Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 14:18 - Buku Lopatulika

18 Pamenepo mfumu inayankha, ninena naye mkaziyo, Usandibisire kanthu ka zimene ndidzakufunsa iwe. Mkaziyo nati, Mbuye wanga mfumu anene.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pamenepo mfumu inayankha, ninena naye mkaziyo, Usandibisire kanthu ka zimene ndidzakufunsa iwe. Mkaziyo nati, Mbuye wanga mfumu anene.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Apo mfumu idamuyankha mkaziyo kuti, “Musandibisire kanthu kalikonse pa zimene ndikufunseni.” Mkazi uja adati, “Ai ndithu, mbuyanga mfumu sindikubisirani.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Kenaka mfumu inati kwa mkaziyo, “Usandibisire chilichonse pondiyankha chimene ndidzakufunsa.” Mkaziyo anati, “Mbuye wanga mfumu yankhulani.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 14:18
5 Mawu Ofanana  

Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.


Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yowabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yowabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu.


Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, namtenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lachitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.


Koma akamva akulu kuti ndalankhula ndi iwe, nakafika kwa iwe, ndi kuti kwa iwe, Utifotokozere ife chomwe wanena kwa mfumu; osatibisira ichi, ndipo sitidzakupha iwe; ndiponso zomwe mfumu inanena kwa iwe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa