Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 27:5 - Buku Lopatulika

5 Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa m'tsenjezi mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pakuti pa tsiku la msautso Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo; adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 27:5
33 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anali nao wobisika m'nyumba ya Mulungu zaka zisanu ndi chimodzi; nakhala Ataliya mfumu yaikazi ya dziko.


Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?


Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.


Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.


Ndisungeni monga kamwana ka m'diso, ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,


Alinganiza mapazi anga ngati a mbawala, nandiimitsa pamsanje panga.


Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.


Wolemekezeka Yehova, pakuti anandichitira chifundo chake chodabwitsa m'mzinda walinga.


Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.


Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.


Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.


Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.


Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine.


Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa.


Apangana mochenjerera pa anthu anu, nakhalira upo pa obisika anu.


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.


Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.


Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.


Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.


Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa