Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Nanga angelo, kodi suja iwo ndi mizimu yotumikira chabe, imene Mulungu amaituma chifukwa cha anthu odzalandira chipulumutso?
“Ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu, kuti akutchinjirizeni pa njira ndi kukufikitsani ku malo amene ndakukonzerani.
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Yakobe adanyamuka ulendo wake, ndipo angelo a Mulungu adakumana naye. Ine sindiyenera kulandira chifundo ndi chikhulupiriro chonse chimene mwandiwonetsa ine mtumiki wanu. Ndidaoloka Yordani ndilibe nkanthu komwe, koma ndodo yokha, koma tsopano ndabwerera ndi magulu aŵiri aŵa. Ndapota nanu, pulumutseni ku mphamvu za mbale wanga Esau. Ndikuwopa kuti mwina akubwera kudzatithira nkhondo, ndipo tonsefe adzatiwononga pamodzi ndi akazi ndi ana omweŵa. Kumbukirani lonjezo lanu lija lakuti, ‘Ndithu ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zosaŵerengeka. Zidzakhala zochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja.’ ” Atagona kumeneko, pambuyo pake adasankhula mphatso izi pa chuma chonse chimene anali nacho: mbuzi zazikazi 200 ndi atonde makumi aŵiri, nkhosa zazikazi 200 ndi zamphongo makumi aŵiri, ngamira zamkaka makumi atatu pamodzi ndi ana ake, ng'ombe zazikazi makumi anai, ndi zazimuna khumi, ndi abulu aakazi makumi aŵiri ndi amphongo khumi. Gulu lililonse la zoŵeta adalipatsa mnyamata wosamala, ndipo adaŵauza onsewo kuti, “Inu mutsogoleko, ndipo poyenda ndi magulu a zoŵeta, muzisiya mpata pakati pa gulu lililonse.” Adauza mnyamata woyamba kuti, “Mbale wanga Esau akakumana nawe ndi kukufunsa kuti, ‘Kodi mbuyako ndani? Nanga ukupita kuti? Nanga zoŵeta zili patsogolo pakozi nza yani?’ Iwe ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za mtumiki wanu Yakobe, ndipo akuzitumiza kwa inu mbuyake, kuti zikhale mphatso. Yakobe mwiniwake ali m'mbuyo mwathumu.’ ” Tsono adauzanso mnyamata wake wachiŵiri mau omwewo, ndi wachitatu, mpaka onse amene ankayenda motsogoza zoŵeta. Adaŵauza kuti, “Zimenezi ndizo mukauze Esau, mukakumana naye. Ataŵaona, adati, “Ili ndi gulu la ankhondo a Mulungu.” Motero malowo adaŵatcha Mahanaimu.
Mwadzidzidzi kudafika mngelo wa Ambuye ndipo kuŵala koti mbee kudaunika m'chipindamo. Mngeloyo adagunduza Petro m'nthitimu kuti amdzutse, ndipo adati, “Dzuka msanga!” Pompo maunyolo aja adakolopoka m'manja mwake.
Elisa adati, “Usachite mantha, pakuti amene ali pa mbali yathu ngambiri kupambana m'mene aliri iwoŵa.” Tsono Elisa adapemphera, adati, “Inu Chauta ndikukupemphani kuti mutsekule maso ake kuti apenye.” Motero Chauta adatsekula maso a wantchito uja, ndipo adangoona kuti phiri lili lodzaza ndi akavalo ndi magaleta amoto atamzungulira Elisa uja.
Koma usiku mngelo wa Ambuye adatsekula zitseko za ndendeyo naŵatulutsa. Adaŵauza kuti,
Akhale ngati mankhusu ouluka ndi mphepo, pamene mngelo wa Chauta akuŵapirikitsa. Njira yao ikhale yamdima ndi yoterera, pamene mngelo wa Chauta akuŵalondola.
Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula. Tamandani Chauta, inu magulu a ankhondo ake onse, atumiki ake ochita zimene Iye afuna.
Atatero adagona tulo patsinde pa kamtengo ka tsache pomwepo. Mwadzidzidzi mngelo adamkhudza namuuza kuti, “Dzuka, udye.” Eliya atapenya, adangoona kuti kumutu kwake kuli buledi wootcha pa makala, ndiponso mkhate wa madzi. Adadya, namwera, nkugonanso. Mngelo wa Chauta uja adabweranso kachiŵiri, namkhudza nati, “Dzuka, udye kuti ulendowu ungakukanike.”
Ndipo adalota akuwona makwerero ochoka pansi mpaka kukafika kumwamba. Angelo a Mulungu ankatsika ndi kumakwera pa makwererowo.
Apo mngelo wa Chauta uja adamuwonekera namuuza kuti, “Chauta ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.”
Chauta, Mulungu Wakumwamba, adanditenga kwathu m'banja mwa bambo wanga ndi m'dziko limene ndidabadwira, ndipo adandilonjeza molumbira kuti, ‘Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako.’ Chautayo adzatuma mngelo wake wokutsogolera, ndipo kumeneko udzamutengera mkazi mwana wanga.
Mngelo amene wandiwombola ku zoipa zonse, aŵadalitsenso! Podzera mwa anaŵa, dzina langa ndi maina a makolo anga Abrahamu ndi Isaki akhale omveka nthaŵi zonse! Adzakhale ndi ana ambiri iwoŵa, adzasanduke mtundu waukulu pa dziko lapansi!”
Kodi ukuyesa kuti Ine sindingapemphe Atate, Iwo nthaŵi yomweyo nkunditumizira magulu ankhondo a angelo oposa khumi ndi aŵiri?
Tsono munthu amene anaima pa timitengo tazitsamba uja anayankha kuti, ‘Ameneŵa ndiwo amene Chauta waŵatuma kuti ayendere dziko lapansi.’ Ndipo onsewo anauza mngelo wa Chauta amene anaima pakati pa timitengo tazitsamba uja, kuti, ‘Tayendera dziko lapansi, ndipo anthu onse ali pa mtendere, akupumula.’
Apo mngelo wa Mulungu, yemwe ankatsogolera Aisraele aja, adakakhala cha kumbuyo kwao. Mtambo womwe unkakhala patsogolo pao uja, udakakhalanso chakumbuyo kwao.
Ambuye adafika ku malo ao oyera kuchokera ku Sinai, ali ndi magaleta amphamvu zikwi zambirimbiri.
Usiku womwe wathawu kunandibwerera mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake, ndipo amene ndimamlemekeza. Mngeloyo anandiwuza kuti, ‘Usachite mantha, Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Mfumu ya ku Roma. Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, walola kuti anzako onse aulendo akhale moyo.’
Titalira kwa Chauta, adamva kulira kwathu, natuma mngelo amene adatitulutsa m'dziko la Ejipitolo. Tsopano tili kuno ku Kadesi, mzinda umene uli m'malire a dziko lanu.
Mngelo wa Chauta adamuwonekera mkaziyo namuuza kuti, “Inu mai, ngakhale mpaka pano muli opanda ana, komabe mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Ndiye inu mudzisamale bwino, musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chilichonse chosaloledwa. Pakuti ndithu mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa, kumutu kwake kusadzapite lumo, pakuti mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulikira Mulungu kuyambira tsiku la kubadwa kwake. Ndipo adzayambapo ntchito yopulumutsa Aisraele kwa Afilisti.” Tsono mkaziyo adadzauza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kuno, ndipo nkhope yake inali yoopsa kwambiri ngati nkhope ya mngelo wa Mulungu. Sindidamufunse kumene akuchokera, iyenso sadandiwuze dzina lake.
Adzapulumutsa moyo wanga pa nkhondo imene ndikumenya, pakuti anthu ambiri akukangana nane.
Tsono mngelo wa Ambuye adaonekera Zakariya. Mngeloyo adaaimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizirapo lubani. Zakariya adadzidzimuka pomuwona, nachita mantha. Koma mngeloyo adamuuza kuti, “Usaope, Zakariya, Mulungu wamva pemphero lako. Mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
Elizabeti ali ndi pathupi pa miyezi isanu ndi umodzi, Mulungu adatuma mngelo Gabriele ku mudzi wina wa ku Galileya, dzina lake Nazarete. Adamtuma kwa namwali wina wosadziŵa mwamuna amene anali atafunsidwa mbeta ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la mfumu Davide. Namwaliyo dzina lake anali Maria. Mngelo uja adadza kwa iye nati, “Moni, inu amene Mulungu wakukomerani mtima kotheratu. Ambuye ali nanu.”
Mngelo wa Ambuye adauza Filipo kuti, “Nyamuka, pita chakumwera, kutsata mseu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu; mseu wodzera m'chipululu uja.”
Buku lino likufotokoza zimene Yesu Khristu adaulula. Mulungu adampatsa zimenezi kuti aonetse atumiki a Mulunguyo zomwe zikuyenera kudzachitika posachedwa. Khristu pofuna kudziŵitsa zinthuzo mtumiki wake Yohane, adachita kutuma mngelo wake kwa iye.
Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona namtindi wa angelo zikwizikwi pozungulira mpando wachifumu uja, Zamoyo zinai zija ndi Akuluakulu aja. Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti, “Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.”
Davide adakweza maso ake naona mngelo wa Chautayo ataimirira pakati pa dziko lapansi ndi dziko lakumwamba, m'manja mwake ali ndi lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Tsono Davide, pamodzi ndi akuluakulu omwe, atavala ziguduli, adadzigwetsa choŵerama pansi.
Choncho ine mdzakazi wanu ndidaaganiza kuti mau anu mbuyanga mfumu adzandipulumutsa, poti inu muli ngati mngelo wa Mulungu, podziŵa zabwino ndi zoipa. Chauta Mulungu wanu akhale nanu.”
Tsiku lina dzuŵa litapendeka, nthaŵi ili ngati 3 koloko, adaona zinthu m'masomphenya. Adaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu akubwera kwa iye nkunena kuti, “Kornelio!” Kornelio adati, “Dzana ilo, ndinkapemphera m'nyumba mwanga, nthaŵi ngati yomwe ino ya 3 koloko dzuŵa litapendeka. Mwadzidzidzi kutsogolo kwangaku kudaimirira munthu wovala zovala zonyezimira. Adandiwuza kuti, ‘Kornelio, Mulungu wamva pemphero lako, ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo. Tsono tuma anthu ku Yopa akaitane Simoni wotchedwa Petro. Iyeyu akukhala kwa Simoni, mmisiri wa zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa njanja.’ Nchifukwa chake ndidaakutumirani anthu msanga, ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akulamulani kuti munene.” Petro adayamba kulankhula, adati, “Zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. Amalandira bwino munthu wa mtundu uliwonse womuwopa nkumachita chilungamo. Mukudziŵa kuti adatumizira Aisraele mau ake naŵauza Uthenga Wabwino wa mtendere kudzera mwa Yesu Khristu, amene ali Ambuye a anthu onse. Mukudziŵa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthaŵi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana. Ife ndife mboni za zonse zimene Iye adachita mu Yerusalemu ndi m'dziko lonse la Ayuda. Iwo adamupha pakumpachika pa mtanda. Iye adayang'anitsitsa mngeloyo mantha atamgwira, ndipo adamufunsa kuti, “Nkwabwino, Ambuye?” Mngeloyo adati, “Mulungu wakondwera nawo mapemphero ako ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo zako.
Onsewo adapitirira gulu loyamba la asilikali aja, kenaka lachiŵiri, mpaka kukafika pa chitseko chachitsulo cha pa chipata choloŵera mu mzinda. Chitsekocho chidangodzitsekukira chokha, iwowo nkutuluka. Adayenda ndithu mu mseu wina wamumzindamo. Atafika polekezera pake mngelo uja adamchokera. Pamenepo Petro adadzidzimuka nati, “Tsopano ndikudziŵadi kuti Ambuye anatuma mngelo wao ndipo andipulumutsa kwa Herode, ndi ku zoipa zonse zimene Ayuda ankayembekeza kuti zidzandichitikira.”
Motero anthu adadya buledi wa angelo, ndipo Mulungu adaŵatumizira chakudya chochuluka.
Koma pataoneka mngelo, ngati mthandizi, mmodzi mwa ambirimbiri otere, wodzamkumbutsa zimene zili zoyenera, ngati mngeloyo amkomera mtima, nati, ‘Mpulumutseni kuti asapite ku manda, dipo lake nali,’
Adavutika poona mavuto ao onse, Mngelo wochokera kwa Iye adaŵapulumutsa. Adaŵaombola mwa chikondi ndi chifundo chake. Wakhala akuŵasamala ngati ana kuyambira kale.
Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.” Maonekedwe ake anali ngati a mphezi, ndipo chovala chake chinali choyera chambee.
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Pambuyo pake ndidaona mngelo wina akuuluka mu mlengalenga. Anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalike kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa anthu a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, ndi a chilankhulo chilichonse.
Mundikhalire thanthwe lothaŵirako, ndiponso linga lolimba lopulumukirako. Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
Tsono kudabuka nkhondo Kumwamba, Mikaele ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho pamodzi ndi angelo ake chidatengana nawo, koma onsewo adagonjetsedwa, mwakuti adataya malo ao Kumwamba. Chinjoka chachikulu chija chidagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakale ija yotchedwa “Mdyerekezi” ndiponso “Satana”, wonyenga anthu a pa dziko lonse lapansi. Chidagwetsedwa pa dziko lapansi pamodzi ndi angelo ake onse.
Atatero adagona tulo patsinde pa kamtengo ka tsache pomwepo. Mwadzidzidzi mngelo adamkhudza namuuza kuti, “Dzuka, udye.” Eliya atapenya, adangoona kuti kumutu kwake kuli buledi wootcha pa makala, ndiponso mkhate wa madzi. Adadya, namwera, nkugonanso. Mngelo wa Chauta uja adabweranso kachiŵiri, namkhudza nati, “Dzuka, udye kuti ulendowu ungakukanike.” Eliya uja adadzuka, nadya nkumwera. Motero adapeza mphamvu zoyendera. Adayenda masiku makumi anai usana ndi usiku mpaka adakafika ku Sinai, phiri la Mulungu.
Pamwamba pao padaaimirira Aserafi. Aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: aŵiri ophimbira kumaso, aŵiri ophimbira mapazi, aŵiri oulukira. Aserafiwo ankafuulirana kuti, “Ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse, ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi.”
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake kudzachotsa mu Ufumu wake anthu onse ochimwitsa anzao, ndi ena onse ochita zoipa,
Tsiku limenelo Chauta adzakhala ngati chishango chotchinjiriza anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti anthu ofooka kwambiri mwa iwo adzakhala amphamvu ngati mfumu Davide. Tsono banja la Davide lidzakhala lolamulira zonse ngati Mulungu, ngati mngelo wa Chauta woŵatsogolera.
Ndine, Yohane, amene ndidamva ndi kuwona zimenezi. Ndipo nditazimva ndi kuziwona, ndidadzigwetsa ku mapazi a mngelo uja amene adandiwonetsa zimenezi. Ndidaati ndimpembedze, koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ngati abale ako aneneri, ndiponso ngati onse otsata mau olembedwa m'buku lino. Iwe pembedza Mulungu.”
Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Pambuyo pake ndidaona mngelo akutsika kuchokera Kumwamba. M'manja mwake anali ndi kiyi ya Chiphompho chija, ndiponso unyolo waukulu.
“Mngelo wanga adzapita patsogolo panu, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Aamori, Ahiti, Aperizi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzaŵaononga onsewo.
Angelo onse adaimirira kuzungulira mpando wachifumu uja, kuzunguliranso Akuluakulu aja ndi Zamoyo zinai zija. Angelowo adadzigwetsa chafufumimba patsogolo pa mpando wachifumuwo, napembedza Mulungu.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Mngelo wa Chauta adamuwonekera ngati malaŵi a moto umene unkayaka m'chitsamba. Mose atapenya, adaona kuti chitsamba chili moto laŵilaŵi, koma osapsa.
Pomwepo Chauta adatsekula maso a Balamu, ndipo adaona mngelo wa Chauta ataimirira m'njira, atasolola lupanga m'manja mwake. Tsono Balamu adazyolika, nadziponya pansi.
Angelo aŵiri aja adaloŵa m'Sodomumo madzulo ndi kachisisira, Loti atakhala pafupi ndi chipata cha mzindawo. Tsono Lotiyo atangoŵaona anthuwo, adaimirira nakaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu, nati, Koma anthu aŵiri anali m'kati aja adamkokera Lotiyo m'nyumba, natseka chitseko. Kenaka adaŵachititsa khungu anthu onse amene adaaima pabwalowo, achinyamata ndi okalamba omwe, kotero kuti sadathenso kuwona khomo. Anthu aŵiriwo adafunsa Loti kuti, “Kodi aliponso wina aliyense amene uli naye kuno? Tenga ana ako aamuna, ana ako aakazi, akamwini ako ndi wina aliyense wachibale amene ali mumzinda muno, mutuluke, chifukwa ife tikuti tiwononge malo ano. Chauta waziona zoipa zonse zimene anthu okhala mumzinda muno akuchita, ndipo tatumidwa kuti tiuwononge mzindawu.” Pamenepo Loti adapita kwa anyamata amene ankafuna kukwatira ana akewo naŵauza kuti, “Fulumirani, tiyeni tituluke kuno, chifukwa patsala pang'ono kuti Chauta aononge malo ano.” Koma iwowo ankangoyesa nthabwala chabe. M'mamaŵa, angelo aja adayesa kumufulumizitsa Loti namuuza kuti, “Fulumira! Iweyo ndi mkazi wako ndi ana ako aakazi aŵiri, mutuluke kupita kunja kwa mzinda, kuti mupulumutse moyo wanu pamene mzinda uno ukukaonongedwa.” Koma Loti ankakayikabe, tsono Chauta adamumvera chifundo. Motero anthuwo adatenga Loti, mkazi wake ndi ana ake aŵiri aja moŵagwira pa dzanja, naŵatulutsa mumzindamo, nkuŵasiya panja pomwepo. Ataŵatulutsira kunja kwa mzindawo, mmodzi mwa angelowo adati, “Thamangani, mupulumutse moyo wanu. Musacheukire m'mbuyo, ndipo musaime m'chigwamo. Thaŵirani ku mapiri kuti mungaphedwe.” Koma Loti adamuyankha kuti, “Iyai mbuyanga musatero. Mwandikomera mtima kwambiri pakupulumutsa moyo wanga. Komatu mapiriwo ali patali kwambiri. Kuwonongeka kwa malo ano mwanenaku kuchitika ine ndisanafike kumapiriko, ndipo ndifa. “Chonde ambuye anga, tiyeni mukafike kunyumba, mukatsuke mapazi ndi kugona komweko. M'maŵa kukacha, mungathe kupitirira ndi ulendo wanu.” Koma iwo adayankha kuti, “Iyai, ife tigona panja mumzinda mommuno.”
kodi pabwere zaka zitatu za njala, kapena inu mukhale miyezi itatu akukukanthani adani anu namakukugonjetsani pa nkhondo, kapena pagwe mliri wa masiku atatu m'dzikomo pamene Chauta adzakukanthani ndi lupanga, ndipo mngelo wa Chauta adzawononga zinthu m'dziko lonse la Israele.’ Tsono tsimikizani choti ndikamuyankhe amene adanditumayo.” Apo Davide adauza Gadi kuti, “Ine pamenepa ine ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka ndigwe m'manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu. Koma chonde ndisagwe m'manja mwa anthu ayi.” Motero Chauta adatumiza mliri pa Aisraele, mwakuti adafapo Aisraele okwanira 70,000. Ndipo Mulungu adamtumadi mngelo uja kukaononga Yerusalemu. Koma pamene ankati aziwononga kumene, Chauta adaona namva chisoni, osafunanso kuchita choipacho. Choncho adauza mngelo woonongayo kuti, “Iyai, basi tsopano! Kwakwanira, bweza dzanja lakolo.” Nthaŵi imeneyo nkuti mngelo wa Chauta uja ataima pa malo opunthira tirigu a Orinani Myebusi. Davide adakweza maso ake naona mngelo wa Chautayo ataimirira pakati pa dziko lapansi ndi dziko lakumwamba, m'manja mwake ali ndi lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Tsono Davide, pamodzi ndi akuluakulu omwe, atavala ziguduli, adadzigwetsa choŵerama pansi.
Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuwonekera m'maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.
Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni.’ Ndiponso, “ ‘Iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ”
Koma inu amene mukusauka tsopano, adzakupatsani mpumulo pamodzi ndi ife tomwe. Adzachita zimenezi, Ambuye Yesu akadzabwera kuchokera Kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Akadali othedwa nzeru choncho pa zimenezo, adangoona anthu aŵiri ovala zovala zonyezimira ataimirira pafupi ndi iwo. Atanena zimenezi adaŵaonetsa manja ake ndi mapazi ake. Iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe, ndipo adaathedwa nzeru. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi pano muli nako kanthu kakudya?” Adampatsa chidutsu cha nsomba yootcha. Iye atalandira nsombayo, adaidya iwo akuwona. Kenaka adaŵauza kuti, “Nzimenezitu zimene ndinkakuuzani pamene ndinali nanu. Paja ndinkanena kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m'Malamulo a Mose, m'mabuku a aneneri, ndi m'buku la Masalimo.” Tsono adaŵathandiza kuti amvetse bwino Malembo. Adaŵauza kuti, “Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zoŵaŵa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao. Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi. Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera Kumwamba.” Akazi aja adachita mantha naŵeramitsa nkhope zao pansi. Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Mukudzafuniranji munthu wamoyo pakati pa anthu akufa?
Kanthaŵi pang'ono mudamsandutsa wochepera kwa angelo. Mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu,
Ndiye usiku umenewo mngelo wa Chauta adapita ku zithando zankhondo za Aasiriya naphako asilikali 185,000. M'maŵa mwake adangoona asilikaliwo ali ngundangunda, atafa onsewo.
Tsono iye adandiwuza kuti ndidziŵitse Zerubabele uthenga wa Chauta wakuti, “Inde udzapambana, koma osati ndi nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi mzimu wanga. Kodi iwe phiri lalitali, ndiwenso chiyani? Udzasanduka dziko losalala pamaso pa Zerubabele. Ndipo akadzabwera nawo mwala wotsiriza wa pa Nyumba yanga, namauika pamwamba, anthu adzafuula kuti, ‘Ati kukongola ati!’ ”
Mngelo wina adabwera naimirira ku guwa lansembe ali ndi chofukizira chagolide. Adapatsidwa lubani wambiri kuti ampereke pamodzi ndi mapemphero a anthu a Mulungu pa guwa lagolide patsogolo pa mpando wachifumu uja. Pamodzi ndi mapemphero a anthu a Mulunguwo, utsi wa lubaniyo udakwera pamaso pa Mulungu kuchokera m'manja mwa mngelo uja.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Paja Chauta amaimirira pafupi ndi munthu wosoŵa, amafuna kumpulumutsa kwa anthu ogamula kuti iyeyo aphedwe.
Koma ngakhale Mikaele yemwe, mkulu wa angelo, pamene iye ankakangana ndi Satana ndi kutsutsana naye za mtembo wa Mose, sadafune kutchuliliza mwachipongwe kuti ndi wolakwa. Adangoti, “Ambuye akulange!”
Kudzamveka lipenga lamphamvu, ndipo Iye adzatuma angelo ake, kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”
Koma pamene ankatuma Mwana wake wachisamba pansi pano, Mulungu adati, “Angelo onse a Mulungu azimpembedza.”
Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo.
Mulungu adamumva mwanayo akulira, ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba, adati, “Kodi iwe Hagara, chikukuvuta nchiyani? Usachite mantha. Mulungu wamva kulira kwa mwanayu.
Mngeloyo adayankha kuti, “Mzimu Woyera adzakutsikirani, ndipo mphamvu za Mulungu Wopambanazonse zidzakuphimbani. Nchifukwa chake Mwana wodzabadwayo adzakhala Woyera, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu. “Onani, mbale wanu uja Elizabeti, nayenso akuyembekezera mwana wamwamuna mu ukalamba wake. Anthu amati ngwosabala, komabe uno ndi mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.”
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse.
Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani? Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize. Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana.
M'mamaŵa, angelo aja adayesa kumufulumizitsa Loti namuuza kuti, “Fulumira! Iweyo ndi mkazi wako ndi ana ako aakazi aŵiri, mutuluke kupita kunja kwa mzinda, kuti mupulumutse moyo wanu pamene mzinda uno ukukaonongedwa.” Koma Loti ankakayikabe, tsono Chauta adamumvera chifundo. Motero anthuwo adatenga Loti, mkazi wake ndi ana ake aŵiri aja moŵagwira pa dzanja, naŵatulutsa mumzindamo, nkuŵasiya panja pomwepo.
Koma tsopano ndikukuuzani kuti mulimbe mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene atayike, koma chombo chokha ndiye chiwonongeke. Usiku womwe wathawu kunandibwerera mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake, ndipo amene ndimamlemekeza. Mngeloyo anandiwuza kuti, ‘Usachite mantha, Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Mfumu ya ku Roma. Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, walola kuti anzako onse aulendo akhale moyo.’
Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku, kapena nkhondo nthaŵi yamasana. Sudzaopanso mliri wogwa usiku, kapena zoononga moyo masana.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Sadzalola phazi lako kuti literereke, Iye amene amakusunga sadzaodzera. Zoonadi, amene amasunga Israele, ndithu sadzaodzera kapena kugona.
Ndipo za angelo Mulungu adati, “Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo, atumiki ake amaŵasandutsa malaŵi a moto.”
Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndaikapo alonda, usana wonse ndi usiku wonse sadzakhala chete. Inu amene mumakumbutsa Chauta za malonjezo ake, musapumule.
Nthaŵi yamasana Chauta ankaŵatsogolera ndi chipilala chamtambo namaŵalangiza njira. Ndipo nthaŵi yausiku, ankaŵatsogolera ndi chipilala chamoto, kuŵaunikira njira kuti aziyenda masana ndi usiku womwe. Nthaŵi zonse chipilala chamtambo chinkatsogolera anthu masana, ndipo chipilala chamoto chinkaŵatsogolera usiku.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa. Ndidzakuthokozani tsiku ndi tsiku, ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya. Onse amene amakonda Chauta, amaŵasunga, koma Chauta adzaononga oipa onse.
Usiku womwe wathawu kunandibwerera mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake, ndipo amene ndimamlemekeza.
Tchinjirizani moyo wanga ndi kundipulumutsa. Musalole kuti andichititse manyazi, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu. Kukhulupirika kwanga ndi kulungama kwanga kunditeteze, popeza kuti ndakukhulupirirani.
“Munthu wosauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m'manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m'manda.
Ndidaika mau anga m'kamwa mwanu, ndipo ndidakutetezani ndi dzanja langa. Ndidayalika zakuthambo, ndi kukhazika maziko a dziko lapansi. Ndidauza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ”
Chauta ndiye amene ali kothaŵirako ndipo pa dziko lapansili amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda, ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse.
Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.”
Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Apo ndidadzigwetsa ku mapazi ake kuti ndimpembedze. Koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ndiponso ngati abale ako amene amachitira Yesu umboni. Iwe pembedza Mulungu.” Pajatu kuchitira Yesu umboni ndiye thima la uneneri.
Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Koma ulendo uno simudzachoka mofulumira, simudzachita chothaŵa. Chauta azidzayenda patsogolo panu, Mulungu wa Aisraele azidzakutetezani kumbuyo kwanu.
Suja Inu mwakhala mukumteteza ponseponse iye uja, pamodzi ndi banja lake ndi zinthu zake zonse zimene ali nazo. Mudamdalitsanso pa ntchito zimene amachita, ndipo chuma chake nchochuluka kwambiri m'dzikomo.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
mwadzidzidzi adangoona anthu atatu ataimirira potero. Atangoŵaona, adanyamuka mwamsanga kukaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu,
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.
Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.
Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.
Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.
Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza.
“Mukatero, mudzaŵala ngati mbandakucha, ndipo mabala anu adzapola msanga. Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani, ndipo ulemerero wanga udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu.
“Khalani amphamvu, limbani mtima. Musati muwope kapena kutaya mtima pamaso pa mfumu ya ku Asiriya ndi chigulu chankhondo chimene ali nachochi. Iyeyo ali ndi gulu lankhondo la anthu, koma ife tili ndi Chauta, Mulungu wathu, wotithandiza ndi wotimenyera nkhondo zathu.” Apo anthuwo adakhulupirira mau a Hezekiya mfumu ya ku Yuda.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Usamaopa zoopsa zobwera modzidzimutsa, usamachita mantha ndi tsoka lodzagwera anthu oipa. Chauta ndiye adzakhale chikhulupiriro chako, adzasunga phazi lako kuti lingakodwe.
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Inu Chauta, chiritseni ndipo ndidzachiradi. Pulumutseni ndipo ndidzapulumukadi. Ndinu amene ndimakutamandani.
Mundichitire chifundo Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti mtima wanga ukudalira Inu. Ndidzathaŵira pansi pa mapiko anu, mpaka chiwonongeko chitandipitirira.
Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.