Mulungu anakulenga kuti ukhale chitoliro cha madalitso kwa anthu akuzungulira, kuonesa ulemerero wake padziko lapansi.
Mu Mateyu 22:37-39, Yesu anatipatsa lamulo lalikulu: "Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiŵiri lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha." Ngati ukunena kuti umamukonda Mulungu, koma sukudalitsa ndi kukonda mnzako, ukulephera pa lamulo ili. Chikondi chenicheni cha Mulungu chimaonekera m’machitidwe athu kwa ena.
Sungalankhule kuti umamukonda amene sukamuona, koma n’kunyoza mnzako amene ali pafupi nawe. Uyenera kukhala chitsanzo cha chikondi cha Atate kumene ukukhala, ndi mtima wowolowa manja wokonzeka kuthandiza. Sikuti kungonena chabe, koma kuchita zinthu zothandiza mnzako.
Ngati uli ndi mphamvu yochita zabwino, zitani, ndipo kumbukira kuti: "Wopatsa munthu wosauka akukongoza Yehova" (Miyambo 19:17). Usamayang'ane zofuna zako zokha, koma zofuna za mnzako. Tsatirani mawu a Yesu, sangalatsani mtima wake ndipo khalani dalitso.
Cholinga chako ndi kubweretsa chimwemwe ndi chisangalalo kwa anthu amene akumufuna Mulungu. Usagwire ntchito chifukwa cha zofuna zako zokha, kumbukira kuti wadalitsidwa kuti udalitse ena.
Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena.
Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Katswiri wina wa Malamulo adaimirira kuti ayese Yesu. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”
Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mudalembedwa chiyani? Mumaŵerengamo zotani?”
Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Yesu adati, “Mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.”
Koma munthu uja pofuna kudziwonetsa ngati wolungama, adafunsa Yesu kuti, “Nanga mnzangayo ndani?”
Pitani tsono. Ndikukutumani ngati anaankhosa pakati pa mimbulu.
Apo Yesu adati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa.
“Ndiye zidangochitika kuti wansembe wina ankapita pa njira yomweyo. Pamene adaona munthu uja, adangolambalala.
Chimodzimodzinso Mlevi wina adafika pamalopo, ndipo pamene adaona munthuyo, nayenso adangolambalala.
Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni.
Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.
M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ”
Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “Inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuŵa, ndani adakhala ngati mnzake wa munthu uja achifwamba adaamugwirayu?”
Iye adati, “Amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.”
Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu.
Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’
Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa?
Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani?
Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife nkudzakuchezetsani?’
Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao.
Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.
Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu.
Tikugwira ntchito kolimba ndi manja athu kuti tidzisunge. Anthu akamatichita chipongwe, timapempha kuti Mulungu aŵadalitse. Anthu akamatizunza, timangopirira.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Ndithu, ndalandira lamulo kuti ndidalitse. Iye wadalitsa, ndipo ine sindingathe kusintha kanthu.
Abale anga, pali phindu lanji, ngati munthu anena kuti, “Ndili ndi chikhulupiriro,” koma popanda chimene akuchitapo? Kodi chikhulupiriro chotere chingampulumutse?
Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira.
Tsono wina mwa inu angoŵauza kuti. “Pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute”, koma osaŵapatsa zimene akusoŵazo, pamenepo phindu lake nchiyani?
Choncho, chikhulupiriro pachokha, chopanda ntchito zake, nchakufa basi.
Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha.
mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”
Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.
Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”
Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.”
“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse.
Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.
Pamenepo anthu aja adafunsa Yohane kuti, “Tsono ife tizichita zabwino zanji?”
Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.”
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.
Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.
Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.”
Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ”
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima.
Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.
Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.
Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse ine mtumiki wanu, monga momwe mudalonjezera.
Chauta adaonekera Abrahamu ku mitengo ya thundu ya ku Mamure ija. Abrahamuyo atakhala pa khomo la hema lake nthaŵi yamasana kutatentha,
Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.” Sara ankangomvetsera ali kuseri kwa chitseko cha hema.
Abrahamu pamodzi ndi Sara anali nkhalamba zokhazokha, ndipo nthaŵi imeneyo nkuti Sara ataleka kusamba monga amachitira akazi.
Motero Sara adangoseka, namati, “Ha, monga ndakalambira inemu, kodi nkuthekanso kuti ndikondwe ndi mwamuna wanga? Komanso mwamuna wanga ndi wokalamba zedi.”
Chauta adafunsa Abrahamu kuti, “Chifukwa chiyani Sara amaseka ndi kunena kuti, ‘Ine monga ndakalambiramu kungatheke bwanji kukhala ndi mwana?’
Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
Apo Sara adakana chifukwa cha mantha, adati, “Sindidaseke.” Koma Iye adati, “Inde, unaseka.”
Tsono anthuwo adachoka, nafika pamalo pamene anali kupenya Sodomu. Abrahamu adapita nawo limodzi, naŵalozera njira.
Ndipo Chauta adanena mwa Iye yekha kuti, “Abrahamuyu sindingamubisire chomwe ndikuti ndichite.
Zidzukulu zake zidzakhala mtundu waukulu wamphamvu. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa chifukwa cha iye.
Ndamsankha iyeyu kuti alamule ana ake ndi mabanja ake akutsogolo kuti azidzamvera mau anga, pochita zabwino ndi zolungama. Choncho ndidzachita zonse zimene ndidamlonjeza.”
mwadzidzidzi adangoona anthu atatu ataimirira potero. Atangoŵaona, adanyamuka mwamsanga kukaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu,
Tsono Chauta adauza Abrahamu kuti, “Pali zolakwa zoopsa zokhudza Sodomu ndi Gomora, ndipo tchimo lao ndi lalikulu kwambiri.
Choncho ndikuti nditsikireko kuti ndikaone ngati zolakwa zimene ndamvazo ndi zoona. Ngati si choncho, ndidzadziŵa.”
Anthu aja adachoka, napita ku Sodomu, koma Abrahamu adatsarira ndi Chauta.
Apo Abrahamu adayandikira kwa Chauta namufunsa kuti, “Kodi monga mudzaonongadi anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa?
Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo?
Ndithu simudzaononga anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa. Chimenechi nchosatheka ndipo simungachite. Mukadatero bwenzi anthu osachimwa akulangidwira kumodzi ndi ochima. Kutalitali, Inu simungachite zotere! Kodi Muweruzi wa dziko lonse lapansi nkupanda chilungamo?”
Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 50 osachimwa m'Sodomu, ndidzauleka mzinda wonsewo osauwononga, chifukwa cha anthu 50 amenewo.”
Abrahamu adalankhulanso, adati, “Chonde, ndalimba mtima pakulankhula nanu chotere, Ambuye. Inetu ndine munthu chabe pamaso panu.
Nanga pa chiŵerengero cha 50 pakangopereŵera anthu asanu okha, bwanji? Kodi mudzaononga mzindawo popeza kuti asoŵa asanu okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 45 olungama, sindidzaononga mzindawo.”
Abrahamu adafunsanso kuti, “Nanga pakapezeka anthu olungama 40 okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 40, sindidzauwononga.”
nati, “Mbuyanga, ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, chonde musapitirire pakhomo pa mtumiki wanu.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.
Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti, nthaŵi iliyonse pamene munkakana kuthandiza wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkakana kuthandiza Ine amene.’
Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi.
Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.
Lamulo limene Iye adatipatsa ndi lakuti, wokonda Mulungu azikondanso mbale wake.
Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.
Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani.
Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu.
Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa.
Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu.
Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
“Ukaona ng'ombe ya mdani wako ikusokera, kapena bulu wake, utenge ukampatse.
Bulu wa mdani wako akagwa ndi katundu, usabzole ndi kumsiya, koma umthandize kuti adzuke.
“Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.”
Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.
Kuli bwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu osauka, kupambana kumagaŵana chuma ndi anthu onyada.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.
Adachita zimenezi kuti pasakhale kugaŵikana m'thupi, koma kuti ziwalo zonse zizisamalirana.
Chiwalo chimodzi chikamamva kuŵaŵa, ziwalo zonse zimamvanso kuŵaŵa. Chiwalo chimodzi chikamalandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwa nao.
Popereka zachifundo kwa amphaŵi, muzipereka zimene zili m'kati, ndiye pamenepo zanu zonse zidzakhala zoyera.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo.
Amapereka chithandizo mwaufulu, amaoloŵa manja kwa anthu osauka. Chilungamo chake chidzakhala chamuyaya, adzakhala wamphamvu ndipo anthu adzampatsa ulemu.
Munthu wosalankhula umlankhulire ndiwe. Anthu osiyidwa uŵalankhulire pa zoŵayenerera.
Uzilankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uziteteza amphaŵi ndi osauka.
Mverani, abale anga okondedwa, kodi suja Mulungu adasankha ooneka amphaŵi m'maso mwa anthu, kuti akhale olemera pa chikhulupiriro, ndi kuti alandire madalitso amene Iye adalonjeza anthu omukonda?
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.
Chauta, mundikumbukire pamene mukukomera mtima anthu anu. Mundithandize pamene mukuŵapulumutsa,
Tsono mkwiyo wa Chauta udayakira anthu ake, chifukwa adanyansidwa nawo anthu akewo.
Adaŵapereka kwa mitundu ina ya anthu, kotero kuti amene ankadana nawo, ndiwo amene ankaŵalamulira.
Adani ao ankaŵazunza, ataŵagonjetsa adaŵaika mu ulamuliro wao.
Nthaŵi zambiri Iye ankaŵapulumutsa, koma iwo ankamuukirabe osaleka, namamira m'machimo ao,
Komabe Chauta adaŵathandiza pa mavuto ao pamene adamva kulira kwao.
Adakumbukira chipangano chake chifukwa cha kuŵakonda anthuwo, naleza mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake chosasinthika.
Chauta adafeŵetsa mitima ya adani onse amene adagwira anthu ake ukapolo, kuti aŵachitire chifundo anthu akewo.
Tipulumutseni Inu Chauta, Mulungu wathu, mutisonkhanitse kuchokera pakati pa anthu akunja, kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera, kuti tizinyadira pokutamandani.
Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Anthu onse anene kuti, “Inde momwemo.” Tamandani Chauta!
kuti ndiwone zokoma za osankhidwa anu, kuti ndigaŵane nawo chisangalalo cha mtundu wanu, kuti ndipeze ulemerero pamodzi ndi anthu anu.
Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.
Ndipo adamuuza kuti, “Ine ndine mwana wa Rebeka, mlongo wa atate ako.” Pomwepo Rakele adathamanga kukauza atate ake.
Labani atamva za Yakobe mwana wa mlongo wake, adathamanga kukakumana naye. Adamkumbatira, namumpsompsona, nkupita naye kunyumba. Tsono Yakobe adafotokozera Labani zonse zimene zidachitika.
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la atate ako. Usachite kupita ku nyumba ya mbale wake, ukakhala pa mavuto. Mnzako wokhala naye pafupi amaposa mbale wako wokhala kutali.
Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.
Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
Nthaŵi zonse munthu wolungama amapatsa mosaumira, ndipo amakongoza mwaufulu, ana ake amakhala madalitso.
Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Chauta akuthandize pa tsiku lamavuto. Mulungu wa Yakobe akuteteze.
Akutumizire chithandizo kuchokera ku malo ake oyera, akuchirikize kuchokera ku Ziyoni.
Yesu adatuluka m'chombomo, ndipo pamene adaŵaona anthu ambirimbiriwo, adaŵamvera chifundo, nayamba kuchiritsa amene ankadwala.
Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira.
Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye.
Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse.
Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi.
Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera.
Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.”
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru.
Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite.
Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.
Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse.
Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.
Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake.
Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse.
Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.
Usamuuze mnzakoyo kuti, “Pita, ukachite kubweranso, ndidzakupatsa maŵa,” pamene uli nazo tsopano lino.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Koma tsopano mukumdziŵa Mulungu, makamaka ndinene kuti Mulungu ndiye akudziŵa inu. Nanga bwanji mukubwereranso ku miyambo yachabe ndi yopanda phindu ija? Bwanji mukufuna kukhalanso akapolo ake?
Anthu amene amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino ndiwo adani anga, chifukwa ine ndimachita zabwino.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
“Mukatero, mudzaŵala ngati mbandakucha, ndipo mabala anu adzapola msanga. Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani, ndipo ulemerero wanga udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Koma kapena wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro, ineyo ndili ndi ntchito zabwino.” Pamenepo ine nkumuyankha kuti, “Uyesetse kundiwonetsa chikhulupiriro chako chopanda ntchito zakecho, ine ndi ntchito zanga ndikuwonetsa chikhulupiriro changa.”
Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe zimene dzanja lako lamanja likuchita.
Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka.
Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.
Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge.
Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.
Maso anga afiira nkuyang'anira malonjezo anu. Ndimafunsa kuti, “Kodi mudzandithandiza liti?”
Ndipo ngakhale nditagaŵira amphaŵi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe.
Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni.
Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima.
Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.
Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.