Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.
Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.
Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako.
Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu.
Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?
Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala?
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Koma amene amamvera ine adzakhala pabwino, adzakhala mosatekeseka, osaopa choipa chilichonse”.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Anthu a Mulungu adzakhala m'midzi yamtendere, m'nyumba zokhulupirika, ndiponso m'malo ousira abata.
Khulupirira Chauta ndipo uzichita zabwino. Khala m'dziko ndi kutsata zokhulupirika.
Munthu wabwino amalankhula zanzeru, pakamwa pake pamatuluka zachilungamo.
Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake, motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno.
Munthu woipa amazonda munthu wabwino, amafunafuna kuti amuphe.
Koma wolungamayo Chauta sadzamsiya yekha m'manja mwa mdani wake, sadzalola kuti pomuweruza, mlandu wake umuipire.
Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake. Motero adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako. Udzaona anthu oipa akuwonongeka.
Ndidaona munthu woipa akunyada ndi kudzitukumula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
Koma pambuyo pake, podutsanso, ndidaona kuti palibe. Ngakhale ndidamfunafuna, sindidathe kumpeza.
Upenye munthu wopanda cholakwa ndi wolungama, ndipo udzapeza kuti munthu wamtendere ali ndi zidzukulu zambiri.
Koma anthu ochimwa adzaonongekeratu kwathunthu, iwo pamodzi ndi zidzukulu zao zomwe.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.
Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.
Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa.
Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.
Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.
Usamaopa zoopsa zobwera modzidzimutsa, usamachita mantha ndi tsoka lodzagwera anthu oipa.
Chauta ndiye adzakhale chikhulupiriro chako, adzasunga phazi lako kuti lingakodwe.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga.
Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo.
Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake.
Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.
Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,
pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe.
Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo.
Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu.
Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha.
Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika.
Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino.
Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.
Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa.
Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Chauta adzamteteza ndi kumsunga ndi moyo. Adzatchedwa wodala pa dziko. Chauta sadzampereka kwa adani ake, kuti amchite zimene iwo akufuna.
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.
Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu.
Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.
Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.
“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”
Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.
Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
Adzakupatsani mtendere wokhazikika pa nthaŵi yanu. Adzakuninkhaninso chipulumutso chachikulu, luntha lambiri ndi nzerunso zambiri. Kuwopa Chauta ndiko kumapezetsa chuma chimenechi.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Sadzalola phazi lako kuti literereke, Iye amene amakusunga sadzaodzera.
Zoonadi, amene amasunga Israele, ndithu sadzaodzera kapena kugona.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Inu mwakhala ngati ngaka kwa anthu osauka, mwakhala ngati linga kwa anthu osoŵa pa nthaŵi yamavuto. Mwakhala ngati pobisalirapo namondwe, ndiponso ngati mthunzi wousirapo dzuŵa. Anthu ankhalwe ali ngati namondwe woomba pa khoma, ngati chitungu m'dziko louma.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Nchifukwa chake mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye yekha Mulungu, ndipo ndi Mulungu wokhulupirika. Iye adzasungadi chipangano chake ndipo adzaonetsa chifundo chake chosasinthika kwa anthu a mibadwo zikwi zambirimbiri amene amakonda Iye namamvera malamulo ake.
Chauta ndiye amene amakusunga, Chauta ndiye mtetezi wako ali ku dzanja lako lamanja.
Dzuŵa silidzakupweteka masana, mwezi sudzakuvuta usiku.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku, kapena nkhondo nthaŵi yamasana.
Sudzaopanso mliri wogwa usiku, kapena zoononga moyo masana.
Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Chauta, ngakhale adani ake omwe amakhala naye mwamtendere.
“Anthu okhulupirika Iye adzatchinjiriza moyo wao, koma anthu oipa adzazimirira mu mdima, pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake.
Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo.
koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
Chauta amayang'ana anthu omumvera, ndi odalira chikondi chake chosasinthika.
Iye amachita izi kuti aŵapulumutse ku imfa ndi kuŵasungira moyo anthuwo pa nthaŵi ya njala.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.
Ozunzikawo atayang'ana kwa Chauta, nkhope zao zidasangalala, sadachite manyazi.
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Anzako chikwi chimodzi angathe kuphedwa pambali pakopa, kapena zikwi khumi ku dzanja lako lamanja, koma iwe zoopsazo sizidzakukhudza.
Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu.
Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu.
Mtima wanga ukukangamira Inu, dzanja lanu lamanja likundichirikiza.
“Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake.
Pamene amphaŵi ndi osauka akufunafuna madzi, koma osaŵapeza, ndipo kum'mero kwao kwangoti gwa ndi ludzu, Ine Chauta ndidzayankha pemphero lao, Ine Mulungu wa Israele sindidzaŵasiya.
Usaisiye nzeru, ndipo idzakusunga. Uziikonda, ndipo idzakuteteza.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.
Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundiloŵetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.
Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.
Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,
chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Yabezi adatama Mulungu wa Israele mopemba kuti, “Mundidalitse ine, ndipo dziko langa mulikuze. Dzanja lanu lamphamvu likhale nane, ndipo mundisunge ine, kuti choipa chisandigwere ndi kumandisautsa.” Motero Mulungu adampatsadi zimene adaapemphazo.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Apo Mose adayankha anthuwo kuti, “Musaope! Limbikani, ndipo muzingopenya zimene Chauta achite lero lino pofuna kukupulumutsani. Aejipito amene mukuŵaona lerowo, simudzaŵaonanso.
Chauta ndiye amene akumenyereni nkhondo. Inuyo simuchitapo kanthu konse.”
Usaope, iwe Yakobe, wofooka ngati nyongolotsi, usachite mantha, iwe Israele, wooneka ngati mtembo, chifukwa Ineyo ndidzakuthandiza. Mpulumutsi wako ndine, Woyera uja wa Israele.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.
Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.
Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.
Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.
Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.
Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.
Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.
Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo, am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu, koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.