Baibulo limatilimbikitsa kuti tisaleke kusonkhana, tilimbikitsane wina ndi mnzake, makamaka pamene tikuyembekezera tsiku la Ambuye. Kusonkhana n’kofunika kwambiri pa zifukwa zosiyanasiyana.
Choyamba, ndi njira yolemekezera Mulungu ndi kumulambira pagulu. Baibulo limatiuza mu Aheberi 10:25 kuti: “Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mwachizoloŵezi cha ena, koma tilimbikitsane wina ndi mnzake, ndipo makamaka pamene mukuona kuti tsiku likuyandikira.”
Chachiwiri, kusonkhana kumatithandiza kukula mwauzimu. Tikamakumana ndi Akhristu anzathu, timatha kuphunzira kuchokera ku zokumana nazo zawo ndi maganizo awo. Timalandira uphungu ndi malangizo ochokera kwa atsogoleri athu auzimu monga abusa ndi aphunzitsi, komanso akulu ampingo.
Chachitatu, kusonkhana kumatithandiza kulimbitsa ubale wathu ndi okhulupirira anzathu. Mpingo ndi gwero la chithandizo ndi chilimbikitso nthawi zovuta. Timapezanso anzathu komanso anthu otipempherera omwe amatithandiza kukula m’chikhulupiriro chathu.
Ndikofunikira kudziwa kuti kusonkhana kumabweretsa madalitso ambiri m'moyo wathu wauzimu ndi wamaganizo: Kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndi ubale wathu ndi Mulungu, kukula mwauzimu ndi kuphunzira, chithandizo ndi chilimbikitso nthawi zovuta, ubwenzi weniweni, mwayi wothandiza ena ndi kusintha dziko lathu, kumva kukhala m’banja la Mulungu ndi cholinga m’moyo.
Kumbukira kuti kusonkhana ndi gawo lofunika kwambiri pa dongosolo la Mulungu pa ife ndipo ndi komwe timakhalira m’cholinga chake chosatha ndikukhala moyo wathunthu, wolimba, komanso wodzipereka mwa Yesu.
osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.
Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.
Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.
Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.
Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu. Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi. Pakutinso thupi silikhala chiwalo chimodzi, koma zambiri.
Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu.
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Pakuti monga m'thupi limodzi tili nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo sizili nayo ntchito imodzimodzi; chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina.
Ndipo masiku onse, mu Kachisi ndi m'nyumba, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira Khristu Yesu.
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu; zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya; mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye; chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.
Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;
Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananene mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.
Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'chiweruziro chomwecho.
Pokhala Inu mpotikonda ndithu, Yehova wa makamu! Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa. Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro. Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu. Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.
Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.
komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;
Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;
Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima;
kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.
koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m'chikondano wina kwa mnzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu; kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m'chiyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ake onse.
Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.
Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.
Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika. Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo. Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.
Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.
ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.
Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike; ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.
kuti kusakhale chisiyano m'thupi; koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake. Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;
naonso ndidzanka nao kuphiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa paguwa langa la nsembe; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.
Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika. Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi; nyanja ibume mwa kudzala kwake. Munda ukondwerere ndi zonse zili m'mwemo; pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera. Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi. Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu; zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.
Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.
Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda woundana bwino: Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova. Pakuti pamenepo anaika mipando ya chiweruzo, mipando ya nyumba ya Davide.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Potero, abale anga okondedwa, olakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, okondedwa.
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu; akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.
Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.
Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu. Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.
Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu. Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti? Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga. Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo. Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.
Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandire monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.
Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.
chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye;
kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.
Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.
Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?
koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.
osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika. Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo,
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,
koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu, Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi? pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake; ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu; tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzatchedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.
ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;
Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga: ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo.
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu; kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.
Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.
Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake.
Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni, kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate. Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu. Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi, akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamange chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe. Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse; momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine. Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu. kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m'mau ndi m'chiphunzitso.
Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.
Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.
Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.
ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo, anthu amene anapereka moyo wao chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu.
Chotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu;
chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu;
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;
Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.
Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira. Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao, Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;