Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


94 Mau a m'Baibulo Okhudza Miyambo Yachipembedzo Cha Santeria

94 Mau a m'Baibulo Okhudza Miyambo Yachipembedzo Cha Santeria


Masalimo 135:15-18

Mafano a mitundu ina ya anthu ndi asiliva ndi agolide chabe, ndi opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula, maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva, ndipo alibe mpweya m'kamwa mwao. Anthu amene amapanga mafanowo afanefane nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:4-5

“Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko. Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 14:6

“Nchifukwa chake uŵauze Aisraele kuti Ineyo Ambuye Chauta ndikunena kuti, ‘Lapani, mulekane nawo mafano anu. Muzisiye zonyansa zanu zonse.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:17

Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza, mwa iwo mulibe konse moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 32:4

Tsono Aroni adalandira golideyo kumanja kwa anthuwo, ndipo adamsungunula, napanga fano la mwanawang'ombe m'chikombole. Ndipo anthu adayamba kufuula kuti, “Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:5

Mumapembedza mafano pa mitengo ya thundu, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse. Mumapereka ana anu ngati nsembe m'zigwa, m'ming'alu yam'mathanthwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:14

Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza mwa iwo mulibe konse moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:19-20

Tsono tanthauzo la zimene ndikunenazi nchiyani? Kodi ndiye kuti nsembe yoperekedwa kwa fano nkanthu? Kapena kuti fanolo nkanthu? Motero mumtambomo ndi m'nyanjamo onsewo adachita ngati kubatizidwa ndi kukhala amodzi ndi Mose. Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 19:5

Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala, pamene amaperekapo ana ao kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala. Zimenezo sindidalamule konse, sindidazilankhule, ngakhale kuziganiza komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 32:35

Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala m'chigwa cha Benihinomu, kuti apereke ana ao aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Sindidalamule zimenezo ndine, ndipo sindidaganizeko kuti iwo nkuchita zonyansa zoterezi, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda pakutero.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 23:39

Adangoti atapereka ana ao nsembe kwa mafano ao, nthaŵi yomweyo nkuloŵa m'Nyumba yanga yoyera naiipitsa. Ndithu zimenezi nzimene adachita m'Nyumba mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 23:24

Masiku amenewo Yosiya adachotsanso anthu amaula, amatsenga, milungu ya m'nyumba ndiponso mafano ena onse, kudzanso zonyansa zonse zimene zinali ku dziko la Yuda ndi ku Yerusalemu. Adachita zimenezi kuti atsate Malamulo amene adalembedwa m'buku lomwe wansembe Hilikiya adalipeza m'Nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 1:4

“Ndidzasamula dzanja langa kuti ndilange anthu a m'dera la Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu. Ndidzafafaniziratu zotsalira zonse za Baala pa malo ano. Palibe aliyense amene adzakumbukirenso ansembe a fanolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 10:14

Pitani mukalirire milungu imene mwaisankhulayo. Ikupulumutseni milungu imeneyo pa nthaŵi ya kuzunzika kwanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 65:11

Koma inu amene mumakana Chauta, amene mumaiŵala phiri langa lopatulika, amene mumapembedza Gadi ndi Meni, milungu yobweretsa mwai ndi tsoka,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:15

Anthu a ku dziko limenelo, musadzachite nawo chipangano, chifukwa akamadziipitsa popembedza milungu yao nkumaiphera nsembe, kapena adzakuitanani kuti mudye nao chakudya cha nsembe zaozo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:18

“Munthu wamkazi wochita zaufiti, musamlole kuti akhale moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:31

“Musamapita kwa anthu olankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa anyanga. Musaŵafunefune kuti angakuipitseni. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:6

“Munthu akapita kwa wolankhula ndi mizimu yoipa ndi kwa wanyanga, nadziipitsa pakutsatira iwowo, ndidzamfulatira ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:27

“Mwamuna kapena mkazi wolankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena munthu wanyanga, ayenera kuphedwa. Aŵaponye miyala, ndipo magazi ao akhale pa iwowo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:10-12

Pakati panu pasadzapezeke wopereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto ngati nsembe. Pasaoneke munthu woombeza kapena woyeseza kulosa zam'tsogolo, kapena wogwiritsa ntchito nyanga kapena zithumwa. Pasapezekenso munthu wopempha nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Chauta, Mulungu wanu, amadana nawo anthu ochita zoipa zimenezi. Chimene Mulungu akupirikitsira anthuŵa pamene inu mukufika ndi chifukwa chakuti anthuwo ankachita zoipa zoterezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:3

“Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:29-31

Chauta, Mulungu wanu, akadzaononga mitundu ina imene mudzalanda dziko lao, inu mudzakhala ndi kukhazikika m'dzikomo. Mukagwetse maguwa ao, ndipo miyala yao yoimiritsa, imene amaiyesa yopembedzerapo, mukaiphwanyephwanye. Mukatenthe mafano ao a Aserimu. Mukaonongenso mafano ao ofanizira milungu yao, ndipo mukafafanize ndi dzina lomwe la milunguyo konsekonse. Chauta ataiwononga mitunduyo inu mukuwona, mukachenjere kuti musakatsate zipembedzo zao. Musadzayese kufunsafunsa za milungu yao kuti, “Kodi mitundu ya anthu iyi imapembedza bwanji milungu yao, kuti ifenso tichite chimodzimodzi?” Musadzapembedze Chauta, Mulungu wanu, mofanafana ndi m'mene iwo amapembedzera milungu yaoyo. Iwo adachita zoipa zoopsa zambiri zimene Chauta amadana nazo, mpaka kutentha ana ao aamuna ndi aakazi pa moto pakuŵapereka kwa milungu yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 21:6

Pambuyo pake adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe. Ankatama mizimu mopemba ndiponso ankaombeza maula, namachita zobwebwetetsa ndi zaufiti. Adachita zoipa zambiri zimene zidakwiyitsa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 10:13

Choncho Saulo adafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake. Iyeyo anali wosakhulupirika kwa Chauta, poti sankamvera mau a Chauta ndiponso ankapempha nzeru kwa anthu olankhula ndi mizimu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 33:6

Ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza. Adachita zimenezi ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo ankachita zobwebwetetsa, namasamala zamalodza ndi zanyanga, nkumamvana ndi anthu olankhula ndi mizimu ndi anthu amatsenga. Adachita zoipa zambiri pamaso pa Chauta, naputa mkwiyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 5:12

Ndidzasakaza masenga anu onse, ndipo pakati panu sipadzakhalanso oombeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 8:19

Tsono anthu akakuuzani kuti, “Kafunseni kwa olankhula ndi mizimu ndi kwa olosa amene amatulutsa liwu loti psepsepse ndi kumang'ung'udza.” Kodi anthu sayenera kupempha nzeru kwa milungu yao? Kodi sungapite kwa anthu akufa kukapemphera nzeru anthu amoyo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:25

Ndine amene ndimalepheretsa mipingu ya anthu onama, ndi kupusitsa anthu oombeza ula. Ndine amene ndimatsutsa mau a anthu anzeru, ndi kuŵaonetsa kuti nzeru zao nzopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 27:9

“Nchifukwa chake musaŵamvere aneneri anu, oombeza anu, otanthauza maloto, amaula ndi amatsenga anu, akamakuuzani kuti musadzatumikire mfumu ya ku Babiloni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:2

Chauta akuti, “Musatsate makhalidwe a anthu a mitundu ina. Musachite mantha ndi zizindikiro zozizwitsa zamumlengalenga, ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 13:18

Uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu zakumutu za anthu a misinkhu yosiyanasiyana, kuti azikola mitima ya anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nkupulumutsa moyo wanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 13:20

“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Ndikuzikana zithumwa zanu zapamkono, zimene mumakolera mitima ya anthu ngati mukukola mbalame. Ndidzazithothola pa mikono yanu, kuti ndiŵapulumutse anthuwo amene mumaŵakola ngati mbalame.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 10:2

Paja mafano am'nyumba amalankhula zonama, ndipo oombeza maula amaona zabodza. Olota maloto amalota zabodza, ndipo mau ao othuzitsa mtima ndi nkhambakamwa chabe. Motero anthu amangoyenda uku ndi uku ngati nkhosa, amazunzika chifukwa chosoŵa mbusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:28

Anthuwo adayamba kupembedzanso Baala wa ku Peori, ndi kumadya nawo nsembe zoperekedwa kwa anthu akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:5

Paja milungu yonse ya mitundu ina ya anthu ndi mafano chabe. Koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-20

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:8

Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:15

Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:10

nati, “Iwe mwana wa Satana, mdani wa chilungamo, wa mtima wa kunyenga kulikonse ndi kuchenjeretsa kwamtundumtundu, udzaleka liti kupotoza njira zolungama za Ambuye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:19

Ambiri amene ankakonda kuchita matsenga, adasonkhanitsa mabuku ao naŵatentha pamaso pa anthu onse. Pamene adaonkhetsa mtengo wa mabukuwo, adapeza kuti udaakwanira ngati ndalama zikwi makumi asanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:23

Mwa iwe simudzaonekanso konse kuŵala kwa nyale. Mwa iwe simudzamvekanso konse mau a mkwati wamwamuna kapena wamkazi. Amalonda anali anthu otchuka kwambiri aja a pa dziko lapansi. Unkanyenga anthu a mitundu yonse ndi maula ako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 7:11

Zitatero Farao adaitana anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo iwowo adachitanso zomwezo mwa matsenga ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:19

Musamale kuti mukapenya ku thambo nkuwona dzuŵa, mwezi, nyenyezi ndi zonse zakuthamboko, mtima wanu usakopeke nkuyamba kupembedza ndi kutumikira zinthu zimene Mulungu wanu wapatsa anthu ena onse a pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 47:12-13

Khala nazo nyanga zako ndi matsenga ako. Wakhala ukuzigwiritsa ntchito chiyambire cha ubwana wako. Mwina mwake zingakuthandize kapena nkuwopsa nazo adani ako. Udangodzitopetsa nako kupempha malangizo ambiri. Nabwere okulangizawo kuti adzakupulumutse. Abweretu anthu amene amaphunzira zakumlengalenga, namayang'ana nyenyezi, amenenso amati mwezi ukakhala nkumalosa zimene zidzakuchitikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nahumu 3:4

Zonsezo zachitika chifukwa cha zonyansa zochuluka za Ninive, mkazi wachiwerewere uja. Ankakopa anthu ndi kukongola kwake konyenga. Ankanyengadi anthu a mitundu yonse ndi zadama zake nakopa mafuko ndi zithumwa zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 15:23

Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 33:3

Adayambitsanso akachisi amene bambo wake Hezekiya adaaŵaononga. Adapanganso maguwa a Abaala ndiponso mafano, namapembedza zinthu zonse zamumlengalenga, ndi kumazitumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:6

Inu Mulungu, mwakana anthu anu, zidzukulu za Yakobe. Dziko ladzaza ndi anthu amatsenga akuvuma, ladzazanso ndi olosa a ku Filistiya. Anthu anu akuchita nao miyambo yachilendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 4:12

Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo, ndipo amaombeza ndi ndodo yao. Mzimu wonyansa waasokeretsa, motero posiya Mulungu wao, akhala osakhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 5:26

Ndipotu muzidzanyamula Sakuti, mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene mudadzipangira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 17:17

Anthuwo adapereka ngati nsembe ana ao aamuna ndi ana ao aakazi, ndipo ankaombeza maula, namachitanso zanyanga. Adadzipereka kuti azichita zoipa zochimwira Chauta, namkwiyitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 14:14

Koma Chauta adandiyankha kuti, “Zakuti aneneriwo amalosa m'dzina langa, ili ndi bodza. Ine sindidaŵasankhe, sindidaŵatume kapena kulankhula nawo. Iwo amakuloserani zinthu zonama zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amaombeza zabodza, zimene amalankhula ndi zonyenga zopeka iwo eni ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 21:21

Mfumu ya ku Babiloni yaima ku njira pa mphambano ya miseu. Ikuwombeza maula ndi mivi kuti ipeze njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake, ndipo ikuyang'ana chiŵindi cha nyama yopereka ku nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 22:28

Ndipo aneneri ake abisa zimenezi monga muja amachitira anthu popaka njereza, amaziphimba ndi zimene amaona m'maloto ao abodza ndi m'maula ao onama. Amati, ‘Ambuye Chauta akunena zakutizakuti,’ pamene Ine Chauta sindidalankhule konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 18:21

Eliya adasendera pafupi ndi anthu onsewo, naŵafunsa kuti, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iŵiri mpaka liti? Ngati Chauta ndiye Mulungu, mtsateni. Koma ngati Baala ndiye Mulungu, tsatani iyeyo.” Anthuwo sadamuyankhe ndi liwu limodzi lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:37-38

Adapereka nsembe ana ao aamuna ndi aakazi kwa mizimu yoipa. Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 23:5

Yosiya adatulutsa ansembe a mafano amene mafumu a ku Yuda adaŵakhazika kuti azipereka nsembe ku akachisi ku mizinda ya m'dziko la Yuda ndi ku malo ozungulira Yerusalemu. Adatulutsanso amene ankapereka nsembe kwa Baala, kwa dzuŵa, kwa mwezi, kwa nyenyezi ndi kwa zinthu zonse zakuthambo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 23:23

Zanyanga sizingamchite kanthu Yakobe, zamaula sizingathe kulimbana ndi Israele. Tsono anthu polankhula za Yakobe ndi za Israele adzati, ‘Onani zimene Mulungu wachita.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 1:2-3

Tsiku lina mfumu Ahaziya ali ku likulu lake ku Samariya, adagwa kuchokera pa khonde la chipinda chake cham'mwamba, navulala kwambiri. Ndiye adatuma amithenga naŵauza kuti, “Pitani, mukafunse kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni, ngati nditi ndichire.” Koma mngelo wa Chauta adauza mneneri Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya, ukaŵafunse kuti, ‘Kodi ku Israele kulibe Mulungu, apa mukupita kukapempha nzeru kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni?’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:6

Chauta, Mfumu ndi Momboli wa Israele, Chauta Mphambe, akunena kuti, “Ine ndine woyamba ndi womaliza. Palibenso Mulungu wina, koma Ine ndekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 2:13

Anthu anga achita machimo aŵiri: andisiya Ine kasupe wa madzi opatsa moyo, adzikumbira okha zitsime, zitsime zake zong'aluka, zosatha kusunga madzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:5

Mafano aowo ali ngati kangamunthu woopsera mbalame m'munda wa minkhaka, sangathe nkulankhula komwe. Ayenera kuŵanyamula, poti sangayende okha. Musaŵaope, chifukwa sangakuchiteni choipa. Alibenso mphamvu zochitira zabwino.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 4:17

“Anthu a ku Efuremu aphathana ndi mafano, izo nzao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:4-7

Koma mafano ao ndi asiliva ndi agolide, opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula. Maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva. Mphuno ali nazo, koma sanunkhiza. Manja ali nawo, koma akakhudza, samva kanthu. Miyendo ali nayo, koma sayenda, ndipo satulutsa ndi liwu lomwe kukhosi kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:25

Mudzatenthe mafano ao ofanizira milungu yao. Musadzakhumbire siliva kapena golide amene iwo adapangira mafanowo. Musadzatengeko zimenezi kuti mungagwe mu msampha, popeza kuti zimenezo zimamnyansa Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 16:20

Kodi munthu nkudzipangira milungu yeniyeni? Atati apange, singakhale milungu konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:35-36

koma adasakanizana ndi mitundu inayo naphunzira kuchita zoipa zomwe anthu enawo ankachita. Adatumikira mafano ao amene adasanduka msampha kwa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:20

Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:20-21

Anthu ena onse otsala, amene sadaphedwe ndi miliri ija, sadatembenuke mtima kuti asiye ntchito za manja ao. Sadaleke kupembedza mizimu yoipa, ndi mafano agolide, asiliva, amkuŵa, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda. Anthuwo sadatembenukenso kuti aleke kupha anzao, ufiti, dama ndi kuba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:14

Tsono okondedwa anga, pewani kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:21

Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 28:7-8

Pamenepo Saulo adauza nduna zake kuti, “Mundifunire mkazi wolankhula ndi mizimu kuti ndipite kwa iyeyo, ndikapemphe nzeru.” Ndunazo zidamuuza kuti, “Ku Endori aliko mkazi wolankhula ndi mizimu.” Tsono Saulo adadzizimbaitsa, navala zovala zachilendo, napita. Pamodzi ndi anthu aŵiri adakafika kwa mkaziyo usiku. Ndipo adamuuza kuti, “Undifunsire zam'tsogolo kwa mizimu, makamaka undiitanire mzimu wa amene ndimtchule.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:14

Koma pali zinthu zingapo zoti ndikudzudzulireni. Kwanuko muli ndi anthu ena otsata chiphunzitso cha Balamu mneneri wonama uja. Iye uja adaaphunzitsa mfumu Balaki kukopa Aisraele kuti azidya za nsembe zoperekedwa kwa mafano, ndi kumachita chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 13:1-3

Mwina mneneri kapena womasulira maloto adzaoneka pakati panupo, namanena kuti adzachita chizindikiro kapena chozizwitsa, Mumuphe ndi miyala. Iye adati akusokeretseni, kuti musiyane ndi Mulungu wanu amene adakutulutsani ku dziko la Ejipito kumene mudaali kuukapolo kuja. Tsono Aisraele onse adzamva zimene zachitikazo nadzachita mantha, ndipo palibe wina pakati panu amene adzachitenso choipa choterechi. Pomakhala m'midzi imene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsaniyo, nthaŵi zina kapena mudzamva kuti anthu ena a mtundu wanu asokeretsa anthu m'mizinda yao yomwe. Akuŵapembedzetsa milungu imene inu simudaipembedzepo nkale lonse. Mbiri yoteroyo muifufuze bwino. Mukapeza kuti mbiriyo njoona, kuti chinthu choipa choterechi chidachitikadi, pompo muphe anthu onse amumzindamo pamodzi ndi zoŵeta zomwe. Muwononge mudzi umenewo kotheratu. Zinthu zonse za anthu a mu mzinda umenewo muzisonkhanitse pamodzi, ndipo muziwunjike pakati pa bwalo lalikulu la mzindawo. Tsono mutatero, muutenthe mzindawo pamodzi ndi zonse zam'menemo, kuti zikhale ngati nsembe yopsereza kwa Chauta, Mulungu wanu. Muusiye choncho kuti ukhale bwinja mpaka muyaya. Musagwireko kanthu kena kalikonse koyenera kuwonongedwa. Tsono Chauta adzaleka osakukwiyiraninso, adzakumverani chisoni ndipo adzakuchitirani chifundo, nadzakuchulukitsani monga adalonjezera makolo anu. Adzakuchitirani zimenezi mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, mukamatsata malamulo ake amene ndikukuuzani lero, ndipo mukamachita zolungama pamaso pa Chauta, Mulungu wanu. Chizindikirocho kapena chozizwitsacho chikachitikadi, iye nakuuzani kuti mupembedze ndi kutumikira milungu ina imene simudaipembedzepo nkale lonse, inu musamvere zimenezo. Chauta, Mulungu wanu, akulola zimenezo kuti akuyeseni, kuti aone ngati mumamkondadi ndi mtima wanu wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:8

Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:43-45

“Mzimu woipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo opanda madzi, kufunafuna malo opumulirako, koma osaŵapeza. Ndiye umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’ Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli zii, mosesasesa ndi mokonza bwino. Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iŵiri yoipa koposa uwowo, kenaka yonseyo imaloŵa nkukhazikika momwemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba. Zidzateronso ndi anthu ochimwa amakono.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 17:12

Tsono adapembedza mafano kuchimwira Chauta amene anali ataŵauza kuti, “Musadzachite zimenezi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 8:4

Ndinene tsono za chakudya choperekedwa kwa mafano. Tikudziŵa kuti fano si kanthu konse, ndiponso kuti palibe mulungu wina, koma Mulungu mmodzi yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:21

Milungu yao yabodza ndachita nayo nsanje, mafano ao andikwiyitsa nawo. Inenso ndidzaŵachititsa nsanje pakusamalira mtundu wina wachabechabe, ndipo ndidzaŵapsetsa mtima pakukondera fuko lina lopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 6:9

Tsono opulumuka mwa inu adzandikumbuka pakati pa anthu a mitundu inayo, kumene adatengedwa ukapolo. Ndidzaŵamvetsa chisoni ndi manyazi chifukwa cha kusakhulupirika kuja ndi kundipandukira kuja, ndiponso chifukwa cha kuika mtima kwao pa mafano. Tsono adzachita nyansi ndi iwo eniakewo poona zoipa zonse zimene adachita, pamodzi ndi zochita zao zonyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:13

Mukamafuula kufuna chithandizo, mafano anuwo akupulumutseni! Mphepo idzaiyalula milunguyo, mpweya udzaiwulutsa. Koma amene amakhulupirira Ine, adzalandira dziko lokhalamo, ndi kumapembedza pa phiri langa loyera.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 7:3

Pamenepo Samuele adauza mtundu wonse wa Aisraele kuti, “Ngati mukubwerera kwa Chauta ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Aasitaroti pakati panu, mtima wanu ukhale pa Chauta ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero adzakupulumutsani kwa Afilisti.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 20:7

Ndidaŵauza onse kuti aliyense ataye zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo, ndipo asadziipitse ndi mafano a ku Ejipito. Ine ndine Chauta Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:14

Anthu amene mukukaŵalanda dziko limene mukakhalemolo, amatsata ndi kumvera amatsenga ndi oombeza. Koma inuyo Chauta, Mulungu wanu, sakulolani kuchita zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:6

Inu mumadana ndi opembedza mafano achabechabe. Koma ine ndimakhulupirira Inu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 13:2

Masiku ano akuchimwirachimwira. Akudzipangira mafano oumba pogwiritsa ntchito siliva wao. Mafano onsewo ndi ntchito ya anthu aluso. Amati, “Perekani nsembe kwa ameneŵa, pembedzani anaang'ombeŵa poŵampsompsona.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 20:16

Paja adakana malangizo anga, sadamvere malamulo anga, ndipo adaipitsa masiku anga a Sabata. Mtima wao udakonda kutsata mafano ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 23:49

Adzalangidwa chifukwa cha makhalidwe ao achiwerewere, ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo la kupembedza mafano. Tsono adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 11:16

Chenjerani, musasokeretsedwe ndi kutembenukira kwa milungu ina, kuti muziipembedza ndi kuitumikira,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:13

Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 8:10

Motero ndidaloŵa, ndipo pamakomapo ndidaonapo zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwaŵa pansi, za nyama zonyansa ndiponso za mafano ena onse amene Aisraele ankapembedza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:20

Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano asiliva ndi agolide, amene adaadzipangira kuti azipembedza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 14:9

Koma iwe wachita zoipa kupambana onse amene analipo kale, iwe usanakhale pa mpando waufumu, pakuti wadzipangira milungu ina ndiponso mafano osungunula. Pakutero wandipsetsa mtima kwabasi. Ineyo wanditayiratu kumbuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa