Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:41 - Buku Lopatulika

41 Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake kudzachotsa mu Ufumu wake anthu onse ochimwitsa anzao, ndi ena onse ochita zoipa,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:41
18 Mawu Ofanana  

Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya, pakuti siigwiridwa ndi dzanja;


Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.


Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,


Tsoka lili ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! Pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka lili ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye.


Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.


tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa