Masalimo 68:17 - Buku Lopatulika17 Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m'malo opatulika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga m'Sinai, m'malo opatulika. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Ambuye adafika ku malo ao oyera kuchokera ku Sinai, ali ndi magaleta amphamvu zikwi zambirimbiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka, ndi miyandamiyanda; Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika. Onani mutuwo |
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,