2 Samueli 14:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yowabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yowabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yowabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yowabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Tsono mfumuyo idafunsa kuti, “Kodi zimenezi Yowabu sakuzidziŵa?” Mkaziyo adayankha kuti, “Pali inu nomwe, mbuyanga mfumu, palibe munthu amene angathe kupewa kuyankha chilichonse chimene inu mwafunsa. Kunena zoona, mtumiki wanu Yowabu ndiye amene adandiwuza kuti ndichite zimenezi. Iyeyo ndiye adandiwuza ine mdzakazi wanu mau onseŵa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi zimenezi sukuchita motsogozedwa ndi Yowabu?” Mkaziyo anayankha kuti, “Pali inu wamoyo, mbuye wanga mfumu, palibe munthu angakhotere kumanja kapena kumanzere pa chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mwanena. Inde, ndi mtumiki wanu Yowabu amene wandilangiza ine kuchita zimenezi ndipo ndi amene anandipatsa mawu onsewa woti ine mtumiki wanu ndiyankhule. Onani mutuwo |