Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 19:12 - Buku Lopatulika

12 kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anthu ankati akatenga zitambaya kapena nsalu zina zimene Paulo ankagwiritsa ntchito, nakaziika pa anthu odwala, odwalawo ankachira, ndipo mizimu yoipa inkatuluka mwa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kotero kuti mipango yopukutira thukuta ndi yovala pogwira ntchito, zomwe zinakhudza thupi la Paulo amapita nazo kwa odwala ndipo amachiritsidwa ndiponso mizimu yoyipa mwa iwo imatuluka.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 19:12
5 Mawu Ofanana  

Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;


kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa