Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala.
Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?
Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu.
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.
Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.
Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake, ndipo amithenga a Mulungu anakomana naye. sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri. Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkulu wanga, m'dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana. Ndipo Inu munati, Ndidzakuchitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbeu yako monga mchenga wa pa nyanja, umene sungathe kuwerengeka chifukwa cha unyinji wake. Ndipo anagona komweko usiku womwewo, natengako zimene anali nazo, mphatso yakupatsa Esau mkulu wake: mbuzi zazikazi mazana awiri, atonde makumi awiri, nkhosa zazikazi mazana awiri, ndi zazimuna makumi awiri, ngamira zamkaka makumi atatu ndi ana ao, ng'ombe zazikazi makumi anai, zazimuna khumi, abulu aakazi makumi awiri ndi ana khumi. Ndipo anazipereka zimenezo m'manja a anyamata ake, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyamata ake, Taolokani patsogolo panga, tachitani danga pakati pa magulu, lina ndi lina. Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? Za yani zimenezi patsogolo pako? Pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu. Ndipo anauzanso wachiwiri ndi wachitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau chotero, pamene mukomana naye: Pamene Yakobo anawaona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anatcha pamenepo dzina lake Mahanaimu.
Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga. Ndipo maunyolo anagwa kuchoka m'manja mwake.
Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo. Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa.
Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawatulutsa, nati,
Akhale monga mungu kumphepo, ndipo mngelo wa Yehova awapirikitse. Njira yao ikhale ya mdima ndi yoterera, ndipo mngelo wa Yehova awalondole.
Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye.
Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye. Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi. Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakukanika.
Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.
Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.
Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.
Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.
mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.
Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?
Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamchisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m'dziko. Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamchisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala chete, lipumula.
Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao;
Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m'malo opatulika.
Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira, nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.
Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa mu Ejipito; ndipo, taonani, tili mu Kadesi, ndiwo mzinda wa malekezero a malire anu.
Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya.
inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabriele, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.
Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna. Chifukwa chake udzisamalire, usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chinthu chilichonse chodetsa; pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m'dzanja la Afilisti. Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunse uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake;
Anaombola moyo wanga kunkhondo, ndikhale mumtendere, pakuti ndiwo ambiri okangana nane.
Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira kudzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira. Ndipo Zekariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira. Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete, kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria. Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe.
Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.
Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;
Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wachifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi; akunena ndi mau aakulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.
Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.
Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati padziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.
Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.
Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio. Ndipo Kornelio anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m'nyumba yanga pa ora lachisanu ndi chinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wovala chovala chonyezimira, nati Kornelio, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m'nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m'mbali mwa nyanja. Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani. Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho; koma m'mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye. Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse) mauwo muwadziwa inu, adadzawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane anaulalikira; za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye. Ndipo ife ndife mboni za zonse adazichita m'dziko la Ayuda ndi mu Yerusalemu; amenenso anamupha, nampachika pamtengo. Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.
Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, anadza kuchitseko chachitsulo chakuyang'ana kumzinda; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo anatuluka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamchokera. Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda.
Akakhala kwa iye mthenga, womasulira mau mmodzi mwa chikwi, kuonetsera munthu chomuyenera; pamenepo Mulungu amchitira chifundo, nati, Mlanditse, angatsikire kumanda, Ndampezera dipo.
M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.
Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano. Kuonekera kwake kunali ngati mphezi, ndi chovala chake choyeretsa ngati matalala;
Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.
Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu;
Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka; mwalamulira kundipulumutsa; popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikaele ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinapambane, ndipo sanapezekenso malo ao m'mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.
Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa panjira ya ku Suri.
Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye. Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi. Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakukanika. Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.
Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao. Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.
Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako. Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala. Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka. Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,
Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala mu Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.
Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo. Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.
Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako. Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Ndipo ndinaona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha ku chiphompho chakuya, ndi unyolo waukulu m'dzanja lake.
Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga.
Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wachifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi kumpando wachifumu, nalambira Mulungu,
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Koma ndidzakufotokozera cholembedwa pa lemba la choonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaele kalonga wanu.
Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera m'chilangali chamoto chotuluka m'kati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, chitsamba chilikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho.
Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi.
Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake. Koma anthu aja anatulutsa dzanja lao, namlowetsa Loti momwe anali iwo m'nyumba, natseka pakhomo. Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang'ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo. Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi, ndi onse ali nao m'mzinda muno, utuluke nao m'malo muno: popeza ife tidzaononga malo ano, chifukwa kulira kwao kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuononge. Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka. Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mzinda. Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mzinda. Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke. Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu; taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe; Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.
kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israele. Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji Iye amene anandituma ine? Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zake zichulukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu. Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israele; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israele. Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka choipachi; nati kwa mthenga wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi. Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati padziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.
Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.
Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso. Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako. Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa; awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.
pakuti kwalembedwa kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize. Ndipo, Pa manja ao adzakunyamula iwe, kuti ungagunde konse phazi lako pamwala.
ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake,
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru nacho, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atavala zonyezimira; Ndipo m'mene ananena ichi, anawaonetsera iwo manja ake ndi mapazi ake. Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno? Ndipo anampatsa Iye chidutsu cha nsomba yokazinga. Ndipo anachitenga, nachidya pamaso pao. Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo. Ndipo anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo; ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu; ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu. Inu ndinu mboni za izi. Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba. ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?
Munamchepsa pang'ono ndi angelo, mudamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu, ndipo mudamuika iye woyang'anira ntchito za manja anu;
Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m'misasa ya Aasiriya zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo.
Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu. Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao.
Ndipo anadza mngelo wina, naima paguwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse paguwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu. Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.
Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbike mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.
Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.
Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu.
Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe.
Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.
Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu. Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma. Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.
Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga. Nati kwa ine, Daniele, munthu wokondedwatu iwe, tazindikira mau ndilikunena ndi iwe, nukhale chilili; pakuti ndatumidwa kwa iwe tsopano. Ndipo pamene adanena mau awa kwa ine ndinaimirira ndi kunjenjemera.
Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu? Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza; m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.
Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mzinda. Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mzinda.
Koma tsopano ndikuchenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo. Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira, nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.
Sudzaopa choopsa cha usiku, kapena muvi wopita usana; kapena mliri woyenda mumdima, kapena chionongeko chakuthera usana.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera. Taonani, wakusunga Israele sadzaodzera kapena kugona.
Ndipo za angelo anenadi, Amene ayesa angelo ake mizimu, ndi omtumikira Iye akhale malawi amoto.
Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete,
Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku; sanachotse mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu.
Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa. Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi. Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.
Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira,
Sungani moyo wanga, ndilanditseni, ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu. Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge, pakuti ndayembekezera Inu.
Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda.
Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.
Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.
Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.
Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.
Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.
Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.
amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;
Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;
Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.
amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.
Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.
Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kuchira kwako kudzaonekera msangamsanga; ndipo chilungamo chako chidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wotchinjiriza pambuyo pako.
Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.
Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena kutenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asiriya ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe achuluka koposa okhala naye; pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anachirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;
Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.
Usaope zoopsa zodzidzimutsa, ngakhale zikadza zopasula oipa; pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, nadzasunga phazi lako lingakodwe.
Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.
Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.
ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.