Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Yohane 2:14 - Buku Lopatulika

14 Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamgonjetsa woipayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woipayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ana okondedwa, ndikukulemberani chifukwa mumawadziwa Atate. Abambo, ndikukulemberani chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi. Inu anyamata, ndikukulemberani chifukwa ndinu amphamvu. Mawu a Mulungu amakhala mwa inu ndipo mumamugonjetsa woyipayo.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 2:14
18 Mawu Ofanana  

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.


Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.


Ndipo mulibe mau ake okhala mwa inu; chifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo.


Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu;


Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamu; koma mufuna kundipha Ine, chifukwa mau anga alibe malo mwa inu.


Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,


Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.


Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'chisomo cha mwa Khristu Yesu.


Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:


Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiona m'maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mau a moyo,


Tikanena kuti sitidachimwe, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ake sakhala mwa ife.


Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.


chifukwa cha choonadi chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha:


Pakuti ndinakondwera kwakukulu, pofika abale ndi kuchita umboni za choonadi chako, monga umayenda m'choonadi.


ndipo uli nacho chipiriro, ndipo walola chifukwa cha dzina langa, wosalema.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa