Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:42 - Buku Lopatulika

42 ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 nadzaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:42
19 Mawu Ofanana  

koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.


Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwake, ndipo moto udzawanyeketsa.


ndipo aliyense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.


nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.


Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.


Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mutulutsidwa kunja.


iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasakaniza m'chikho cha mkwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulufure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa;


Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:


Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Ndipo anatsegula pa chiphompho chakuya; ndipo unakwera utsi wotuluka m'chiphomphomo, ngati utsi wa ng'anjo yaikulu; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, chifukwa cha utsiwo wa kuchiphomphocho.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa