Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 27:23 - Buku Lopatulika

23 Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Usiku womwe wathawu kunandibwerera mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake, ndipo amene ndimamlemekeza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Usiku wathawu mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake ndipo ndimamutumikira, anayima pafupi ndi ine,

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 27:23
41 Mawu Ofanana  

Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu; ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; mwandimasulira zondimanga.


Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo, Israele, akhale chuma chake chenicheni.


Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga, ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga; pakuti ine ndine mtumiki wanu.


Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;


Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wake: aweta zake pakati akakombo.


Ndine wake wa wokondedwa wanga, wokondedwa wanganso ndiye wa ine; aweta zake pakati pa akakombo.


Kumbukira zinthu izi, Yakobo; ndi Israele, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; ndakuumba, iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, sindidzakuiwala.


Wina adzati, Ine ndili wa Yehova; ndi wina adzadzitcha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lake, Ndine wa Yehova, ndi kudzitcha yekha ndi mfunda wa Israele.


Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;


ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;


Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa zikondwerero zake zoikika, momwemo mizinda yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.


Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo la ng'anjo yotentha yamoto, analankhula, nati, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, inu atumiki a Mulungu Wam'mwambamwamba, tulukani, idzani kuno. Pamenepo Sadrake, Mesake, ndi Abedenego, anatuluka m'kati mwa moto.


Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.


Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.


Ndipo poyandikira padzenje inafuula ndi mau achisoni mfumu, ninena, niti kwa Daniele, Daniele, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango?


Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira.


Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.


Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatse Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.


Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.


Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale chete;


Ndipo usiku wake Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.


Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawatulutsa, nati,


Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.


Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,


Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu,


Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.


Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.


Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake.


Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,


Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,


Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.


Paulo, kapolo wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo,


amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukuchitirani umboni za izi mu Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa