Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


113 Mau a Mulungu Othamangitsira Ziwanda

113 Mau a Mulungu Othamangitsira Ziwanda

Ndili wokhulumela Ambuye, ndikukukumbutsa kuti choipa chilipodi mdziko lapansi. Ngakhale tili ndi chikhulupiriro chathu, tifunika kuzindikira kuti adani athu si maganizo a anthu okha, koma ndi mphamvu zenizeni zochokera mumdima. Baibulo limati: "Pakuti sitilimbana ndi anthu a thupi ndi mwazi, koma ndi maufumu, ndi maulamuliro, ndi olamulira a dziko lapansi la mdima, ndi mizimu yoipa m'malo akumwamba" (Aefeso 6:12). Satana ali ndi magulu a ziwanda omwe amachita chifuniro chake ndipo akugwira ntchito padziko lapansi pofuna kuwononga dongosolo la Mulungu.

Komabe, ndikofunikira kudziwa kuti Khristu wapatsa mpingo mphamvu pa mphamvu za mdima. Choncho, Mulungu akuyembekezera kuti anthu ake azikhala atcheru komanso olimba mtima poyang'anizana ndi gulu lankhondo la mdani, akuwalalatira m'dzina la Yesu, chifukwa palibe dzina lina padziko lapansi lamphamvu kuposa la Yesu wa Nazareti.




Marko 16:17

Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:25-26

Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye. Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kufuula ndi mau aakulu, unatuluka mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:18

Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:1

Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:12

kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:22

Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamchiritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:17-20

Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu. Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba. Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse. Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake. Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:1

Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:33

Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nkulowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:34

Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:21

Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:19

Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:39

Ndipo analowa m'masunagoge mwao mu Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:19

Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:18

Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:26

Ndipo pamene unafuula, numng'ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:12-13

Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo. Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:10-12

Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:31

Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:12

Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkuloleka kuchita zabwino tsiku la Sabata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 3:2

Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:9

Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbike mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:4

Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:15

atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:20

Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:28

Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 10:4-5

(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga); ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:4

amene anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m'nyengo ya pansi pano ino yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:17

Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:16

Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:14

Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:13

Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8-9

Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: ameneyo mumkanize okhazikika m'chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:14-15

Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi; nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:21-22

pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo ino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza; ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamutu pa zonse, kwa Mpingo

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:57

koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:7

Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7-8

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:36-37

Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka. Ndipo mbiri yake ya Iye inafalikira kumalo onse a dziko loyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:15-16

Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani? Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawagonjetsa onsewo, kotero kuti anathawa m'nyumba amaliseche ndi olasidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1-3

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso. Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi. Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu. Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja. Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu, nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:32-33

Ndipo pamene iwo analikutuluka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi chiwanda. Ndipo m'mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:18

Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19-20

Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:39

Pakuti mwandizingiza mphamvu m'chuuno ku nkhondoyo; mwandigonjetsera amene andiukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:1

Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:12

Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:32-34

Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m'chuuno, nakonza njira yanga ikhale yangwiro. Alinganiza mapazi anga ngati a mbawala, nandiimitsa pamsanje panga. Aphunzitsa manja anga agwire nkhondo; kuti walifuka uta wamkuwa ndi manja anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:31

Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo; koma wopulumutsa ndiye Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 2:14

Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:20

pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:29-30

Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse, Ndipo anawathira manja, nawaika m'ndende kufikira m'mawa; pakuti mpa madzulo pamenepo. m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:5

Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:25

Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:37

Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:6

Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18

Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:7

Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:18

Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:29

Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:20

Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:9

koma monga kulembedwa, Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve, nisizinalowe mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:6

ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Khristu Yesu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:14

Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:13

amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:13

Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1

Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:9

Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:16-18

Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29

Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:13

Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:114

Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:18

Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:14

Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamgonjetsa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 12:5

Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:23

tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:14

Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:13

Dikirani, chilimikani m'chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 44:5

Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe, m'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:28

Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni: Mundilimbitse monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:12

Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:19-20

Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoze bwanji kuchitulutsa? ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala. Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:1

Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:16

Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:1

Auke Mulungu, abalalike adani ake; iwonso akumuda athawe pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:1-3

Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo. Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa. Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa mmodzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale. Ndi kuti, Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuimbirani. Ndiponso, Ndidzamtama Iye. Ndiponso, Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa. Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi; nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo. Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbeu ya Abrahamu. Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu. Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa. Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama, tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:155

Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:14

M'chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:18

Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:1-2

Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye. Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu. Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri, kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu. Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:14-15

Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:27

ndiponso musampatse malo mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:15

Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:3

Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:12

Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:7

Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wamphamvu Zonse! Ndikubwera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu, Inu nokha ndinu Woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kwakukulu. Atate Woyera, zikomo chifukwa munabwera padziko lapansi kudzawononga ntchito za mdima ndi kumasula onse omwe ali m'ndende ya satana ndipo m'dzina lanu mwandipatsa Mphamvu ndi ulamuliro pa mizimu yoipa. Mawu anu amati: “Ndipo zizindikiro izi zidzatsata okhulupirira: M’dzina langa adzatulitsa ziwanda; adzalankhula malilime atsopano.” Ndikukupemphani mundithandize kugonjetsa mantha, kuphunzira kuyenda mu ulamuliro ndikugwiritsa ntchito mphamvu zomwe munandipatsa kale pa dziko la mdima chifukwa munagonjetsa satana ndi ziwanda zake zonse. Ndithandizeni kukhala moyo wogwirizana ndi chifuniro chanu, kumamatira kwambiri mawu anu, osasiya zitseko zotseguka kwa mdani m'moyo wanga kapena wa banja langa. Mundidziwitse kuti kukhala ndi moyo wopemphera ndi wodzaza ndi kukhalapo kwa Mzimu Woyera ndiyo chitsimikizo chokha cha chipambano changa. Mumawonetsa m'mawu anu: “Chifukwa chake, gonjerani kwa Mulungu; tsutsani mdierekezi, ndipo adzathawa kwa inu.” Ambuye, ndikupemphani kuti mumasule ndi kubwezeretsa miyoyo ya anthu omwe pakali pano akukumana ndi vuto lililonse chifukwa cha matenda, zachuma kapena m'banja. Ndikupempherera iwo omwe ali m'ndende, omwe akuzunzidwa ndi mizimu yoipa, ndikudzudzula kuwukira kulikonse kwa mdani ndipo ndikuwalengeza kuti ali omasuka ku ukapolo uliwonse, chifukwa kumene kuli Mzimu wa Ambuye kuli ufulu. M’dzina lamphamvu la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa