Zekariya 12:8 - Buku Lopatulika8 Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala mu Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala m'Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Tsiku limenelo Chauta adzakhala ngati chishango chotchinjiriza anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti anthu ofooka kwambiri mwa iwo adzakhala amphamvu ngati mfumu Davide. Tsono banja la Davide lidzakhala lolamulira zonse ngati Mulungu, ngati mngelo wa Chauta woŵatsogolera. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Pa tsiku limenelo Yehova adzatchinjiriza onse okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anthu ofowoka kwambiri pakati pawo adzakhala ngati Davide, ndipo nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mngelo wa Yehova wowatsogolera. Onani mutuwo |