Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 20:16 - Buku Lopatulika

16 Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa mu Ejipito; ndipo, taonani, tili mu Kadesi, ndiwo mzinda wa malekezero a malire anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa m'Ejipito; ndipo, taonani, tili m'Kadesi, ndiwo mudzi wa malekezero a malire anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Titalira kwa Chauta, adamva kulira kwathu, natuma mngelo amene adatitulutsa m'dziko la Ejipitolo. Tsopano tili kuno ku Kadesi, mzinda umene uli m'malire a dziko lanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 koma titalirira Yehova, Iyeyo anamva kulira kwathuko ndipo anatitumizira mngelo amene anatitulutsa ku Igupto.” “Taonani, tsopano tili pano pa Kadesi, mzinda wa mʼmalire a dziko lanu.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 20:16
14 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova.


Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao;


Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu.


ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapirikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;


Ndamvanso kubuula kwa ana a Israele, amene Aejipito awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa.


Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.


kuti makolo athu anatsikira kunka ku Ejipito, ndipo tinakhala mu Ejipito masiku ambiri; ndipo Aejipito anachitira zoipa ife, ndi makolo athu.


Ndipitire pakati padziko lako; sitidzapatuka kulowa m'munda, kapena m'munda wampesa, sitidzamwako madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu, kufikira tapitirira malire ako.


Nachokera ku Kadesi, nayenda namanga m'phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu.


Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?


Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, mu Ejipito;


Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa