Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi. Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.
Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha.
Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.
Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake? Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ”
Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”
Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.
Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
Abale anga, pali phindu lanji, ngati munthu anena kuti, “Ndili ndi chikhulupiriro,” koma popanda chimene akuchitapo? Kodi chikhulupiriro chotere chingampulumutse? Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira. Tsono wina mwa inu angoŵauza kuti. “Pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute”, koma osaŵapatsa zimene akusoŵazo, pamenepo phindu lake nchiyani? Choncho, chikhulupiriro pachokha, chopanda ntchito zake, nchakufa basi.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni. Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.
Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho.
Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse.
Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphaŵi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse.
Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.
mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe. Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.
Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.”
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.
Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Malinga munthu akakhala ndi changu cha kupereka, Mulungu amalandira mokondwa zimene munthuyo ali nazo, ndipo samkakamiza kuti apereke zimene alibe.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.
Iyai, inu muzikonda adani anu, muzichita zabwino, ndipo muzikongoza osayembekeza kulandirapo kanthu. Mukatero mudzalandira mphotho yaikulu, ndiye kuti mudzakhala ana a Mulungu Wopambanazonse. Pajatu Iye amachitira zabwino anthu osayamika ndi oipa omwe.
Koma makamaka, monga mau a Mulungu akunenera, “Ngati mdani wako wamva njala, iwe umpatse chakudya. Ngati wamva ludzu, iwe umpatse madzi akumwa. Ukatero udzamchititsa manyazi kwambiri.” Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.
Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi. “Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.”
Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”
Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.
Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.
Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu. Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”
Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.
Kodi wamkulu ndani? Ndi amene alikudya, kapena amene akumtumikira? Si amene alikudyayo nanga? Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumukira.
Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe zimene dzanja lako lamanja likuchita. Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu? “Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’ Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu akumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi. Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso. Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira. Ukatero, zachifundo zakozo zidzakhala zodziŵa iwe wekha. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.
Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto.
Pamenepo anthu aja adafunsa Yohane kuti, “Tsono ife tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.”
Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”
Ku Yopa kunali wophunzira wina wamkazi, dzina lake Tabita (pa Chigriki amati Dorika). Iyeyu ankachita ntchito zabwino zambiri ndi kumathandiza osauka.
Akhale mai woti anthu amamchitira umboni wakuti amachitadi ntchito zabwino. Akhale woti ankalera ana ake bwino, ankalandira bwino alendo, ankasambitsa mapazi a anthu a Mulungu, ndipo ankathandiza anthu amene anali m'mavuto. Akhalenso mai woti ankadzipereka pa ntchito zonse zabwino.
Ndipo adathandizadi mopitirira pa zimene tidaayembekeza, pakuti poyamba adadzipereka kwa Ambuye, kenaka mwa kufuna kwa Ambuye adadziperekanso kwa ife.
Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”
Adangopempha chokhachi kuti tisaleke kukumbukira anthu ao aumphaŵi. Ndipotu chimenechi ndicho ndakhala ndikuchita moikapo mtima.
Munthu wosalankhula umlankhulire ndiwe. Anthu osiyidwa uŵalankhulire pa zoŵayenerera. Uzilankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uziteteza amphaŵi ndi osauka.
Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”
Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Amene amatseka m'khutu wosauka akamalira, adzalira iyenso, koma kulira kwakeko sikudzamveka.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”
Kwa amene ali ndi chikhulupiriro chofooka, ndidakhala ngati wa chikhulupiriro chofooka, kuti ndiŵakope ofookawo. Kwa anthu onse ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ngati nkotheka ndikope ena mwa iwo.
Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.
Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.
Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.
Uzilemekeza nacho Chauta chuma chako chonse, uzimuyamika nazo zokolola zako zonse zam'minda.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
Muzikumbukira am'ndende, ngati kuti mukuzunzikira nawo limodzi m'ndendemo. Muzikumbukira ovutitsidwa, pakuti inunso muli ndi thupi.
Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’
Amapereka chithandizo mwaufulu, amaoloŵa manja kwa anthu osauka. Chilungamo chake chidzakhala chamuyaya, adzakhala wamphamvu ndipo anthu adzampatsa ulemu.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.
Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo. Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao. Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.
Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.”
Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.”
Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.
Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu. Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko.
Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “Zimene ndiri nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse. Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankaŵakomera mtima kwambiri. Panalibe munthu wosoŵa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. Ndipo ndalamazo ankagaŵira munthu aliyense malinga ndi kusoŵa kwake.
Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba.
Kunena za ine, ndidzakondwa kupereka zanga zonse, ndi kutaya ngakhale moyo wanga womwe chifukwa cha inu. Ine ndikamakukondani kwambiri chotere, kodi ndiye kuti inuyo muzingondikonda pang'ono?
Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.
Ndakondwa kwambiri mwa Ambuye kuti tsopano, patapita nthaŵi yaitali, mwayambanso kuwonetsa kuti mumandikumbukira. Kukumbukira munkandikumbukiradi, koma munkangosoŵa mpata woti muwonetsere.
Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “Inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuŵa, ndani adakhala ngati mnzake wa munthu uja achifwamba adaamugwirayu?” Iye adati, “Amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.”
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi. Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.
Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu.
Ndidzambwezera chiyani Chauta pa zabwino zonse zimene adandichitira? Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.
Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu. Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Pakuti ntchito imeneyi ikuŵatsimikizira kuti chifundo chanu nchoona, iwo adzatamanda Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu povomereza Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Adzatero chifukwanso cha ufulu wanu poŵagaŵirako iwowo ndi anthu ena onse zinthu zimene muli nazo. Tsono adzakuwonetsani chikondi chao ndi kukupemphererani, chifukwa Mulungu wakukomerani mtima kopitirira.
“Sindikupempherera iwo okhaŵa ai, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha mau ao. Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi. Monga Inu Atate mumakhala mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife. Motero anthu onse adzakhulupirira kuti mudandituma. Ulemerero womwewo umene mudandipatsa, ndaŵapatsanso iwoŵa. Akhale amodzi monga Ife tili amodzi. Ine ndikhale mwa iwo, Inu mwa Ine, kuti akhale amodzi kwenikweni. Motero anthu onse adzazindikira kuti mudandituma ndinu, ndipo kuti mumaŵakonda monga momwe mumandikondera Ine.