Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 8:33 - Buku Lopatulika

33 Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nkulowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Iyo idatuluka, nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Ziwanda zija zitatuluka mwa munthuyo, zinakalowa mwa nkhumbazo, ndipo gulu lonselo linathamangira ku mtsetse ndi kukalowa mʼnyanja ndi kumira.

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:33
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi.


Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;


Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya m'phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola.


Ndipo akuwetawo m'mene anaona chimene chinachitika, anathawa, nauza okhala mumzinda ndi kuminda.


Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.


Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:


Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa