Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 12:29 - Buku Lopatulika

29 Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 “Palibe munthu amene angathe kuloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkufunkha chuma chake, atapanda kuyamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Atatero ndiye angafunkhe zam'nyumbamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 “Kapenanso wina aliyense angathe bwanji kulowa mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kunyamulamo zinthu zake, sipokhapo atayamba wamanga munthu wa mphamvuyo? Pamenepo iye akhoza kuba mʼnyumbamo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 12:29
11 Mawu Ofanana  

Kodi chofunkha chingalandidwe kwa wamphamvu, pena am'nsinga a woopsa angapulumutsidwe?


Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.


Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.


Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.


Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma ayambe wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwake.


iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.


Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa