Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 18:39 - Buku Lopatulika

39 Pakuti mwandizingiza mphamvu m'chuuno ku nkhondoyo; mwandigonjetsera amene andiukira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Pakuti mwandizingiza mphamvu m'chuuno ku nkhondoyo; mwandigonjetsera amene andiukira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Paja ndinu mudandipatsa mphamvu zomenyera nkhondo, ndinu mudandigonjetsera anthu ondiwukira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Inu munandiveka ndi mphamvu yokachitira nkhondo, munachititsa kuti ndigonjetse adani anga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:39
13 Mawu Ofanana  

Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? Sanakupumulitseni pambali ponse? Pakuti anapereka nzika za m'dziko m'dzanja mwanga, ndi dziko lagonjetsedwa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa anthu ake.


Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m'chuuno, nakonza njira yanga ikhale yangwiro.


Mphulupulu idzamupha woipa; ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.


Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.


Koma wondichimwira apweteka moyo wake; onse akundida ine akonda imfa.


Atero Yehova, Ntchito ya Ejipito, ndi malonda a Kusi, ndi a Seba, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.


Otilondola atigwira pakhosi pathu, tatopa osaona popumira.


Iye wondida Ine, adanso Atate wanga.


ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamutu pa zonse, kwa Mpingo


amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa