Genesis 48:16 - Buku Lopatulika16 mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati pa dziko lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Mngelo amene wandiwombola ku zoipa zonse, aŵadalitsenso! Podzera mwa anaŵa, dzina langa ndi maina a makolo anga Abrahamu ndi Isaki akhale omveka nthaŵi zonse! Adzakhale ndi ana ambiri iwoŵa, adzasanduke mtundu waukulu pa dziko lapansi!” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse, ameneyo adalitse anyamata awa. Kudzera mwa iwowa dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka. Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulu pa dziko lapansi.” Onani mutuwo |