Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 44:5 - Buku Lopatulika

5 Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe, m'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe, m'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndi thandizo lanu tidakantha adani athu. Ndi mphamvu zanu tidapondereza ogalukira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu; kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 44:5
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti.


Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.


M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.


Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima, ndipo Iye adzapondereza otisautsa.


Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.


Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.


Ndinaona nkhosa yamphongo ilikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pake; panalibenso wakulanditsa m'dzanja lake; koma inachita monga mwa chifuniro chake, nidzikulitsa.


Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzachita nkhondo, chifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzachitidwa manyazi.


Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.


Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa