Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Timoteyo 4:13 - Buku Lopatulika

13 Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Mpaka pamene ndidzabwere, uchite khama kuŵerengera anthu mau a Mulungu, kuŵalalikira ndi kuŵaphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 4:13
20 Mawu Ofanana  

Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;


Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.


Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.


kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.


Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.


Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa.


Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m'vumbulutso, kapena m'chidziwitso, kapena m'chinenero, kapena m'chiphunzitso?


ndipo azikhala nacho, nawerengemo masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mau onse a chilamulo ichi ndi malemba awa, kuwachita;


Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.


Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa m'mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;


ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.


Izi lankhula, ndipo uchenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse.


Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa