Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 20:17 - Buku Lopatulika

17 Tipitetu pakati padziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Tipitetu pakati pa dziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Mutilole tsono tidzere m'dziko mwanu. Sitidzera m'minda mwanu kapena m'mipesa mwanu. Ndipo sitidzamwa madzi a m'zitsime zanu. Tidzangodzera mu mseu wanu waukuluwo basi, mpaka titadutsa dziko lanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Chonde mutilole tidutse mʼdziko lanu. Sitidzera mʼminda yanu kapena mu mpesa wanu, kapenanso kumwa madzi mʼchitsime chilichonse. Tidzayenda kutsata msewu waukulu wa mfumu ndipo sitidzapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere mpaka titadutsa malire a dziko lanu.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 20:17
7 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalole Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;


Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwera, anamva kuti Israele anadzera njira ya Atarimu, anathira nkhondo pa Israele, nagwira ena akhale ansinga.


Ndipitire m'dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere,


Undigulitse chakudya ndi ndalama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndalama, kuti ndimwe; chokhachi ndipitire choyenda pansi;


monga anandichitira ana a Esau akukhala mu Seiri, ndi Amowabu akukhala mu Ari; kufikira nditaoloka Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa