Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


76 Mau a Mulungu Oteteza Ku Zoipa

76 Mau a Mulungu Oteteza Ku Zoipa

Masalmo 68:20 amatiuza kuti Mulungu ndiye chipulumutso chathu, ndiye amene amatitulitsa ku imfa. Ngakhale mtsogolo mulibe chitsimikizo, kusankha mwanzeru kungatipatse moyo wautali.

Miyambo 13:14 imati nzeru ndiye chitsime cha moyo, ndipo imateteza otsatira ake ku misampha ya imfa. Baibulo limalonjeza mtsogolo mopanda imfa, koma pano padziko lapansi, ndikofunika kugwiritsa ntchito mpata umene Mulungu watipatsa, kukhala mogwirizana ndi malamulo ake, kusunga malamulo ake mumtima mwathu, ndikuzisinkhasinkha usana ndi usiku.

Moyo umenewu, woperekedwa ndi Yehova, umatipatsa mwayi wokhala padziko lapansi limene watipatsa, komanso m'nyumba zakumwamba zimene Atate wathu anakonzeratu. Popeza imfa siidziwika nthawi yake, ndikofunikira kukhala moyanjana ndi Mulungu ndi anansi athu, kufunafuna kuyera pamaso pa Ambuye nthawi zonse.

Motero Yehova adzatuma angelo ake kuti atiteteze ku zoopsa zonse, kuti tisapunthwe, chifukwa tamvera mawu ake. Osachita mantha, pakuti Mulungu adzakhala nafe, adzatikhutiritsa nthawi ya chilala, adzalimbitsa mafupa athu, ndi kutiphimba ndi kukhalapo kwake kwamuyaya.




Masalimo 118:18

Chauta wandilanga koopsa, koma sadandisiye kuti ndife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 13:14

Kodi ngati ndidzaŵapulumutsa kwa akufa? Kodi ngati ndidzaŵaombola ku imfa? Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? Anthu ameneŵa sindidzaŵachitiranso chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:28

Ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Mwana wa Munthu akubwera ndi ulemerero waufumu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:5

Pokhala ndi chikhulupiriro, Enoki adatengedwa kupita Kumwamba, osafa konse. Sadapezekenso, popeza kuti Mulungu adamtenga. Malembo amamchitira umboni kuti asanatengedwe, anali wokondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:13

Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa. Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe, kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu m'kuŵala kwa amoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:7-8

Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:11

Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 28:15

Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 41:2

Chauta adzamteteza ndi kumsunga ndi moyo. Adzatchedwa wodala pa dziko. Chauta sadzampereka kwa adani ake, kuti amchite zimene iwo akufuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:20

Mulungu wathu ndi Mulungu wotilanditsa, ndi Mulungu, Ambuye amene amatipulumutsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:2

Anthu amene ankayenda mumdima aona kuŵala kwakukulu. Amene ankakhala m'dziko la mdima wandiweyani, kuŵala kwaŵaonekera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:24

“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 25:8

Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m'maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:1-2

Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 5:11

Nchifukwa chake adaitananso akalonga onse a Afilisti kuti asonkhane, ndipo adati, “Chotsani Bokosili, ndipo mulibwezere kumene lidachokera, kuti lingatiphe ife pamodzi ndi anthu athu.” Pakuti munali mantha aakulu zedi mumzinda monsemo. Mulungu ankaŵalanga koopsa anthu akumeneko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:22

Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 18:32

Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:21

Pakuti monga imfa idadza pansi pano kudzera mwa munthu wina, momwemonso kuuka kwa akufa kudadza kudzera mwa munthu wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:28

Njira ya chilungamo imafikitsa ku moyo, koma njira ya zoipa imafikitsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:16

Anthu okhala mu mdima aona kuŵala kwakukulu. Anthu okhala m'dziko la mdima wabii wa imfa, kuŵala kwaŵaonekera.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:51

Ndithu ndikunenetsa kuti munthu akamvera mau anga, sadzafa konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:2

Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:12

Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 50:20

Inu mudaapangana kuti mundichite chiwembu, koma Mulungu adazisandutsa kuti zikhale zabwino ndipo kuti zipulumutse moyo wa anthu ambiri. Choncho onsewo ali moyo lero lino chifukwa cha zimenezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:17

Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:3-4

Ndiye Mulungu wanga ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga. Ndiye linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndinu amene mumandiwombola pa nkhondo. Ndi chithandizo chanu ndingathe kugonjetsa gulu la ankhondo. Ndi chithangato chanu, Inu Mulungu, ndingathe kupambana. Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye. “Palibe Mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha? Mulungu wathu ndiye linga langa lolimba, wandichotsera zoopsa m'njira zanga. Amalimbitsa mapazi anga ngati a mbaŵala, ndipo amandisunga bwino ku mapiri. Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo. Inu mwanditeteza ndi chishango chanu chachipulumutso. Mwandikweza ndi chithandizo chanu. Mwalimbitsa miyendo yanga kuti ndiyende bwino, choncho mapazi anga sadaterereke. Ndidalondola adani anga ndi kuŵapeza, sindidabwerere mpaka nditaŵagonjetsa. Ndidaŵakantha, ndidaŵagwetsa pansi, kotero kuti sadadzukenso, ndidaŵapondereza ndi mapazi anga. Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda, ndipo amandipulumutsa kwa adani anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:23

Kuwopa Chauta kumabweretsa moyo, ndipo amene amaopayo amakhala pabwino, ndiye kuti choipa sichidzamgwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:7

Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:11-12

Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:11

Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu: “Ngati tidafa pamodzi naye, tidzakhala moyonso pamodzi naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:7-8

Ndidzapita kuti, pofuna kupewa Mzimu wanu, kapena pofuna kuthaŵa nkhope yanu? Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko, ndikagona m'dziko la anthu akufa, Inu muli momwemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:28

Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:19

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1-2

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:5

Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:4

Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:4

Inu Chauta, tetezeni kwa anthu oipa, tchinjirizeni kwa anthu andeu, amene amaganiza zofuna kundigwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:1

Chauta akuthandize pa tsiku lamavuto. Mulungu wa Yakobe akuteteze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:20

Ndipo Mulungu amene amapatsa mtendere, posachedwa adzatswanya Satana pansi pa mapazi anu. Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:19

Wofunitsitsa chilungamo, adzakhala moyo. Koma wothamangira zoipa, adzafa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:7

Mngelo wa Chauta amatchinjiriza anthu omvera Iye, ndipo amaŵapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:3

Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:10

Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:18

Tikudziŵa kuti aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamsunga, ndipo Woipa uja sangamkhudze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1-3

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama, ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:6

Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:13

Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:4

Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:2

Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 5:19

Iye adzakupulumutsa ku masautso nthaŵi ndi nthaŵi. Zovuta sizidzakukhudza konse, zingachuluke bwanji.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:114

Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:16

“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:13

Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8-9

Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye. Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:5-6

Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku, kapena nkhondo nthaŵi yamasana. Sudzaopanso mliri wogwa usiku, kapena zoononga moyo masana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:3

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:10

zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:21

Adamkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi akuluakulu onse a Kumwamba, ndiponso pamwamba pa maina ena onse amene anthu angaŵatchule nthaŵi ino kapenanso nthaŵi ilikudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:11

Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 10:4

Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 97:10

Chauta amakonda anthu odana ndi zoipa. Iye amasunga moyo wa anthu ake oyera mtima. Amaŵapulumutsa kwa anthu oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:3-4

Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:7

Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:11

Inu amene mumaopa Chauta, mkhulupirireni. Chauta ndiye mthandizi wanu ndi chishango chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:4

Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:33

Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:2

Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wachikondi, ulemerero ndi ulemu zonse kwa Inu! Lero ndikuthokozani chifukwa cha chikondi chanu ndi chifundo chanu chachikulu. Zikomo chifukwa nthawi zonse mwakhala wabwino ndi kundizungulira ndi ubwino wanu. Zikomo chifukwa pakati pa imfa munamva kulira kwanga ndi pemphero langa. Ndinu Mulungu wokhulupirika ku mawu anu. Lero nditha kunena modzidalira kuti ngakhale nditayenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa chilichonse, chifukwa Inu mudzakhala nane. Ambuye, zikomo chifukwa munandipulutsa ku imfa yauzimu ndipo tsopano mwasunga moyo wanga kundipulumutsa ku imfa yakuthupi. Zikomo chifukwa nthawi zanga zili m'manja mwanu. Lero ndikudzudzula mzimu uliwonse wa imfa womwe ukundizinga. M'dzina lamphamvu la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa