chimphona champhamvu, mukulimbana nkhondo zake zonse. Mumuteteze ku ziwembu zonse za mdani. Zikomo Ambuye, ulemerero ndi ulemu zonse zikhale kwa inu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa