Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 14:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Choncho ine mdzakazi wanu ndidaaganiza kuti mau anu mbuyanga mfumu adzandipulumutsa, poti inu muli ngati mngelo wa Mulungu, podziŵa zabwino ndi zoipa. Chauta Mulungu wanu akhale nanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 “Ndipo tsopano mtumiki wanu akuti, ‘Lolani mawu a mbuye wanga mfumu abweretse mpumulo kwa ine, pakuti mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu pozindikira chabwino ndi choyipa. Yehova Mulungu wanu akhale nanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 14:17
13 Mawu Ofanana  

Pamenepo mfumu inayankha, ninena naye mkaziyo, Usandibisire kanthu ka zimene ndidzakufunsa iwe. Mkaziyo nati, Mbuye wanga mfumu anene.


Mnyamata wanu Yowabu anachita chinthu ichi kuti asandulize mamvekedwe a mlanduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse zili m'dziko lapansi.


Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu; chifukwa chake chitani chimene chikukomerani.


Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu?


Ndipo Aisraele onse anamva maweruzidwe ake idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.


Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?


Kodi pali chosalungama palilime panga? Ngati sindizindikire zopanda pake m'kamwa mwanga?


Siliva asungunuka m'mbiya, ndi golide m'ng'anjo, motero chomwe munthu achitama adziwika nacho.


Wosyasyalika mnzake atcherera mapazi ake ukonde.


Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.


Monga momwe tinamvera mau onse a Mose momwemo tidzamvera inu; komatu akhale ndi inu Yehova Mulungu wanu monga anakhala ndi Mose.


Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, Iye asamuke nafe kunkhondoko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa